Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja
1 Mphatso yaikulu imene inu monga kholo lachikristu mungapatse ana anu ndiyo kukonda kwanu Yehova. Nthawi yabwino imene mungachitire zimenezi ndi “pokhala pansi m’nyumba zanu” pamene mukuchita phunziro la Baibulo la banja mlungu uliwonse. (Deut. 6:5-7) Kaya makolo nonse awirinu ndinu Mboni, kaya ndinu osiyana zikhulupiriro, kapena ndinu kholo limene likulera lokha ana, mukhoza kuthandiza ana anu kukukondani ndi kukonda Yehova mwa kuchita phunziro la banja nthawi zonse.
2 Mmene Mungayambire Kuphunzira: Chinthu choyambirira chomwe mungachite ndicho kukhala ndi chizolowezi chophunzirira limodzi monga banja. Ngati mukukayikira za nthawi yabwino imene mungamachite phunzirolo, bwanji osayesa kukambirana za nkhaniyi monga banja. (Miy. 15:22) Ngati muli ndi ana aang’ono, mungasankhe kumaphunzira nawo kwa nthawi yochepa koma kwa mlungu wonse. Konzani ndandanda yomwe ingakhale bwino mogwirizana ndi zochita za banja lanu. Pa ndandanda yanuyo, lembani nthawi yeniyeni yochitira phunziro lanu la banja ndipo onetsetsani kuti mukuitsatira.
3 Kodi mungamaphunzire chiyani? Ena amakonzekera zimene akaphunzire pa Phunziro la Buku la Mpingo kapena pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ena amaphunzira nkhani zomwe anazikonzera makamaka achinyamata. Bambo wina yemwe ali ndi ana awiri, wamwamuna ndi wamkazi, anati: “Chimene chimapangitsa ana kukonda phunziro lathu mlungu uliwonse n’chakuti timachita masewero a nkhani zochokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Chofunika kwambiri ndi zimene anawa amaphunzira ndi kuzimvetsa osati kuchuluka kwa ndime zimene timaphunzira.”
4 Muziphunzira Mlungu Uliwonse: Phunziro la banja lizichitika nthawi zonse ndipo aliyense m’banjamo ayenera kumaliyembekezera mwachidwi. N’zotheka kusintha tsiku ndi nthawi chifukwa cha zina zogwa mwadzidzidzi zofunika kuzisamalira. Nthawi zina pangafunikenso kusintha nkhani imene mudzaphunzire. Koma kusintha kulikonse kumene kungakhalepo sikufunika kusokonezeratu ndandanda yonse ya banja yoti inakhazikitsidwa kale. M’banja lina, mwana wina wamkazi anati: “Ngati nthawi yochitira phunziro yasintha, bambo amalemba kapepala kosonyeza nthawi yatsopanoyo n’kukaika pa malo oonekera bwino kuti tonse tithe kudziwa nthawi imene tidzachita phunzirolo.” Zoterezi n’zoyamikirika kwambiri chifukwa zimathandiza kuti phunzirolo lizichitika nthawi zonse. Mukamapitiriza kulera ana anu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,” mumasonyeza chikondi chanu ponse pawiri, kwa ana anu ndiponso kwa Atate wathu wakumwamba.—Aef. 6:4.