Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani?—Poyamba Kukambirana ndi Anthu
1. Kodi tinalandira kabuku kati, komwe kangatithandize mu utumiki?
1 Pa msonkhano wachigawo wachaka chatha, tinalandira kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? Kodi tingakagwiritse ntchito bwanji poyamba kukambirana ndi anthu mu utumiki? Kabukuka kali ndi mitu yofotokoza nkhani za m’Baibulo ndi malemba pansi pa mituyo mofanana ndi buku la Kukambitsirana. Choncho, kangatithandize kwambiri poyamba kukambirana ndi anthu.
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani?
2 Pogwiritsa ntchito mutu 8, munganene kuti: “Tikucheza ndi anthu mwachidule kuti tidziwe maganizo awo pa funso ili, ‘Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti anthu azivutika?’ [M’madera ena zimakhala bwino kumuonetsa munthu funsoli.] Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Baibulo lili ndi yankho la funso limeneli.” Werengani lemba limodzi kapena angapo kuchokera m’Baibulo n’kukambirana. Ngati munthuyo akuoneka kuti akufuna kudziwa zambiri, musonyezeni mitu 20 ya m’kabukuka. Kenako m’pempheni kuti asankhe umodzi kuti mudzakambirane ulendo wotsatira. Kapenanso mungamupatse buku kapena kabuku kamene timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu komwe kali ndi nkhani imene mwakambirana.
3. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? tikamalalikira m’dera lomwe anthu ambiri si Akhristu?
3 Mitu 4 komanso 13 mpaka 17 ndi yothandiza kwambiri ngati tikulalikira m’dera lomwe anthu ambiri si Akhristu. Mwachitsanzo pogwiritsa ntchito mutu 17, munganene kuti: “Tikucheza ndi anthu mwachidule n’kumakambirana nawo mfundo zothandiza mabanja. Kodi nanunso mumaona kuti mabanja masiku ano akukumana ndi mavuto ambiri? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri okwatirana amaona kuti mawu awa ndi othandiza kwambiri: ‘Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.’ [Simukufunikira kumuuza kuti mawuwa achokera palemba la Aefeso 5:33. Ngati mukulankhula ndi mzimayi, mukhoza kumuuza mawu a pa Aefeso 5:28.] Kodi mukuganiza kuti malangizo amenewa angathandize kuti banja likhale losangalala?”
4. Kodi mungatani ngati mwakambirana kwakanthawi ndi munthu yemwe si wachipembedzo chachikhristu?
4 Pomaliza mufunseni funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira. Mwina mungadzakambirane malemba ena omwe ali m’mutu womwe mwakambirana. Mukakambirana naye kwakanthawi ndipo munthuyo akapitiriza kusonyeza chidwi, mungamuuze kuti mfundo zimene mumakambiranazo n’zochokera m’Baibulo. Potengera zimene mwakhala mukukambirana naye kapena ngati munthuyo wayamba kukhulupirira Baibulo, mungamupatse buku kapena kabuku komwe mukuona kuti angakakonde.—Onani nkhani yakuti, “Kodi Tingawanthandize Bwanji?” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December 2013.