“Kodi Ndiziwerengera Bwanji Nthawi Ndikakhala mu Utumiki?”
Kodi munadzifunsapo funso limeneli? Mungapeze malangizo a mmene mungawerengere nthawi m’buku la Gulu, patsamba 86 mpaka 87. Komanso nthawi zina timapatsidwa malangizo pa nkhaniyi, monga amene ali m’Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2008. Chifukwa chakuti zinthu zimasiyanasiyana, sitinapatsidwe malamulo ambirimbiri pa nkhaniyi. Choncho si bwino kuti akulu kapena anthu ena aike malamulo ena owonjezera.
Ngati tili ndi funso linalake ndipo palibe malangizo amene gulu linalemba oyankha funsolo, wofalitsa aliyense azidzifunsa kuti: Kodi nthawiyi ndaigwiritsa ntchito mu utumiki, kapena pa zinthu zina zosakhudzana ndi utumiki? Zimene timalemba palipoti lathu lautumiki wakumunda mwezi uliwonse zizitipatsa chimwemwe, osati kuvutitsa chikumbumtima chathu. (Mac. 23:1) Cholinga chathu chachikulu sikungopeza maola ayi, koma kugwiritsa ntchito nthawi yathu moyenera pochita khama tikakhala mu utumiki.—Aheb. 6:11.