Ndandanda ya Mlungu wa March 30
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 30
Nyimbo Na. 58 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 10 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 106 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 14-15 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 14:36-45 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Mapemphero Amene Mulungu Amayankha—bt tsa. 78-79 ndime 6-9 (Mph. 5)
Na. 3: Ulosi Wokhudza Masiku Otsiriza Ukukwaniritsidwa—igw tsa. 13 ndime 1 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Khalani Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Mph. 15: Mavidiyo Enanso Opezeka pa Webusaiti Yathu Omwe Tingagwiritse Ntchito mu Utumiki. Nkhani yokambirana. Ikani vidiyo yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? Kambiranani kuti tingagwiritsire ntchito bwanji vidiyoyi mu utumiki. Kenako, chitaninso chimodzimodzi ndi vidiyo yakuti, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? Pomaliza, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingachitire zimenezi. Ngati simungathe kuonetsa mavidiyowa, gwiritsani ntchito timapepala tomwe tinatuluka pamsonkhano wachigawo wa 2013 komanso 2014.
Mph. 15: “Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? Poyamba Kukambirana Ndi Anthu.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti atchule njira zina zomwe tingagwiritsire ntchito kabukuka mu utumiki. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritse ntchito kabukuka mu utumiki.
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero