Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Enieni?
Yehova analenga anthu m’njira yoti azitha kucheza komanso kufuna kukhala ndi anzawo. (Miy. 17:17; 18:1; 18:1, 24) Komabe kuti zinthu zizitiyendera bwino, tiyenera kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo. (Miy. 13:20) Pambuyo powerenga nkhani ya mutu wakuti, Kodi Ndipeze Anzanga Ena Abwino?, yochokera mu Galamukani! ya March 2009, tsamba 18 mpaka 20, yankhani mafunso otsatirawa?
Mawu Oyamba:
(1) Kodi mnzanu weniweni ayenera kukhala wotani?
Zimene Zingakuthandizeni Kuti Mupeze Anzanu:
(2) Tikamasankha anzathu, kodi tiyenera kuganizira mfundo zitatu ziti? (3) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati tikamaganizira mfundo zitatu zimene tatchulazi? (4) Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi anzathu ambiri?—2 Akor. 6:13.
Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu:
(5) Kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti zimenezi zitheke? (Sal. 34:8) (6) Ngati titakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kodi tingapezenso anzathu otani?
Anzanu Amene Si Amakhalidwe Abwino:
(7) Kodi ndi anthu a makhalidwe otani amene simuyenera kucheza nawo? (1 Akor. 15:33) (8) Kodi kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa kungawononge bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?
(9) Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani ya m’Baibulo yonena za Dina? (Gen. 34:1, 2, 7, 19)
Kufunsa:
(10) Funsani achinyamata awiri achitsanzo chabwino mafunso otsatirawa: (a) Kodi amakumana ndi mavuto otani kusukulu pa nkhani yokhudza anthu ocheza nawo? (b) Kodi zinthu monga kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu paokha, kupezeka pamisonkhano yachikhristu mokhazikika zimawathandiza bwanji kulimbana ndi mavuto amenewa?
(c) Kodi kugwira nawo ntchito yolalikira kumawathandiza bwanji kupeza anzawo mu mpingo?
Mawu Omaliza:
(11) Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhaniyi? (12) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji nkhani yopezeka mu Galamukani! ya March 2009 pothandiza anthu ena?
Choncho, tiyeni tizisankha bwino anzathu amene angatithandize kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, amene ndi bwenzi lathu labwino kuposa munthu aliyense.—Sal. 15:1, 4; Yes. 41:8.