Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/03 tsamba 1
  • Kufunafuna Anthu Oyenerera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Anthu Oyenerera
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwayesa Kuchitira Umboni Kwamadzulo?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Mmene Tingalalikirire M’gawo la Malonda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Perekani Chisamaliro Chokhazikika ku Chiphunzitso Chanu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 12/03 tsamba 1

Kufunafuna Anthu Oyenerera

1 Sikophweka kutsatira malangizo a Yesu ogwirira ntchito yolalikira. Iye anati: “M’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukaloŵamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo.” (Mat. 10:11) Poti anthu ambiri sakumakhalakhala panyumba masiku ano, kodi tingatani kuti ntchito yofunafuna anthu oyenererayi iyende bwino?

2 Pendani Gawo Lanu: Pendani gawo lanu choyamba. Ndi nthaŵi iti yomwe nthaŵi zambiri anthu amakhala panyumba? Kodi masana mungawapeze kuti? Kodi pali tsiku linalake pamlungu kapena nthaŵi inayake patsiku pamene angasangalale kwambiri kuchezeredwa? Mungapindule kwambiri mwa kuloŵa m’gawo mogwirizana ndi zochita za anthu a m’gawolo komanso mmene iwo alili.—1 Akor. 9:23, 26.

3 Ofalitsa ambiri amapeza anthu panyumba zawo pamene dzuŵa litapendeka. Nthaŵi imeneyi eninyumba ena amakhala omasuka kwambiri ndiponso ndi nthaŵi yoti angamvetsere bwino kwambiri. Kulalikira m’malo amalonda ndiponso m’malo omwe mumapezeka anthu ambiri ndizo njira zinanso zofalitsira uthenga wabwino kwa anthu.

4 M’mwezi wina wa ntchito yapadera, mpingo wina unakonza zolalikira dzuŵa litapendeka patsiku Loŵeruka ndi Lamlungu ndiponso kulalikira kutada masiku aŵiri a mkati mwa mlungu. Anakonzanso zolalikira kudzera patelefoni ndiponso kukalalikira m’malo amalonda. Dongosolo limeneli linathandiza kuti anthu akhale achangu mu utumiki moti mpingowo unakonza zopitiriza kuchita zimenezi.

5 Yesetsani Kubwererako: Ngati m’gawo lanu n’zovuta kupeza anthu panyumba mukapita paulendo wobwereza, yesetsani kuti nthaŵi zonse pomaliza kucheza ndi munthu, kuphatikizaponso paulendo woyamba, muzipangana bwinobwino nthaŵi yoti mudzam’pitirenso. Ndiyeno, onetsetsani kuti mwachita zomwe mwapanganazo. (Mat. 5:37) Ngati m’poyenera, mungam’funse mwininyumbayo adiresi kapena nambala yake ya telefoni. Izi zingakuthandizeninso kuti mudzalankhule nayenso.

6 Mosakayikira Yehova adzadalitsa khama lathu lofunafuna anthu oyenerera ndi kuwapitiranso kukakulitsa chidwi chawo.—Miy. 21:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena