Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 8 tsamba 71-86
  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • OFALITSA ATSOPANO
  • ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AKHALE WOFALITSA
  • KUTHANDIZA ANA
  • KUDZIPEREKA NDIPONSO KUBATIZIDWA
  • LIPOTI LA MMENE UTUMIKI UKUYENDERA
  • LIPOTI LANU LA UTUMIKI WAKUMUNDA
  • LIPOTI LA MPINGO LOLEMBAPO NTCHITO ZA WOFALITSA
  • UBWINO WOPEREKA MALIPOTI
  • MUZIKHALA NDI ZOLINGA
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhosa za Yehova Zimafuna Kuzisamalira Mokoma Mtima
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Perekani Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 8 tsamba 71-86

MUTU 8

Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino

YEHOVA anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri choti tizitsatira. Chitsanzo chimenechi ndi Mwana wake Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Aliyense akakhala wotsatira wa Yesu, amakhala mtumiki wa Mulungu ndipo amayamba kulalikira uthenga wabwino. Posonyeza kuti kukhala wotsatira wa Yesu n’kolimbikitsa mwauzimu, iye anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Lonjezo limeneli limakwaniritsidwa kwa aliyense amene amavomera kukhala wotsatira wake.

2 Yesu, yemwe ndi Mtumiki Wamkulu wa Mulungu, anaitana anthu enaake kuti akhale otsatira ake. (Mat. 9:9; Yoh. 1:43) Anawaphunzitsa mmene angachitire utumiki n’kuwatumiza kuti akagwire ntchito yolalikira yomwe nayenso ankagwira. (Mat. 10:1–11:1; 20:28; Luka 4:43) Kenako, anatumizanso ophunzira ena 70 kuti akalengeze uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Luka 10:1, 8-11) Potumiza ophunzira amenewa Yesu anawauza kuti: “Amene akukumverani, akumveranso ine. Ndipo amene akunyalanyaza inu akunyalanyazanso ine. Ndipotu amene akunyalanyaza ine akunyalanyazanso amene anandituma.” (Luka 10:16) Polankhula mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti ophunzira akewo apatsidwa udindo waukulu. Iwo ankaimira Yesu ndiponso Mulungu Wam’mwambamwamba. Ndi mmenenso zilili masiku ano ndi anthu amene akumvera kuitana kwa Yesu kwakuti: “Ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Luka 18:22; 2 Akor. 2:17) Onse amene amavomera kuitana kumeneku, Mulungu amawapatsa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiponso kuphunzitsa anthu.​—Mat. 24:14; 28:19, 20.

3 Chifukwa chomvera kuitana kwa Yesu koti tikhale otsatira ake, takhala ndi mwayi ‘wophunzira ndi kudziwa’ za Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. (Yoh. 17:3) Taphunzitsidwa njira za Yehova ndipo iye watithandiza kusintha maganizo athu, kuvala umunthu watsopano ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. (Aroma 12:1, 2; Aef. 4:22-24; Akol. 3:9, 10) Pofuna kusonyeza kuyamikira kwathu, tinadzipereka kwa Yehova ndipo tinasonyeza zimenezi pamene tinabatizidwa. Munthu akabatizidwa m’pamene amaikidwa kukhala mtumiki wa Mulungu.

4 Nthawi zonse tiyenera kukumbukira kuti aliyense amene akufuna kutumikira Mulungu ayenera kukhala wopanda mlandu komanso woyera. (Sal. 24:3, 4; Yes. 52:11; 2 Akor. 6:14–7:1) Tili ndi chikumbumtima choyera chifukwa choti timakhulupirira Khristu. (Aheb. 10:19-23, 35, 36; Chiv. 7:9, 10, 14) Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti zochita zawo zonse zizilemekeza Mulungu n’cholinga choti asakhumudwitse ena. Nayenso mtumwi Petulo anasonyeza kuti khalidwe labwino lingachititse anthu ena kuti aphunzire choonadi. (1 Akor. 10:31, 33; 1 Pet. 3:1) Koma kodi mungathandize bwanji munthu kuti nayenso akhale mtumiki wolalikira uthenga wabwino?

OFALITSA ATSOPANO

5 Mukangoyamba kuphunzira Baibulo ndi munthu wachidwi, muzimulimbikitsa kuti aziuza anthu ena zimene akuphunzira. Angamauze achibale ake, anzake, ogwira nawo ntchito komanso anthu ena ndipo angachite zimenezi pamene akucheza nawo. Kuchita zimenezi ndi kofunika kwambiri pophunzitsa atsopano kuti azilalikira uthenga wabwino potsatira chitsanzo cha Yesu Khristu. (Mat. 9:9; Luka 6:40) Wophunzirayo akayamba kudziwa zambiri komanso akazolowera kufotokozera anzake zimene akuphunzira, angauze amene akuphunzira nayeyo kuti akufuna kuti azilalikira limodzi ndi mpingo.

ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AKHALE WOFALITSA

6 Musanauze munthu amene mukuphunzira naye Baibulo kuti angayambe kumalalikira kunyumba ndi nyumba, muyenera kuonetsetsa kuti akukwanitsa zonse zofunikira. Munthu akalowa nafe mu utumiki anthu amamuona kuti ndi wa Mboni za Yehova. Choncho ayenera kukhala kuti anasintha khalidwe lake kuti lizigwirizana ndi mfundo zolungama za Yehova moti akhoza kukhala wofalitsa wosabatizidwa.

7 Popeza mwakhala mukuphunzira komanso kukambirana mfundo za m’Baibulo ndi munthuyo, ndiye kuti mukumudziwa bwino kwambiri. N’kutheka kuti mwaona kuti wasintha khalidwe lake kuti lizigwirizana ndi zimene akuphunzira. Komabe palinso zinthu zina zokhudza munthuyo zimene akulu angakonde kukambirana nanu limodzi ndi munthuyo.

8 Wogwirizanitsa ntchito za akulu adzakonza zoti akulu awiri (mmodzi wa m’komiti ya utumiki) akambirane nanu limodzi ndi wophunzira Baibuloyo. M’mipingo imene muli akulu ochepa, mkulu mmodzi angachite zimenezi limodzi ndi mtumiki wothandiza woyenerera. Abale amene asankhidwa ayenera kugwira ntchitoyi mwamsanga. Ngati akulu auzidwa tsiku la misonkhano zoti munthu wina akufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa, zikhoza kutheka kukambirana ndi anthuwo tsiku lomwelo pambuyo pa misonkhano. Akulu ayenera kuyesetsa kuti aliyense akhale womasuka pa nthawi yokambiranayo. Wophunzirayo asanavomerezedwe kukhala wofalitsa wosabatizidwa, akulu ayenera kutsimikizira zinthu izi:

  1. (1) Amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu.​—2 Tim. 3:16.

  2. (2) Amadziwa ndi kukhulupirira ziphunzitso zoyambirira za m’Malemba ndipo ngati atafunsidwa angayankhe mogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa osati zimene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa kapena za m’maganizo mwake.​—Mat. 7:21-23; 2 Tim. 2:15.

  3. (3) Amamvera lamulo la m’Baibulo lakuti anthu a Yehova azisonkhana pamodzi ngati angathe kutero.​—Sal. 122:1; Aheb. 10:24, 25.

  4. (4) Amadziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya dama, chigololo, mitala, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndipo akuyesetsa kupewa makhalidwe amenewa. Ngati munthuyo akukhala ndi mwamuna kapena mkazi amene si m’bale wake, anthuwo ayenera kukwatirana motsatira malamulo.​—Mat. 19:9; 1 Akor. 6:9, 10; 1 Tim. 3:2, 12; Aheb. 13:4.

  5. (5) Amamvera lamulo la m’Baibulo loletsa kuledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala alionse osokoneza bongo.​—2 Akor. 7:1; Aef. 5:18; 1 Pet. 4:3, 4.

  6. (6) Amazindikira kufunika kopewa kugwirizana ndi anthu oipa.​—1 Akor. 15:33.

  7. (7) Anafufutitsa dzina lake monga membala wachipembedzo chonyenga kapena bungwe lililonse lachipembedzo ndipo anasiya kupita kumisonkhano yawo kapena kuchita nawo zinthu zina.​—2 Akor. 6:14-18; Chiv. 18:4.

  8. (8) Salowerera nawo nkhani zandale.​—Yoh. 6:15; 15:19; Yak. 1:27.

  9. (9) Amakhulupirira ndipo amayesetsa kutsatira zimene zili pa Yesaya 2:4 zokhudza kusalowerera m’mikangano ya mayiko.

  10. (10) Akufunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova.​—Sal. 110:3.

9 Ngati akulu sanatsimikizire za mmene wophunzirayo akuonera mfundo ina, angakambirane naye pogwiritsa ntchito malemba amene asonyezedwawo n’kumufunsa mmene akuonera mfundoyo. M’pofunika kuti azindikire kuti munthu amene amalalikira limodzi ndi Mboni za Yehova ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Malemba amanena. Zimene munthuyo anganene zingathandize akulu kudziwa ngati munthuyo akuzindikira kuti akufunika kumachita zotani monga wofalitsa komanso ngati akuoneka kuti akhoza kuyamba kumalalikira limodzi ndi mpingo.

10 Akulu ayenera kumuuza wophunzirayo mwamsanga ngati akuyenerera kapena ayi. Nthawi zambiri zimakhala zotheka kumuuza zimenezi zokambiranazo zikangotha. Ngati wayenerera, akuluwo angamuuze kuti amulandira monga wofalitsa. (Aroma 15:7) Amulimbikitse kuti asachedwe kuyamba kulalikira ndiponso kuti adzapereke lipoti lake kumapeto kwa mwezi. Akuluwo angamufotokozere kuti wophunzira Baibulo akayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa n’kupereka lipoti lake loyamba, amupangira Lipoti la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa, n’kuliika mu faelo ya mpingo. Akulu amasunga zinthu zokhudza iyeyo zimene zimalembedwa pa lipotili n’cholinga choti gulu lithe kupitiriza kusamalira Mboni za Yehova padziko lonse komanso kuti iyeyo azitha kutenga nawo mbali pa zinthu zokhudza mpingo ndiponso azithandizidwa mwauzimu. Kuwonjezera pamenepa akulu angakumbutse wofalitsa watsopanoyo kuti zinthu zokhudza iyeyo zimene amasungazi amazigwiritsa ntchito mogwirizana ndi Mfundo za Mboni za Yehova Zapadziko Lonse Zokhudza Kusunga Chinsinsi, zomwe zimapezeka pa jw.org.

11 Tingamulimbikitse kwambiri wofalitsa watsopano ngati titamayesetsa kudziwana naye komanso ngati timasonyeza kuti tili ndi chidwi ndi zimene akuchita. Zimenezi zingamuthandize kuti azipereka malipoti ake mwezi uliwonse komanso azichita khama kwambiri potumikira Yehova.​—Afil. 2:4; Aheb. 13:2.

12 Akulu akaona kuti wophunzira Baibulo akuyenera kuyamba kulowa mu utumiki, angamupatse buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Akapereka lipoti lake loyamba la utumiki wakumunda, chilengezo chachidule chiyenera kuperekedwa kumpingo chonena kuti iye ndi wofalitsa wosabatizidwa.

KUTHANDIZA ANA

13 Nawonso ana angayenerere kukhala ofalitsa uthenga wabwino. Yesu anacheza ndi ana aang’ono ndiponso kuwadalitsa. (Mat. 19:13-15; 21:15, 16) Ngakhale kuti ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana awo, anthu enanso mumpingo angathandize ana amene akufuna kugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu. Ngati ndinu kholo, mukamasonyeza chitsanzo chabwino mu utumiki, mudzalimbikitsanso ana anu kuti azilimbikira polalikira. Ndiye kodi pali njira zinanso ziti zimene tingathandizire mwana amene ndi wachitsanzo chabwino ndipo akufuna kuti azifotokozera ena chikhulupiriro chake?

14 Makolo ayenera kuonana ndi mkulu mmodzi wa m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo n’kukambirana naye kuti aone ngati mwanayo ali woyenerera kukhala wofalitsa. Wogwirizanitsa ntchito za akulu adzakonza zoti akulu awiri (mmodzi wa m’komiti ya utumiki) akumane ndi mwanayo limodzi ndi kholo kapena makolo ake onse, ngati onse ali okhulupirira, kapenanso limodzi ndi munthu aliyense amene amamusamalira. Ngati mwanayo akudziwa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo komanso akusonyeza kuti akufunitsitsa kuti azilalikira, umenewu ungakhale umboni wakuti akupita patsogolo. Pambuyo pokambirana zimenezi komanso mfundo zina zofanana ndi zimene zimakhudza anthu akuluakulu, akuluwo angaone ngati mwanayo ali woyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa. (Luka 6:45; Aroma 10:10) Pamene akukambirana ndi mwana, akulu safunika kukambirana naye nkhani zimene sizikumukhudza zomwe nthawi zambiri zimakhudza anthu akuluakulu.

15 Pamene akukambirana, akuluwo ayenera kumuyamikira mwanayo chifukwa cha kupita kwake patsogolo ndiponso ayenera kumulimbikitsa kuti akhale ndi cholinga chodzabatizidwa m’tsogolo. Angayamikirenso makolo chifukwa chochita khama pophunzitsa mwana wawoyo choonadi. Ndipo kuti awathandize kupitiriza kuthandiza mwanayo, angawalimbikitse kuti awerenge “Mawu kwa Makolo Achikhristu” omwe ali patsamba 179-181.

KUDZIPEREKA NDIPONSO KUBATIZIDWA

16 Ngati mwadziwa Yehova komanso kuyamba kumukonda, moti mwasintha moyo wanu n’kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kugwira nawo ntchito yolalikira, mukufunika kuyesetsa kulimbitsa ubwenziwo. Koma kodi mungaulimbitse bwanji? Muyenera kudzipereka ndiponso kubatizidwa. Kubatizidwa ndi umboni wosonyeza kuti munthu anadzipereka kwa Mulungu.​—Mat. 28:19, 20.

17 Kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza kumulonjeza Yehova m’pemphero lochokera pansi pa mtima kuti mudzamutumikira komanso kutsatira malamulo ake kwa moyo wanu wonse. Zimasonyeza kuti kwa moyo wanu wonse simudzatumikira mulungu wina aliyense koma Yehova yekha. (Deut. 5:9) Munthu amadzipereka ali payekha ndipo munthu wina sangamuchitire zimenezi.

18 Koma palinso zinthu zina zimene muyenera kuchita kuwonjezera pa kungomuuza Yehova kumbali kuti mukufuna kukhala mtumiki wake. Muyenera kuwasonyeza anthu ena kuti munadzipereka kwa Mulungu. Mungachite zimenezi pobatizidwa m’madzi, ngati mmene Yesu anachitira. (1 Pet. 2:21; 3:21) Ngati mwatsimikiza kuti mukufuna kutumikira Yehova ndiponso kubatizidwa, kodi muyenera kutani? Muyenera kufotokoza maganizo anuwo kwa wogwirizanitsa ntchito za akulu. Iye adzakonza zoti akulu angapo akambirane nanu kuti aone ngati mukuyesetsa kutsatira zimene Mulungu amafuna. Kuti mudziwe zambiri, werengani ““Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizidwa,” omwe ali patsamba 182-184 komanso “Mafunso kwa Anthu Amene Akufuna Kubatizidwa,” omwe ali patsamba 185-207.

LIPOTI LA MMENE UTUMIKI UKUYENDERA

19 Kwa zaka zambiri, malipoti osonyeza mmene kulambira koona kukupitira patsogolo, akhala akulimbikitsa kwambiri anthu a Yehova. Kungoyambira pamene Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi, Akhristu oona akhala akuyembekezera mwachidwi kuona mmene zimenezi zidzakwaniritsidwire.​—Mat. 28:19, 20; Maliko 13:10; Mac. 1:8.

20 Otsatira a Yesu oyambirira ankasangalala kumvetsera malipoti osonyeza kuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino. (Maliko 6:30) Buku la Machitidwe limafotokoza kuti panali anthu 120 pa nthawi imene mzimu woyera unkatsanuliridwa pa ophunzira pa Pentekosite mu 33 C.E. Pasanapite nthawi chiwerengerochi chinawonjezereka kufika pafupifupi 3,000 ndipo kenako chinafika pafupifupi 5,000. Pa nthawiyi panaperekedwa lipoti lakuti “Yehova anapitiriza kuwawonjezera anthu amene anali kuwapulumutsa” komanso kuti “ansembe ambirimbiri anakhala okhulupirira.” (Mac. 1:15; 2:5-11, 41, 47; 4:4; 6:7) Malipoti amenewa ayenera kuti analimbikitsa kwambiri ophunzirawo. Ayenera kuti analimbikitsidwa kupitiriza kugwira ntchito imene Mulungu anawapatsa ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda.

21 Cha m’ma 60 mpaka 61 C.E., Paulo analemba kalata yake yopita kwa Akorinto ndipo m’kalatayo anafotokoza kuti uthenga wabwino ‘unkabala zipatso ndiponso kuwonjezeka m’dziko lonse’ komanso unali ‘utalalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’ (Akol. 1:5, 6, 23) Akhristu oyambirira ankamvera Mawu a Mulungu ndipo mzimu woyera unawathandiza kugwira ntchito yaikulu yolalikira pamene mtundu wa Ayuda unali usanawonongedwe m’chaka cha 70 C.E. Akhristu okhulupirika amenewa ayenera kuti ankalimbikitsidwa kwambiri kumva malipoti osonyeza kuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino.

Kodi inuyo mumaona kuti muyenera kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira mapeto asanafike?

22 Masiku anonso, gulu la Yehova limayesetsa kusunga malipoti okhudza mmene ntchito yolalikira ikuyendera pokwaniritsa lemba la Mateyu 24:14, lomwe limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” Monga atumiki odzipereka a Mulungu, tinapatsidwa ntchito imeneyi yomwe tikufunika kuigwira mwamsanga ndipo aliyense payekha ayenera kuigwira mwakhama mapeto asanafike. Yehova adzaonetsetsa kuti ntchito imeneyi yagwiridwa mokwanira ndipo ngati tingagwire nawo, adzasangalala nafe.​—Ezek. 3:18-21.

LIPOTI LANU LA UTUMIKI WAKUMUNDA

23 Kodi timafunika kuchitira lipoti zinthu ziti? Kapepala kamene timalandira kolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda kamasonyeza zimene tiyenera kulembapo. Komabe, mfundo zotsatirazi zingakhale zothandiza.

24 Pamalo olembedwa kuti “Zomwe Ndagawira (Pa Zipangizo Zamakono Kapena Zosindikizidwa),” lembani chiwerengero cha zinthu zonse zimene mwagawira kwa anthu amene si Mboni za Yehova zobatizidwa, kaya zinthuzo ndi zosindikizidwa kapena za pa zipangizo zamakono. Pamene palembedwa kuti “Mavidiyo Amene Ndaonetsa,” lembani maulendo amene mwaonetsa mavidiyo athu.

25 Pamalo olemba kuti “Maulendo Obwereza” muzilembapo chiwerengero cha maulendo onse omwe munakambirana ndi anthu omwe si Mboni za Yehova zodzipereka komanso zobatizidwa amene anasonyeza chidwi mutawalalikira koyamba. Mungapange ulendo wobwereza ngati mwabwereranso kwa munthuyo, mwamulembera kalata, kumuimbira foni, kumutumizira uthenga wapafoni kapena imelo, kapenanso ngati mwapita kukam’patsa mabuku ndi magazini. Nthawi iliyonse imene mwachititsa phunziro la Baibulo, mungalembenso ulendo wobwereza. Kholo limene limachita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse ndi banja lake lingalembe ulendo wobwereza umodzi pa mlungu ngati pali mwana yemwe ndi wosabatizidwa.

26 Ngakhale kuti timachititsa phunziro la Baibulo mlungu uliwonse, tiyenera kulemba phunziro limodzi kumapeto kwa mwezi. Ofalitsa ayenera kulemba chiwerengero chonse cha maphunziro a Baibulo amene achititsa m’mweziwo. Maphunziro a Baibulo amene tingachitire lipoti angaphatikizepo anthu amene si Mboni zodzipereka ndi zobatizidwa. Mungawerengerenso phunziro la Baibulo ngati mumaphunzira ndi m’bale kapena mlongo wofooka, mutauzidwa ndi mkulu mmodzi wa mu komiti ya utumiki kapena ngati mumaphunziranso ndi munthu yemwe wangobatizidwa kumene amene sanamalize buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa, ndi la Mulungu Azikukondani.

27 Ndi bwino kuti tizilemba chiwerengero cholondola cha “Maola.” Imeneyi ndi nthawi imene mwakhala mukulalikira kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, kuchititsa maphunziro a Baibulo kapena kulalikira kwa anthu amene mwangokumana nawo omwe si Mboni zobatizidwa. Ngati ofalitsa awiri akulalikira limodzi, onse angawerengere nthawi imene akhala akulalikira koma munthu mmodzi yekha ndi amene angachitire lipoti maulendo obwereza kapena maphunziro a Baibulo amene achititsa. Makolo akamathandizana kuphunzitsa ana awo pa Kulambira kwa Pabanja onse angawerengere ola limodzi pa mlungu. Abale angawerengerenso nthawi imene amakamba nkhani ya onse. Nayenso amene akumasulira nkhani ya onse akhoza kuchitira lipoti nthawi imene wakhala akumasulira nkhaniyo. Koma pali ntchito zina zofunika zimene siziyenera kuchitiridwa lipoti, monga kukonzekera utumiki wakumunda, kukhala pa msonkhano wokonzekera utumiki ndiponso nthawi imene timakhala tikugwira ntchito zina za mpingo.

28 Wofalitsa aliyense ayenera kukhala wosamala ndiponso kutsatira chikumbumtima chake pamene akuganizira zinthu zimene akhoza kuchitira lipoti. Ofalitsa ena amalalikira m’madera opezeka anthu ambiri, pamene ena amalalikira m’madera omwe kumapezeka anthu ochepa moti amayenda mtunda wautali kuti apeze anthu. Popeza madera olalikira amasiyana, ofalitsanso amasiyana mmene amaonera utumiki wawo. Bungwe Lolamulira silimasankhira mpingo wa padziko lonse zochita pa nkhani ya mmene wofalitsa aliyense angawerengere nthawi ya utumiki wakumunda ndipo silinapereke udindo kwa wina aliyense kuti azisankhira anthu zimenezi.​—Mat. 6:1; 7:1; 1 Tim. 1:5.

29 Tiyenera kuchitira lipoti maola okha, osati maminitsi. Munthu angachitire lipoti maminitsi pokhapokha ngati ndi wokalamba kwambiri, akudwala moti sakutha kuyenda, amakhala kunyumba zosungira anthu okalamba kapena sangathe kulalikira nthawi yaitali chifukwa cha mavuto ena. Ofalitsa ngati amenewa angamawerengere nthawi yawo pophatikiza ma 15 minitsi aliwonse amene alalikira. Ngakhale atalalikira kwa 15 minitsi yokha pamwezi, ayenerabe kuchitira lipoti nthawiyo. Ndipo angamaonedwebe ngati munthu amene nthawi zonse amalalikira za Ufumu. Zimenezi zikuphatikizaponso ofalitsa amene kwa mwezi umodzi wokha kapena ingapo, sangathe kulalikira bwinobwino chifukwa cha kudwala kwambiri kapena kuvulala. Ofalitsa amene angapereke lipoti lotereli, ndi okhawo amene ali ndi mavuto aakulu kwambiri moti sangathe kulalikira bwinobwino. Komiti ya utumiki ya mpingo ndi imene ingakambirane kuti ione ngati wofalitsa akuyenerera kupereka malipoti ake mwa njira imeneyi.

LIPOTI LA MPINGO LOLEMBAPO NTCHITO ZA WOFALITSA

30 Malipoti anu a utumiki wakumunda a mwezi uliwonse amalembedwa pa Lipoti la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa. Lipoti limeneli ndi la mpingo osati la wofalitsayo. Choncho ngati mukufuna kusamukira ku mpingo wina, dziwitsani akulu a mpingo wanu. Mlembi wa mpingo wanu wakale adzaonetsetsa kuti lipoti lanu lolembapo ntchito za wofalitsa latumizidwa kumpingo watsopanowo. Zimenezi zidzathandiza kuti akulu a mpingo umene mwasamukirawo akulandireni ndi kupitiriza kukuthandizani mwauzimu. Ngati mukuchoka kwa miyezi yosapitirira itatu, mungapitirize kutumiza malipoti anu a utumiki wakumunda kumpingo wanu womwewo.

UBWINO WOPEREKA MALIPOTI

31 Kodi nthawi zina mumaiwala kupereka malipoti anu? N’chifukwa chake tonsefe timafunika kukumbutsidwa nthawi ndi nthawi. Koma ngati timakhala ndi mtima wofunitsitsa kupereka lipoti ndiponso ngati timaona kufunika kwake, kudzakhala kosavuta kuti tizikumbukira kupereka lipoti lathu la utumiki wakumunda nthawi zonse.

32 Ena amafunsa kuti: “Poti Yehova amadziwa kale zimene ndimachita pomutumikira, n’chifukwa chiyani ndiyeneranso kupereka lipoti ku mpingo?” N’zoona kuti Yehova amadziwa zimene tikuchita ndiponso amatha kuona ngati tikumutumikira ndi mtima wonse kapena ngati tikungochita modzikakamiza. Komabe kumbukirani kuti Yehova analemba m’Baibulo nambala ya masiku amene Nowa anakhala m’chingalawa komanso zaka zimene Aisiraeli anayenda m’chipululu. Mulungu anasunganso chiwerengero cha anthu okhulupirika komanso cha osamvera. Analembanso zinthu zosiyanasiyana zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankagonjetsa dziko la Kanani komanso analemba zinthu zimene oweruza okhulupirika a Aisiraeli anachita. Iye ndi amene anathandiza anthu kuti alembe zinthu zambiri zimene atumiki ake ankachita ndipo zikutithandiza kudziwa mmene amaonera kufunika kosunga ziwerengero zolondola za zinthu.

33 Nkhani zokhudza mbiri yakale zimene zinalembedwa m’Baibulo zimasonyeza kuti anthu a Yehova ankasunga malipoti olondola a nkhani zosiyanasiyana. Nkhani zambiri zofotokozedwa m’Baibulo sizikanakhala zochititsa chidwi zikanakhala kuti sizinatchule manambala enieni a zinthu. Taonani zitsanzo izi: Genesis 46:27; Ekisodo 12:37; Oweruza 7:7; 2 Mafumu 19:35; 2 Mbiri 14:9-13; Yohane 6:10; 21:11; Machitidwe 2:41; 19:19.

34 N’zoona kuti malipoti athu samasonyeza zinthu zonse zimene tachita potumikira Yehova, komabe malipoti amenewa amakhala othandiza kwambiri m’gulu lathu. Kale atumwi atabwera kuchokera kolalikira, anapereka lipoti kwa Yesu la “zonse zimene iwo anachita ndi kuphunzitsa.” (Maliko 6:30) Nthawi zina malipoti amasonyeza kuti pali zinthu zina zokhudza utumiki wathu zimene sizikuyenda bwino. Mwachitsanzo akhoza kusonyeza kuti, ngakhale kuti chiwerengero cha zinthu zina chakwera, zinthu zina monga chiwerengero cha ofalitsa, zatsika. Malipoti ngati amenewa akhoza kusonyeza kuti ofalitsa akufunikira kulimbikitsidwa kapena kusonyeza kuti pali mavuto ofunika kukonzedwa. Oyang’anira akaona malipotiwo amayesetsa kukonza zimene zikulepheretsa anthu ena kapena mpingo wonse kupita patsogolo.

35 Malipoti amathandizanso gulu la Mulungu kudziwa madera amene kukufunika antchito ambiri. Komanso amathandiza kudziwa madera amene ntchito yolalikira ikuyenda bwino kwambiri, amene ntchito siikupita patsogolo kwenikweni komanso mabuku amene akufunika kuti athandize anthu kuphunzira choonadi. Malipotiwa amathandizanso gulu kudziwa mabuku amene angadzafunike m’tsogolo m’madera osiyanasiyana padziko lonse lapansi.

36 Ambirife timalimbikitsidwa kwambiri ndi malipoti amene timamva. Timasangalala kwambiri tikamamva zimene abale athu akuchita polalikira uthenga wabwino padziko lonse. Ziwerengero zikamakwera zimatithandiza kudziwa mmene gulu lonse la Yehova likukulira. Malipoti a mmene ntchito ya ofalitsa anzathu ikuyendera amatilimbikitsa kuti nafenso tizichita khama pa ntchito yolalikira. (Mac. 15:3) Tikamayesetsa kupereka malipoti a utumiki wathu timasonyeza kuti timaganizira abale athu padziko lonse. Kuchita zimenezi kungaoneke ngati nkhani yaing’ono koma zimasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova komanso timagonjera gulu lake.​—Luka 16:10; Aheb. 13:17.

MUZIKHALA NDI ZOLINGA

37 Palibe chifukwa choyerekezera lipoti lathu la utumiki wakumunda ndi la munthu wina. (Agal. 5:26; 6:4) Tikutero chifukwa zinthu pa moyo wa anthu zimasiyana. Tiyenera kukhala ndi zolinga zimene tikhoza kuzikwanitsa ndipo tingaone mmene tikuchitira utumiki wathu poganizira mmene tikukwaniritsira zolingazo. Kukwaniritsa zolingazi kungatithandize kuti tizisangalala ndi utumiki wathu.

38 Umboni ukusonyeza kuti Yehova akuchititsa kuti ntchito yosonkhanitsa anthu amene adzawapulumutse pa ‘chisautso chachikulu’ igwiridwe mofulumira. Panopa ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa. Ulosi wake ndi wakuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” (Chiv. 7:9, 14; Yes. 60:22) Tiyenera kuona kuti tili ndi mwayi waukulu kukhala atumiki olengeza uthenga wabwino m’masiku otsiriza ano.​—Mat. 24:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena