Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 8/1 tsamba 26-29
  • Phunziro la Banja Losangalatsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunziro la Banja Losangalatsa
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tiyenera Kuphunziranji?
  • Pangitsani Nthaŵiyo Kukhala Yabata
  • Pangitsani Baibulo Kukhala Losangalatsa
  • Thandizani Aliyense Kulankhulapo
  • Lankhulanani​—Musawakwiyitse!
  • Khama Limapindula
  • Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Chitanipo Kanthu Kuti Banja Lanu Likaloŵe m’Dziko Latsopano la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 8/1 tsamba 26-29

Phunziro la Banja Losangalatsa

“KUDZIŴA kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika chamtengo wake,” limatero Baibulo. (Miyambo 24:4) Chuma chamtengo wake chimenechi sikuti ndi chuma chakuthupi chabe komanso chimaphatikizapo chikondi choona, mantha aumulungu, ndiponso chikhulupiriro cholimba. Mikhalidwe yoteroyo ndithudi imapangitsa banja kukhala lachimwemwe. (Miyambo 15:16, 17; 1 Petro 1:7) Komabe, kuti tiipeze, pafunikira kuti tipangitse nyumba yathu kudziŵa Mulungu.

MUTU wa banja ali ndi udindo wophunzitsa za Mulungu ena onse m’banjamo. (Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 5:25, 26; 6:4) Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zochitira zimenezi ndiyo kuchititsa phunziro la banja nthaŵi zonse. Zingakhale zosangalatsa chotani kwa amene amakhalapo paphunzirolo ngati lichitidwa mwakuti atolepo nzeru komanso mokondweretsa! Tiyeni tsopano tipende momwe tingachititsire phunziro la banja logwira mtima.a

Phunziro la banja limakhala lothandiza kwambiri ngati limachitika nthaŵi zonse. Koma ngati limachitika mwamwaŵi kapena modzidzimutsira, nzokayikitsa kuti lingakhale laphindu. Motero muyenera ‘kuwombola nthaŵi’ yoti muzichita phunziro. (Aefeso 5:15-17 NW) Kusankha nthaŵi yoyenera kwa onse m’banjamo kungakhale kovuta. “Timalephera kuti tizichita phunziro la banja nthaŵi zonse,” mutu wa banja wina anavomera motero. “Tinayesa nthaŵi zosiyanasiyana kufikira potsirizira pake tinapeza nthaŵi yoyenerana ndi ife cha madzulo kutayamba kamdima. Tsopano timachita phunziro lathu la banja nthaŵi zonse.”

Mutaipeza nthaŵi yoyenera, khalani maso kuti musalole zinthu zina kusokoneza phunzirolo. “Alendo akabwera tili pa phunziro,” akukumbukira choncho Maria,b yemwe tsopano ali ndi zaka 33, “Atate amawapempha kuti ayembekeze kufikira titatha. Koma itakhala telefoni, amangomuuza munthuyo kuti amuyankha nthaŵi ina.”

Komabe, izi sizikutanthauza kuti tiyenera kukhala osasinthika. Pakhoza kukhala zinthu zina zofunika msangamsanga kapena zochitika za mwadzidzidzi, ndipo kungakhale koyenerera kuchotsapo phunziro nthaŵi zina kapena kudzalichita tsiku lina. (Mlaliki 9:11) Koma khalani maso kusalola kuti zimenezi zisokoneze ndandanda yanu.​—Afilipi 3:16.

Kodi phunziro liyenera kutenga nthaŵi yaitali motani? Robert, yemwe walera bwino ana ake, wamkazi ndi wamwamuna, akuti: “Kaŵirikaŵiri maphunziro athu amatenga ola limodzi. Pamene anawa anali ang’onoang’ono, timayesetsa kuwapanga kukhalabe osangalatsidwa ola lonselo mwa kukambitsirana zinthu zosiyanasiyana, monga ndime zochepa za phunziro la Nsanja ya Olonda, kusankha ndime pang’ono m’Baibulo, ndiponso ndime zina za m’mabuku ena.” Maria akukumbukira kuti: “Pamene ineyo ndi akulu anga aŵiri tinali aang’ono kwambiri, phunziro lathu limatenga mphindi 20 kaŵiri kapena katatu pamlungu. Pamene tinasinkhukirapo, phunziro lathu la banja la mlungu ndi mlungu limatenga ola lathunthu kapena kuposerapo.”

Kodi Tiyenera Kuphunziranji?

Kufunsa zimenezi pamene onse asonkhana kale kudikirira phunziro kukhoza kuwapangitsa kugwa mphwayi ndiponso kuwononga nthaŵi ya phunziro pachabe. Zikakhala motero, ana sakhala ndi chidwi choti adzaphunzirapo zakutizakuti ndipo posatenga nthaŵi amagwa ulesi. Choncho sankhani pasadakhale chofalitsa cha Sosaite chimene mudzaphunzira.

“Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wafalitsa mabuku ambiri amene mungasankhepo. (Mateyu 24:45-47) Mwina mukhoza kugwiritsira ntchito buku limene banjalo silinaphunzirepo. Ndiponso nkosangalatsa chotani nanga kusankha ndime zina zokambitsirana mu Insight on the Scriptures ngati mabuku ameneŵa alipo m’chilankhulo chanu! Mwachitsanzo, mukhoza kuŵerenga nkhani ya Mgonero wa Ambuye milungu yoyandikira tsiku la chikumbutso. Mabanja ambiri amakonda kukonzekereratu Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo. Komabe, nkhani zinazo za mu Nsanja ya Olonda nazonso ndi zabwino kuphunzira. Mutu wa banja, amene amadziŵa zosoŵa zauzimu za banjalo, ndiye akhoza kusankha bwino buku loti nkuphunzira.

“Nthaŵi zonse timaphunzira buku lomwe linali litasankhidwa pasadakhale kumbuyoko,” akukumbukira motero Maria. “Koma patabuka funso mwina kena kake kachitika kusukulu, pamenepo timasintha ndi kuphunzira zokhudza vutolo.” Pali zinthu zina zomwe zimabuka, monga mavuto amene achinyamata amapeza kusukulu, zibwenzi, zochitika zina za kusukulu, ndi zina zotero. Pakachitika zotere, sinthirani ku nkhani kapena mabuku amene amanena za vuto lilipolo. Ngati mwaona nkhani mu magazini atsopano a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! imene mukufuna kuti muphunzire ndi banja lanu nthaŵi yomweyo, musakayike kuchita zimenezo. Komabe, mufunikira kuliuziratu banjalo za kusinthako pasadakhale. Pamene mwasamala vutolo, tsimikizirani kuti mwabwereranso ku ndandanda yanu yoikidwayo.

Pangitsani Nthaŵiyo Kukhala Yabata

Kuphunzira kumachitika bwino pamene pali mtendere. (Yakobo 3:18) Choncho pangitsani nthaŵiyo kukhala yakumasuka, komanso onse nkukhala aulemu. Mutu wabanja wina ku United States anati: “Kaya tikuphunzirira m’nyumba kaya ndi pakhonde, timayesa kukhala pafupipafupi chapamodzi m’malo mokhala chotalikirana m’chipinda chachikulu. Kwa ife, kukhala choncho kumatipangitsa kumva kukhala okondana.” Ndipo Maria akukumbukira ndi chimwemwe chachikulu kuti: “Ineyo ndi abale anga timaloledwa kusankha malo m’nyumbamo pamene tingakonde kuti tidzachitire phunziro mlungu umenewo. Izi zimatipangitsa kukhala omasuka.” Kumbukirani kuti kuwala kwabwino, kakhalidwe kabwino, ndiponso chimwemwe ndi malo aukhondo, zonsezi zimawonjezera bata panthaŵiyo. Kukhala ndi zosangulutsa litatha phunziro la banjalo kumathandizanso kupangitsa banja kuona madzulowo kukhala osangalatsa.

Mabanja ena amaitanira ngakhale mabanja ena pa phunziro lawo nthaŵi zina, akumapangitsa phunzirolo kukhala losangalatsirapo ndiponso kuti pakhale ndemanga zosiyanasiyana. Pamene achatsopano m’choonadi aitanidwa kudzakhala nawo pa phunziro lotere, akhoza kupindula mwakuonerera mutu wa banja wachidziŵitso akuchititsa phunziro la banja.

Pangitsani Baibulo Kukhala Losangalatsa

Pangitsani nthaŵi ya phunziro kukhala yosangalatsa kwa ana, ndiye adzayamba kumaliyembekezera mwachidwi. Mukhoza kuchita zimenezi mwakulimbikitsa ana kujambula zithunzithunzi za zochitika za m’Baibulo. Ngati nkoyenera, uzani ana kuyeserera zochitika za m’Baibulo ndi kupanga maseŵero. Mukakhala ndi ana aango’no sikofunikira kuumirira pa kachitidwe kakekake kaja ka mafunso ndi mayankho. Kuŵerenga kapena kumangosimba nkhani za m’Baibulo ndi njira ina yosangalatsa yophunzitsira ana malamulo a Mulungu. Robert, wotchulidwa poyamba uja, akukumbukira kuti: “Nthaŵi zina timapatsidwa kuŵerenga ndime za m’Baibulo, timasinthanasinthana, kuŵerenga ‘mawu a anthu’ osiyanasiyana.” Ana angaloledwe kusankha munthu amene akufuna kuŵerenga mawu ake.

Kugwiritsira ntchito mapu ndi matchati kukhoza kuthandiza ana okulirapo kuyerekeza malo ndi zinthu za kumalo kumene kunachitikira zimene mukuphunzirazo. Nzoonekeratu kuti kungophatikizapo zoyerekezera pang’ono, phunziro la banja likhoza kukhala losangalatsa ndiponso logwira mtima. Ndipo ana akhoza kuyamba kulakalaka Mawu a Mulungu.​—1 Petro 2:2, 3.

Thandizani Aliyense Kulankhulapo

Kuti ana asangalale ndi phunziro, nawonso ayenera kuona kuti akutengamo mbali. Komabe, kupangitsa ana amisinkhu yosiyana kulankhulapo nkovuta. Koma pulinsipulo la Baibulo limati: “Iye wakuweruza, aweruze ndi changu.” (Aroma 12:8) Kukhala wansangala nkothandiza, chifukwa kumapangitsa enawonso kusangalala.

Ronald amapangitsa mwana wake wazaka zisanu, Dina, kulankhulapo, mwakumpempha kuŵerenga mitu yaing’ono m’nkhani yophunziridwayo ndiponso kumpempha kuperekapo ndemanga pa zithunzithunzi. Pamene Chikumbutso cha imfa ya Kristu chimayandikira chaka chatha, analimbikira kuonetsa zithunzi zokhudza Chikumbutso m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.c Iye akuti: “Izi zinampangitsa kumvetsetsa tanthauzo la Chikumbutsocho.”

Koma ndi Misha, mwana wake wamkazi wazaka khumi, Ronald amachita zoposerapo. “Misha wafika poti sikuti amangozindikira zinthunzi chabe, komanso zimene zikutanthauza,” akutero Ronald. “Motero pamene timaphunzira buku la Revelation​—Its Grand Climax At Hand!d tinakambapo kwambiri pa tanthauzo la zithunzi, ndipo zimenezi zamthandiza.”

Pamene ana akula kufika pa unyamata, alimbikitseni kuti azigwiritsira ntchito zomwe akuphunzira. Pakabuka mafunso mkati mwaphunziro, agaŵireni mbali zoti akafufuze. Robert anachita zimenezo pamene mwana wake wazaka 12, Paul, anamfunsa ponena za kalabu yatsopano kusukulu yomwe imachitanso maseŵera otchedwa Dungeons ndi Dragons ophatikizapo machitidwe achisembwere ndi chiwawa. Paul ndi ena m’banjamo anafufuza nkhani imeneyi pogwiritsa ntchito Watchtower Publications Index, ndipo anakambitsirana pa phunziro lawo la banja. “Zotsatira zake,” akutero Robert, “mwamsanga Paul anamvetsa kuti maseŵerawo ndi oipa kwa Mkristu.”

Robert amawagaŵira nkhani zoti afufuze nthaŵi zina. Mkazi wake, Nancy, akukumbukira kuti: “Pamene tinkafufuza za atumwi a Yesu, aliyense amagaŵiridwa kufufuza mtumwi mmodzi pamlungu. Zinali zokondweretsa kuona ana akunena mwachidwi pa phunziro la banja zimene anapeza!” Kufufuza paokha ndi kukambirana ndi ena m’banjamo zomwe apezazo kumathandiza ana kuti ‘akule pamaso pa Yehova.’​—1 Samueli 2:20, 21.“Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

Kufunsa mafunso​—openda ndiponso otsogolera ku yankho​—ndi njiranso yabwino yopangitsira ana kulankhulapo. Mphunzitsi Wamkulu, Yesu, amafunsa mafunso openda momwe munthu wamvera, monga akuti, “Uganiza bwanji?” (Mateyu 17:25) “Pamene aliyense wa ife anali ndi funso, makolo athu samayankha mwachindunji,” akukumbukira motero Maria. “Nthaŵi zonse amafunsa mafunso otsogolera ku yankho, kutithandiza kuganiza pa nkhaniyo.”

Lankhulanani​—Musawakwiyitse!

Paphunziro la banja chisangalalo chimakula ngati onse akulankhula za malingaliro awo momasuka osaopa kuti asekedwa. Koma “kulankhulana kwabwino paphunziro la banja kumatheka pokhapokha ngati pamakhalanso kulankhulana kwabwino nthaŵi zina,” akutero tate wina. “Simungathe kungokuchita nthaŵi ya phunziro chabe.” Mwanjira iliyonse, pewani ndemanga zoŵaŵitsa mtima, monga kuti, ‘Tere nzimene umati unene basi? Ndimayesa unena za nzeru; ‘Nzopusa zimenezo’; ‘Munganenenji inu? Ndiwe mwana umadziŵanji.’ (Miyambo 12:18) Khalani achifundo ndi omvera chisoni ana anu. (Salmo 103:13; Malaki 3:17) Sangalala nawoni, ndipo athandizeni pamene akuyesayesa kugwiritsira ntchito zimene akuphunzira m’miyoyo yawo.

Paphunziro payenera kukhala mzimu wakuti ana akuyembekezera kutengapo malangizo. “Ngati uyamba kuwakalipira,” likutero kholo lina lomwe linalera bwino ana ake anayi, “umakhala ndi omvetsera omwe akulundira.” Zikatero, mwina zomwe muphunzirezo sizingaloŵe mwa iwo. Choncho pewani kupanga nthaŵi yaphunziro kukhala yokalipira ndi kulanga ana. Ngati nzofunika, zichiteni nthaŵi ina ndipo aliyense payekha.

Khama Limapindula

Kumanga banja lolemera mwauzimu kumalira nthaŵi ndiponso khama. Koma wamasalmo akunena kuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphotho yake.” (Salmo 127:3) Ndipo makolo anapatsidwa udindo wa ‘kuwalera [ana] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’ (Aefeso 6:4) Motero kulitsani luso la kuchititsa phunziro la banja losangalatsa ndiponso lothandiza. Yesetsani kuti mupereke “mkaka woyenera, wopanda chinyengo,” kuti ana anu ‘akule kufikira chipulumutso.’​—1 Petro 2:2; Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

a Ngakhale kuti mfundo zambiri m’nkhani ino ndi zokhudza mmene tingaphunzitsire ana paphunziro la banja, malingaliro ake amagwiranso ntchito m’banja limene mulibe ana.

b Maina ena asinthidwa.

c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

d Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena