Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/96 tsamba 1-7
  • Perekani Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Perekani Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 4/96 tsamba 1-7

Perekani Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku

1 Tapatsidwa mwaŵi wapadera kwambiri. Ndiwo mwaŵi wa kukhala mboni za Yehova. Tili m’gulu lapadziko lonse la alaliki limene Yehova akugwiritsira ntchito kukwaniritsa ntchito yaikulu koposa ya kulengeza Ufumu imene sinachitikepo! (Marko 13:10) Poona kufulumira kwa nthaŵi yathu, kodi tikuichita ntchitoyi pamlingo wokwanira ndithu?

2 Sitikudziŵa unyinji wa amene potsiriza adzalabadira kulalikira kwathu. Yehova akutilonjeza kuti lidzakhala “khamu lalikulu,” amene onse akudziŵika mwa “kupereka kwa iye utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:9, 15, NW) Mboni zoposa mamiliyoni asanu zimene zikuchita changu mu utumiki wa Mulungu sizili chabe omvetsera ochita chidwi, sizilinso anthu ongopezeka pamisonkhano. Ali antchito olengeza uthenga wabwino padziko lonse!

3 Tsiku ndi tsiku, pamakhala mipata yakutamanda Yehova, kaya mu utumiki wakumunda kapena mwamwaŵi. Talingalirani za umboni waukulu umene ungaperekedwe ngati ife aliyense payekha tingayambe kumagaŵana choonadi ndi munthu mmodzi chabe tsiku lililonse. Chiyamikiro chathu kwa Yehova chiyenera kutisonkhezera kulankhula za iye mwachangu.—Sal. 92:1, 2.

4 Thandizani Ena Kupereka Utumiki Wopatulika: Yehova wapitiriza kutidalitsa ndi chiwonjezeko. (Hag. 2:7) Chaka chatha chautumiki m’Malaŵi, avareji ya maphunziro a Baibulo apanyumba omwe anachititsidwa mwezi uliwonse inali 27,723. Cholinga chathu pophunzira ndi anthu aŵa ndicho kuwathandiza kukhala ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19, 20) Ambiri a iwo apita kale patsogolo bwino lomwe mwa kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. Ayamba kulankhula kwa anansi awo “zazikulu za Mulungu” zimene aphunzira. (Mac. 2:11) Kodi iwo tsopano angapemphedwe kutengamo mbali mu utumiki wapoyera?

5 M’April tiyenera kuyesetsa ndithu kupempha atsopano amene ayenerera kutsagana nafe mu utumiki wakumunda. Kodi wophunzira wanu wakuuzani kuti akufuna kuchita zimenezi? Ngati watero, kodi akufitsa zofunika za Malemba? (Onani buku la Uminisitala Wathu, masamba 97-9.) Pamene wophunzirayo afuna kutengamo mbali mu utumiki wakumunda, kambitsiranani za chikhumbo chake ndi woyang’anira wotsogoza, amene adzalinganiza kuti akulu aŵiri apende nkhaniyo. Ngati wophunzirayo ayeneretsedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa, m’pempheni kutsagana nanu m’munda. Oyang’anira utumiki ndi ochititsa maphunziro a buku ayenera kukhala atcheru kwambiri kuthandiza aja amene angayeneretsedwe kuti ayambe kufalitsa m’April.

6 Makolo angaone ngati ana awo akuyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa. (Sal. 148:12, 13) Ngati mwana wanu akufuna kumalankhula mu utumiki wa Ufumu ndipo ali ndi khalidwe labwino, mungapite kwa mmodzi wa akulu a m’komiti yautumiki kumuuza za nkhaniyo. Atakumana ndi inu limodzi ndi mwana wanu, akulu aŵiri adzaona ngati mwana wanu ali woyenerera kukhala wofalitsa. Pamakhala chifukwa chachikulu chokhalira ndi chimwemwe pamene ana athu atsagana nafe kutamanda Mulungu!

7 Yehova yekha ndiye ayenerera utumiki wathu wopatulika. (Luka 4:8) Tiyeni tonsefe tigwiritsire ntchito mwaŵi wathu wabwino kwambiri wakumtamanda iye “kwakukulu.”—Sal. 109:30; 113:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena