Ndandanda ya Mlungu wa June 27
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 27
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 9 ndime 1-9 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 52–59 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. “Kodi Ndiziwerengera Bwanji Nthawi Ndikakhala mu Utumiki?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Mukamaliza kukamba nkhaniyi, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka lolambirira m’mwezi wa July, pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki patsamba 4. Limbikitsani onse kuti ayesetse kuyambitsa maphunziro.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa July. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, tchulani nkhani zina zimene zili m’magaziniwo. Kenako sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu, ndipo funsani omvera kuti anene mafunso ndi malemba amene tingagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira magazini iliyonse.
Mph. 15: Khalani Osamala Polalikira. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 197 mpaka 199. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuyankha mosasamala zimene anthu otsutsa amakonda kutinena kwanuko. Kenako chitani chitsanzo china chosonyeza wofalitsa akuyankha nkhani yomweyo mosamala.
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero