Mitu ya Mabanja—Khalanibe ndi Ndandanda Yabwino Yochitira Zinthu Zauzimu
1 Danieli ankadziŵika kuti anali kutumikira Yehova ‘mosalekeza,’ ngakhale kuti anakhala zaka zambiri ndi anthu opembedza mafano ndiponso a makhalidwe oipa a ku Baibulo. (Dan. 6:16, 20) Kodi anakwanitsa bwanji kukhalabe wolimba mwauzimu? Nkhani ya m’Baibulo imasonyeza kuti anali ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu zokhudza kulambira koona. Mwachitsanzo, anali ndi ndandanda yopemphera katatu patsiku m’chipinda chake cha patsindwi. (Dan. 6:10) Mosakayikira, analinso ndi ndandanda yochitira zinthu zina zauzimu monga kuŵerenga Chilamulo. Choncho, Danieli atakumana ndi chiyeso choika moyo pangozi, sanasunthike pa kudzipereka kwake kwa Yehova, ndipo anapulumutsidwa modabwitsa.—Dan. 6:4-22.
2 Chimodzimodzinso masiku ano, tiyenera kulimbikira “kukhala maso nthaŵi zonse.” (Aef. 6:18, NW) M’dziko limene tikukhala lino ‘likugona mwa woipayo.’ (1 Yoh. 5:19) Chitsutso kapena ziyeso zingabwere mwadzidzidzi ndipo zingayese chikhulupiriro chathu. Panthaŵi ya chisautso chachikulu, Gogi wa ku Magogi adzaukira kotheratu atumiki a Mulungu ndipo iwo adzaoneka ngati alibe populumukira. Adzafunika kukhulupirira kwambiri Yehova.—Ezek. 38:14-16.
3 Mawu oyamba a seŵero la pa msonkhano wachigawo wa 1998 lakuti “Mabanja—Pangani Kuŵerenga Baibulo kwa Tsiku ndi Tsiku Kukhala Chizoloŵezi Chanu!” ananena kuti: “Njira imodzi yofunika ndi yakuti banja likhale ndi chizoloŵezi choŵerenga Baibulo, kuliphunzira, ndi kukambirana mogwira mtima.” Mawuwo anapitiriza kuti: ‘Pamene mabanja atsatira pulogalamu yotereyi nthaŵi zonse ndiponso mwa njira imene imapangitsa mawu a m’Baibulo kukhala ogwira mtima, chizoloŵezi chozikidwa pa Baibulo chimenechi chingabweretse zodabwitsa pabanja. Chimawonjezera chidziŵitso chathu. Chimalimbikitsa chikhulupiriro chathu. Ndipo chimatipatsa zitsanzo zoti tizitsatira—amuna ndi akazi anthaŵi zakale okhulupirikadi—zimene zingatilimbikitse, kutisonkhezera kugwiritsitsa choonadi.’ Pamene tikuona mbali zosiyanasiyana za ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu, mitu ya mabanja iyenera kuona njira imodzi kapena ziŵiri zowongolerera pulogalamu yauzimu m’banja lawo.
4 Kambiranani Mawu a Mulungu Tsiku ndi Tsiku: Mawu a m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2001 pa ndemanga za lemba la pa September 11, anati: “Pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulira popanda kutsutsidwa ndipo chifuno chake chitachitidwa padziko lapansi monga kumwamba, sikudzakhalanso anthu olusa ayi, ngakhale nyama zolusa sizidzakhalako ‘sizidzaipitsa kapena kusakaza.’ (Yes. 11:9; Mat. 6:9, 10)” Mawu ameneŵa anali olimbikitsa kwambiri. Monga mutu wa banja, kodi tsiku lililonse mumakambirana lemba la m’Baibulo ndi ndemanga yake ndi banja lanu? Izi n’zothandiza kwambiri. Ngati simungathe kupangira pamodzi m’mawa, mwina mungachite nthaŵi ina tsikulo. Bambo wina anati: “Nthaŵi ya chakudya chamadzulo ndi yabwino kwa ife kukambirana lemba la m’Baibulo.”
