Mmene Banja Limachitira Zinthu Kuti Onse Azitengamo Mbali Mokwanira—Pa Phunziro la Baibulo
1 Choonadi chimawonjezera tanthauzo ndi chifuno chenicheni cha moyo wabanja, koma kutumikira Yehova bwino lomwe sikungochitika mwadzidzidzi. Pamafunika nthaŵi ndi kuyesetsa kuti mukhale ndi banja lolimba mwauzimu. Ndi kofunika kwambiri kuti banja lonse lizigwirizana poyesa kuchita zimenezi. Mbali yoyamba ino ya nkhani yomwe ndi yambali zitatu, ilongosola mmene mabanja angachitire zinthu pamodzi kuti akhale ndi zizoloŵezi zabwino za kuphunzira.
2 mwa Kuŵerenga Baibulo Tsiku Lililonse: Miyambo 24:5 imanena kuti “munthu wodziŵa ankabe nalimba.” Chidziŵitso chimene munthu amachipeza poŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse chimamupatsa nyonga ya m’kati imene amafunika kuti alimbane ndi Satana pamene aukira mkhalidwe wake wauzimu. (Sal. 1:1, 2) Kodi mumaŵerenga Baibulo pamodzi monga banja tsiku lililonse? Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ili ndi “Ndandanda ya Kuŵerenga Baibulo Yowonjezera” ya mlungu uliwonse kwa chaka chonse. Banja limangofunika nthaŵi yochepa chabe tsiku lililonse, mwina mphindi ngati khumi, kuti lizitsatira ndandandayi. Sankhani nthaŵi yoyenera, monga ngati panthaŵi ya chakudya cha mmaŵa, pambuyo pa chakudya cha madzulo, kapena musanakagone, kuti muŵerenge Baibulo ndi kukambirana lemba latsiku mu kabuku ka Kusanthula Malemba. Pangani zimenezi kukhala mbali ya zochita za tsiku ndi tsiku za banja lanu.
3 mwa Kuphunzirira Pamodzi Mlungu Uliwonse: Phunziro la Baibulo la banja liyenera kukhala chochitika chachikulu cha banja pa mlunguwo. Aliyense wa m’banjamo ayenera kulichirikiza mwa kutengamo mbali mofunitsitsa m’phunzirolo. Mutu wa banja afunika kulingalira zosoŵa za banjalo posankha nkhani zophunziridwa ndiponso tsiku, nthaŵi, ndi utali wa phunzirolo. Ikani phunziro la banja pamalo oyamba m’zochitika za mlunguwo. Musalole zinthu zina zosafunika kwambiri kuti zisokoneze.—Afil. 1:10, 11.
4 Bambo wina amene kaŵirikaŵiri anali kulandira mafoni a zantchito kunyumba kwake anali kudula telefoni panthaŵi ya phunziro la banja. Ngati makasitomala anafika kunyumbako, anali kuwaitana kuti akhale nawo paphunzirolo kapena kudikira mpaka atamaliza kuphunzirako. Bamboyo anali kutsimikiza kuti palibe chilichonse chimene chikasokoneza phunziro la banjalo. Ana ake anachita chidwi kwambiri ndi zimenezi, ndipo nawonso malonda ake anamuyendera bwino.
5 Zimakhaladi zosangalatsa pamene banja lichitira pamodzi zinthu zauzimu! Kukhala wokhulupirika pa zoyesayesa zathu za kuchitira pamodzi phunziro la Baibulo la banja kudzabweretsa madalitso a Yehova.—Sal. 1:3.