Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/03 tsamba 3
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 11/03 tsamba 3

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi phunziro la Baibulo la banja liyenera kuchitiridwa lipoti ku mpingo?

Ngati kholo lachikristu limachititsa phunziro la Baibulo la banja ndipo pamakhalanso ana osabatizidwa, khololo lingachitire lipoti ola limodzi lokha pamlungu, ulendo wobwereza umodzi pamlungu, ndiponso phunziro la Baibulo lapanyumba limodzi pamwezi. Izi zimakhalanso choncho ngakhale phunzirolo litachitika kwa maola angapo, maulendo angapo pamlungu, kapena kuchita ndi mwana aliyense payekha.—Onani buku la Utumiki Wathu, tsa. 104, ndime 2.

Ngati onse m’nyumbamo ali Mboni zobatizidwa, ndiye kuti nthaŵi yochititsira phunzirolo ndiponso phunzirolo sitichitira lipoti monga utumiki wa kumunda (pokhapokha ngati mwanayo akuphunzirabe buku lachiŵiri atabatizidwa). Izi zili choncho chifukwa chakuti lipoti la utumiki wa kumunda la mpingo kwenikweni limasonyeza zimene timachita polalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa choonadi cha Baibulo anthu amene si atumiki a Yehova odzipatulira ndi obatizidwa. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Komabe, izi sizikusonyeza kuti si kofunika kuchititsa phunziro limeneli nthaŵi zonse.

Ndi udindo wa makolo achikristu kuphunzira ndi ana awo. Amene akufuna kuwathandiza kukhazikitsa phunziro la banja kapena kusintha mmene amachitira phunziro lawolo kuti likhale labwino angapemphe akulu kuti awathandize. Ngati chifukwa cha mmene zinthu zilili pakufunika kuti wofalitsa wina azichita phunziro la Baibulo ndi mwana wosabatizidwa amene makolo ake ndi Akristu mu mpingowo, onanani kaye ndi woyang’anira wotsogolera kapena woyang’anira utumiki. Ngati avomereza kuti ayambe kuphunzira naye, wochititsayo angachitire lipoti phunzirolo monga angachitire ndi phunziro la Baibulo lina lililonse.

Kuphunzitsa ana m’njira ya Yehova kumafuna nthaŵi yambiri ndiponso khama kuposa zimene zimalembedwa pa lipoti la utumiki wa kumunda. (Deut. 6:6-9; Miy. 22:6) Makolo achikristu afunika kuwayamikira posamalira maudindo awo aakulu kuti alere ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aef. 6:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena