Bokosi la Mafunso
◼ Kodi makolo onse awiri azilemba lipoti la nthawi imene amachititsa phunziro la banja?
Ngakhale kuti abambo ndi amene ali ndi udindo waukulu wolerera ana awo “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake,” makolo onse awiri amathandizana kuphunzitsa ana awo. (Aef. 6:4) Baibulo limalangiza ana kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” (Miy. 1:8) Njira imodzi yofunika kwambiri imene makolo angaphunzitsire ana awo ndiyo phunziro la Baibulo la banja.
M’mbuyomu, kholo limodzi lokha limene linkachita phunziro la banja ndi ana osabatizidwa ndi limene linkalemba lipoti, ngakhale kuti makolo onse awiri ankatenga nawo mbali paphunzirolo. Koma tsopano zimenezi zasintha. Ngati paphunziro la banja makolo onse awiri akuthandizana, aliyense angawerengere nthawi yosapitirira ola limodzi mlungu uliwonse ngati ntchito yakumunda. N’zoona kuti makolo amathera nthawi yoposa ola limodzi pamlungu akuphunzitsa ana awo. Ndiponso, makolo onse awiri amachita khama kuti aphunzitse ana awo. (Deut. 6:6-9) Komabe, cholinga chachikulu cha malipoti a mwezi ndi mwezi ndi kusonyeza zimene zikuchitika m’munda. Choncho, makolo asamalembe nthawi yopitirira ola limodzi pamlungu, ngakhale phunzirolo litapitirira ola limodzi, litachitika kangapo pamlungu, kapena ngati mwana aliyense amaphunzira naye payekha. Koma kholo limodzi lokha ndi limene liyenera kulemba lipoti la phunziro la Baibulo la banja ndi kulembanso ulendo wobwereza umodzi mlungu uliwonse umene achita phunzirolo.