5 Ngati muli nayo kale ndandanda yabwino yokambirana lemba la tsiku monga banja, mukuchita bwino kwambiri. Mwina mungapindule kwambiri mwa kuŵerenga mbali ina ya Baibulo panthaŵi yomweyo. Ena ali ndi chizoloŵezi choŵerenga chaputala chonse pamene pachokera lemba la tsikulo. Ena amaŵerenga motsatizana, kuŵerenga pang’onopang’ono buku la m’Baibulo limene asankha. Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kudzathandiza banja lanu kuopa kukhumudwitsa Yehova ndiponso kudzawachititsa kufunitsitsa kuchita chifuno chake.—Deut. 17:18-20.
6 Ndandanda ya banja lanu yoŵerenga Baibulo ndi kukambirana lemba la tsiku idzakhala yopindulitsa kwambiri ngati mukhala ndi nthaŵi pang’ono yokambirana phindu la zimene mukuphunzirazo. Buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 60, pali malingaliro aŵa: “Mungasankhe mavesi ochepa pandandanda yanu ya kuŵerenga Baibulo ya mlunguwo. Kambiranani matanthauzo ake, kenako funsani mafunso ngati aŵa: ‘Kodi lembali limatithandiza motani? Kodi mavesiŵa tingawagwiritse ntchito motani mu ulaliki? Kodi amasonyezanji za Yehova ndi njira yake yochitira zinthu? Ndipo amakulitsa motani chiyamikiro chathu kwa iye?’” Kukambirana zinthu zauzimu kumeneku kudzathandiza a m’banja lanu onse ‘kudziŵa chifuniro cha Ambuye n’chiyani.’—Aef. 5:17.
7 Phunziro la Banja: Kuchititsa phunziro la banja mokhazikika mlungu uliwonse ndi njira yabwino imene mitu ya mabanja ingasonyezere ana awo kuti zinthu zauzimu ziyenera kukhala patsogolo. Mnyamata wina anati: “Nthaŵi zina Atate pochokera ku ntchito ankakhala otopa moti ankavutika kukhala maso, komabe phunziro silimalephereka, ndipo izi zinatithandiza kuona kufunika kwa phunzirolo.” Ananso angathandize kuti phunzirolo liziyenda bwino. Nthaŵi zonse banja lina la ana nayini linkadzuka 5 koloko kuti lichite phunziro la banja chifukwa kuchita nthaŵi ina kunali kovuta.
8 Kuti phunziro la banja likhale logwira mtima, mutu wa banja uyenera ‘kudzipenyerera ndi chiphunzitsocho.’ (1 Tim. 4:16) Buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 32 limati: “Tinganene kuti phunziro la banja logwira mtima limayamba ndi kuliphunzira banja lanu lenilenilo. Kodi a m’banja lanu akupita patsogolo motani mwauzimu? . . . Pamene muli muulaliki limodzi ndi ana anu, kodi amachita manyazi poonekera kwa anzawo kuti ndi Mboni za Yehova? Kodi amasangalala ndi pulogalamu yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo monga banja? Kodi akutengadi njira ya Yehova kukhala njira ya moyo wawo? Popenda mosamala mudzazindikira zimene muyenera kuchita monga mutu wa banja, kuti mukhazikitse ndi kukulitsa makhalidwe auzimu mwa aliyense wa m’banja lanu.”
9 Misonkhano ya Mpingo: Kukonzekera ndi kupezeka pa misonkhano ya mpingo kuyenera kukhala mbali yofunika kwambiri pa ndandanda yanu ya mlungu uliwonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthaŵi zina, zingatheke kukonzekera misonkhano ina monga banja. M’malo modikira mpaka nthaŵi ithe, kodi mungakonzekere kutatsala nthaŵi yaitali? Ndandanda yabwino pankhani imeneyi idzathandiza kuti kukonzekera kwanu kukhale kwabwino kwambiri ndiponso kuti mupindule kwambiri ndi misonkhano.—Miy. 21:5.
10 Kukonzekera bwino ndiponso kuchita zimenezo nthaŵi zonse n’zofunika kwambiri pa ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu. Bwanji ngati mikhalidwe yanu sikulolani kukonzekera misonkhano yonse? Buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 31, lili ndi malingaliro aŵa: “Pewani chizolowezi choipa chongoŵerenga nkhanizo kungoti muzimalize, kapenanso osaziphunzira n’komwe ati chifukwa simungazimalize. M’malo mwake, onani kuti mungaphunzire kufika pati, ndipo phunzirani zomwezo bwino lomwe. Teroni mlungu ndi mlungu. M’kupita kwa nthaŵi, yesetsani kulowetsapo misonkhano inanso.”
11 Mabanja akafika mofulumira pamisonkhano, zimawathandiza kukhazikika maganizo kuti atamande Yehova ndi kupindula ndi malangizo amene alandire. Kodi banja lanu limakonda kuchita zimenezi? Zimenezi zimafuna kukonzekera bwino ndiponso kugwirizana kwa onse m’banjamo. Ngati nthaŵi zambiri mumaona kuti banja lanu limachita zinthu mothamanga ndiponso limapanikizika masiku a misonkhano, kodi mungasinthe zimene mumachita? Kodi pali zinthu zimene mungachitiretu? Ngati wina m’banjamo ali ndi ntchito yambiri, kodi ena angamuthandize? Kodi zingachepetse kupanikizika ngati aliyense wakonzeka kupita ku misonkhano nthaŵi yabwino? Kukonzekera bwino kumathandiza kulimbikitsa mtendere wa m’banja ndi mu mpingo momwe.—1 Akor. 14:33, 40.
12 Utumiki wa Kumunda: Kukhazikitsa nthaŵi yeniyeni yochita utumiki ndi mbali ina ya ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu. Mnyamata wina dzina lake Jayson akuti: “M’banja mwathu, Loŵeruka lililonse m’mawa tinali kupita muutumiki wa kumunda. Zimenezi zinandithandiza chifukwa kupitapita mu utumiki kunandichititsa kuona phindu lake ndiponso kukonda kwambiri utumiki.” Anthu ambiri okulira m’mabanja a Mboni angavomereze kuti kukhala ndi nthaŵi yeniyeni yochita utumiki mlungu uliwonse kunawathandiza kupita patsogolo monga atumiki achikristu.
13 Ndandanda yabwino ingathandizenso kuti nthaŵi imene banja lanu limakhala mu utumiki wakumunda izikhala yosangalatsa komanso yopindulitsa kwambiri. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, patsamba 21 inanena malingaliro aŵa: “Kodi inu nthaŵi ndi nthaŵi mumagwiritsa ntchito nthaŵi ya phunziro lanu labanja kuthandiza anthu a m’banja lanu kukonzekera utumiki wakumunda wa mlunguwo? Kuchita zimenezi kungakhale kopindulitsa kwambiri. (2 Timoteo 2:15) Zingathandize kuti utumiki wawo ukhale watanthauzo ndi waphindu. Nthaŵi zina, mungapatule nthaŵi yonse ya phunziro kuti mukonzekere zimenezi. Kaŵirikaŵiri, mungamakambirane mbali zina za utumiki wakumunda kwa kanthaŵi kochepa mukamaliza phunziro labanja kapena nthaŵi ina mkati mwa mlunguwo.” Kodi banja lanu layesa zimenezi?
14 Pitirizani Kupita Patsogolo: Pazimene takambiranazi, kodi mwaona mbali zimene a m’banja lanu akuchita bwino? Ayamikireni ndipo limbikirani kuwongolera mbali zimenezi. Ngati mukuona kuti pali mbali zambiri zofunika kuwongolera, sankhani mbali imodzi kapena ziŵiri kaye zoti mugwirirepo ntchito. Zikakhazikika pandandanda yanu yochitira zinthu zauzimu, gwirirani ntchito pambali ina imodzi kapena ziŵiri. Khalani ndi maganizo abwino ndipo musachite zonse nthaŵi imodzi, chitani mofatsa. (Afil. 4:4, 5) Kukhala ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu m’banja lanu kumafuna khama, koma mpake, chifukwa Yehova akutitsimikizira kuti: “Iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.”—Sal. 50:23.