MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mfundo Zothandiza Kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki Uzikhala Wabwino
Mofanana ndi mmene zilili ndi misonkhano ina yonse yampingo, misonkhano yokonzekera utumiki ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo imatipatsa mwayi woti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. (Ahe 10:24, 25) Misonkhanoyi iyenera kuchitika kwa maminitsi 5 mpaka 7, ndipo nthawi imeneyi ikamatha, anthu ayenera kukhala atauzidwa kale oyenda naye, gawo lomwe akalalikire komanso pemphero laperekedwa. (Ngati msonkhanowu ukuchitika pambuyo pa msonkhano wina wa mpingo, uyenera kukhala waufupi kuposa pamenepa.) Wochititsa msonkhanowu ayenera kukonzekera bwino zinthu zomwe zingathandize amene akulowa mu utumiki patsikulo. Mwachitsanzo ngati ndi Loweruka, pamene anthu ambiri omwe abwera pamsonkhanowo ndi oti sanalowe mu utumiki kwa mlungu wonse, zingakhale zothandiza kungokambirana zomwe munganene polalikira. Kodi ndi nkhani zina ziti zimene mungakambirane pamsonkhanowu?
Chitsanzo cha zimene tinganene chopezeka mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
Mmene tingagwiritsire ntchito zochitika za posachedwapa poyamba kukambirana ndi anthu
Mmene tingayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo
Mmene tingayankhire munthu wokana Mulungu, wokhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha, wolankhula chinenero china kapena wa m’chipembedzo chimene si chofala m’dera lanu
Mmene tingagwiritsire ntchito webusaiti ya jw.org, JW Library® kapena Baibulo
Mmene tingagwiritsire ntchito chimodzi mwa zinthu zopezeka pa Zinthu Zophunzitsira
Mmene tingachitire mtundu winawake wa ulaliki monga kulalikira patelefoni, kulemba makalata, kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri, kuchita maulendo obwereza kapena kuchititsa maphunziro a Baibulo
Kukumbutsana zofunikira pa nkhani ya kukhala otetezeka, kusintha mogwirizana ndi zomwe zikuchitika, kukhala ndi makhalidwe abwino, kuona zinthu moyenera, kapena mfundo zina zotero
Kukambirana phunziro kapena vidiyo ya m’kabuku ka Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Mmene mungalimbikitsire kapena kuthandizira mnzanu amene mwayenda naye mu utumiki
Lemba logwirizana ndi utumiki kapena chitsanzo cholimbikitsa cha zimene zinachitikira ena mu utumiki