Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
1 Pamene tikuloŵa nyengo ya Chikumbutso ya chaka cha 2003, tili ndi zifukwa zambiri zokhalira ‘achangu pa zinthu zabwino.’ (1 Pet. 3:13) Chifukwa chachikulu chimene chawachititsa anthu ambiri kukhala a changu ndi nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Mogwirizana ndi zimenezi, mtumwi Petro analemba kuti: “Simunawomboledwa ndi zovunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe. . . . Koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.” (1 Pet. 1:18, 19) Pofuna kuyamikira chikondi chopambana chimenechi, timayesetsa kukhala otanganidwa pochita zabwino, tikumazindikira kuti Yesu “anadzipereka yekha m’malo mwa ife, kuti akatiwombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.”—Tito 2:14; 2 Akor. 5:14, 15.
2 Tikamachita zimene zimakondweretsa Mulungu, timakhala naye pa ubale wabwino ndipo amatisamalira mwachikondi. Petro anapitiriza kuti: “Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, . . . apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola. Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.” (1 Pet. 3:10-12) Mu nthaŵi zoopsa zino, ndi dalitsotu kudziŵa kuti Yehova akutiyang’anira ndipo ndi wokonzeka ‘kutisunga ngati kamwana ka m’diso.’—Deut. 32:10; 2 Mbiri 16:9.
3 Ngakhale kuti Akristu oyambirira amene Petro anawalembera kalata anakumana ndi ziyeso, anali ndi changu chimene sichikanazilala, ndipo analalikira uthenga wabwino kulikonse kumene akanatha kupita. (1 Pet. 1:6; 4:12) N’chimodzimodzinso ndi anthu a Mulungu lerolino. Ngakhale kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” kuyamikira ubwino wa Yehova kumatilimbikitsa kuti tichite chifuno cha Mulungu mwachangu. (2 Tim. 3:1; Sal. 145:7) Tiyeni tione zina mwa ntchito zabwino zimene zititagwanitse nyengo ya Chikumbutso ikubwerayi.
4 Itanirani Ena ku Chikumbutso: Njira imodzi imene tingasonyezere kuyamikira mphatso yopambana ya dipo ndi kupezeka pa mwambo wapachaka wokumbukira imfa ya Yesu. Chaka chino mwambowu udzachitika Lachitatu, April 16, dzuŵa litalowa. (Luka 22:19, 20) Chaka chatha, mipingo 94,600 inapereka lipoti padziko lonse, ndipo atawonkhetsa ziŵerengero zonse tinakwana 15,597,746! Chiŵerengero chimenechi chinaposa cha chaka chinacho ndi anthu 220,000.
5 Kodi chaka chino padzabwera anthu angati? Makamaka zikudalira khama lathu polimbikitsa ena kuti adzasonkhane nafe. Yambani ndi kulemba mayina a onse amene mukufuna kuwaitana. Pamwamba pa mayinawo pakhale a m’banja lanu. Ngati mkazi kapena mwamuna wanu ndi wosakhulupirira, m’fotokozereni ndi mtima wonse kuti mukufunitsitsa atasonkhana nanu. Mwamuna wina wosakhulupirira ananena kuti anakapezeka pa Chikumbutso chaka chatha chifukwa chakuti anaona kuti imeneyi ndi nkhani yaikulu kwa mkazi wake komanso kuti mkazi wakeyo adzasangalala iye akapezekapo. Kenako, pa mayinawo pangakhale achibale, anansi, ogwira nawo ntchito, kapena anzanu akusukulu. Tsimikizirani kuti mwaitananso ophunzira Baibulo anu.
6 Mukalemba mayina, patulani nthaŵi yoti mukalankhule ndi aliyense amene mwamulemba dzina. Gwiritsani ntchito timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Kuti muthandize anthu kukumbukira tsiku ndi malo kumene Chikumbutso chikachitikire, lembani mooneka bwino nthaŵi ndi malo ake m’munsi mwa kapepalako. Tsiku la April 16 likayandikira, kumbutsani onse amene munawalemba mayinawo, pokawayendera kapena powaimbira telefoni. Tiyeni tiyesetse kuthandiza anthu ambiri kuti adzapezeke pa mwambo wopatulika umenewu.
7 Thandizani Amene Afika Pachikumbutso: Nthaŵi zonse usiku umene Chikumbutso chimachitika umakhala nthaŵi yosangalatsa. Timakhala ndi mwayi wolandira anthu amene sabwera nthaŵi zonse pa misonkhano yathu. Konzani zodzafika mofulumira ndi kusachoka msanga, ngati zingatheke malinga ndi kwanuko. Yesetsani kuti mudziŵane ndi atsopano amene abwera. Khalani womasuka ndiponso wochezeka.—Aroma 12:13.
8 Kodi mungathandize ena opezeka pa Chikumbutso kuti apite patsogolo mwauzimu pochita nawo phunziro la Baibulo? Yesetsani kutenga mayina ndi maadiresi a alendo alionse amene alibe owayendera kuti muwathandize. Mukawathandiza mwachikondi, ena mwa ameneŵa angapite patsogolo mpaka kuyeneretsedwa kukhala ofalitsa osabatizidwa Chikumbutso cha chaka chamaŵa chisanafike. Mukamapita kwa amene anapezeka pa Chikumbutso, aitanireninso ku nkhani yapadera imene idzakambidwa pa April 27.
9 Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza Chaka Chino? Chaka chilichonse changu chathu kwa Yehova chimatilimbikitsa kuchita khama pa utumiki m’miyezi imeneyi pamene timakhala ndi ntchito yaikulu mu mpingo. Chaka chatha m’Malaŵi muno, tinali ndi apainiya othandiza 3,247 m’mwezi wa March ndi 3,141 m’mwezi wa April. Zimenezi zikutanthauza kuti avareji ya mwezi uliwonse inali 3,194. Sikuti ziŵerengero zimenezi ndi zongoyerekeza koma zikusonyeza khama limene mipingo yonse inachita polalikira uthenga wabwino nyengo ya Chikumbutso imeneyi.
10 Mpingo wina wa ofalitsa 107 ndi apainiya okhazikika 9 unachita lipoti kuti unali ndi “mwezi wapadera kwambiri” mu April chaka chatha. Anthu 53 anachita upainiya wothandiza, pamodzi ndi akulu ndi atumiki otumikira onse. Kodi akulu anachita bwanji kuti alimbikitse ena kukhala ndi mtima wofuna kuchita upainiya wothandiza mwezi umenewo? Anayambirira kulimbikitsa anthu ambiri kulembetsa upainiya wothandiza. Anachita misonkhano yokonzera utumiki wa kumunda nthaŵi zosiyanasiyana pa tsiku kuti igwirizane ndi onse mu mpingomo. Anafotokozanso mwapadera kufunika kolalikira pa telefoni, makamaka kwa ofalitsa okalamba amene thanzi lawo linali lofooka.
11 Mlongo wina wa zaka 86, amene satha kuyenda chifukwa cha mavuto athanzi, analembetsa upainiya wothandiza. Kuyambira m’maŵa, ankachita ulaliki wa pa telefoni kwa maola angapo atakhala pa thebulo la kukhichini. Amapuma kwa maola ochepa, kenako n’kuyambiranso. Mkazi wina amene anamuimbira telefoni mwamuna wake ndi ana ake aamuna aŵiri achinyamata anali atamwalira zaka ziŵiri m’mbuyomo, ndipo samamvetsa chifukwa chimene Mulungu amalolera zinthu zoipa ngati zimenezo kuchitika. Anamulalikira mogwira mtima, ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo.
12 Akulu aja anamaliza lipoti lawo ponena kuti: “Tinasangalala zedi ndipo tikuthokoza kwambiri mwayi ndi madalitso amene Yehova wapatsa aliyense wa ife.” Mukakonzekera bwino, mpingo wanunso ungakhale ndi madalitso ngati ameneŵa.
13 Yesetsani Kuchita Utumiki Mokwanira: Chifukwa chokonda Mulungu ndi anansi athu, timapeza nthaŵi mwezi uliwonse youza ena uthenga wabwino. (Mat. 22:37-39) Oyang’anira Maphunziro a Buku a Mpingo ndi owathandiza awo aziyesetsa kuthandiza amene ali m’gulu lawo kuti achite nawo utumiki mwezi uliwonse. Njira yabwino yochitira zimenezi ndi kupangana pasadakhale ndi munthu wina m’gulu lawo kuti adzapitire limodzi mu utumiki. M’malo moyembekezera kuchita zimenezi pamapeto pa mwezi, yambirirani. Zimenezi zidzakuthandizani kukhala ndi mipata yambiri yothandiza ena mwachikondi.
14 Kodi m’gulu lanu la phunziro la buku muli ndi ofalitsa okalamba amene thanzi lawo ndi lofooka moti amavutika kwambiri kuchita nawo utumiki? Ngati ena akudwalira kunyumba zawo, n’zomveka kuti sangachite ulaliki mokwanira. Koma mwa kugwiritsa ntchito mipata yochepa yomwe amakhala nayo kuti awalitse kuunika kwawo, angathandize anthu amene amaona ntchito zawo zabwino kuchitadi chidwi ndi choonadi. (Mat. 5:16) Oyang’anira maphunziro a buku ayenera kutsimikizira kuti anthu oterewa akudziŵa kuti akhoza kupereka lipoti la ntchito ya utumiki wa kumunda mphindi 15, 30, kapena 45. Ofalitsa okhulupirika ameneŵa akamatha kupereka lipoti la nthaŵi imene athera mu ulaliki, zimawalimbikitsa ndipo amasangalala. Zimathandizanso kuti lipoti la padziko lonse la ntchito ya anthu a Mulungu ikhale yolondola.
15 Achinyamata Amene Atanganidwa ndi Kuchita Zabwino! N’zolimbikitsa kwambiri kuona Akristu achinyamata akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mu utumiki wa Yehova! (Miy. 20:29) Ngati ndinu wachinyamata, kodi mungasonyeze bwanji changu chanu kwa Yehova miyezi ya ntchito yapadera kwambiri imeneyi?
16 Ngati simuli wofalitsa wosabatizidwa mu mpingo, kodi zingatheke kuti mukhale wofalitsa wosabatizidwa? Dzifunseni mafunso otsatiraŵa: ‘Kodi ndili ndi chidziŵitso choyambirira cha choonadi cha Baibulo? Kodi ndikufuna kuchita nawo utumiki wa Ufumu? Kodi ndine wakhalidwe labwino? Kodi ndingathe kusonyeza chikhulupiriro changa mwa kuuuza ena uthenga wabwino? Kodi ndingatero kuchokera pansi pa mtima?’ Ngati mungayankhe kuti inde mafunso ameneŵa, uzani makolo anu kuti mukufuna kukhala wofalitsa. Makolo anu angalankhule ndi mmodzi wa akulu amene ali m’komiti ya utumiki.
17 Ngati muli kale wofalitsa uthenga wabwino, kodi mungagwiritse ntchito tchuti cha kusukulu kuti muwonjezere utumiki wanu? Mwa kukhala ndi ndandanda yabwino ndiponso chithandizo cha makolo ndi ena, achinyamata ambiri obatizidwa atha kuchita upainiya wothandiza. Ngati zimenezo sizingatheke, yesetsanibe kuwonjezera mbali yanu mu utumuki wa kumunda. Dziikireni cholinga. Kuwonjezera pa cholinga cha maola, khalaninso ndi cholinga china pa utumiki wanu. Mwina mungayesetse kuŵerenga lemba panyumba iliyonse, kuwongolera luso lanu pa maulendo obwereza, kuyambitsa phunziro la Baibulo, kapena kuwonjezera utumiki wanu kuti muzichitako mbali zina za utumiki. Kodi mungakhale ndi cholinga choti mudzakhale ndi mnansi, mnzanu wakusukulu, kapena wachibale pa Chikumbutso chaka chino? Kuchita nawo mokwanira ntchito zimenezi kudzakhala kopindulitsa ndipo mosakayikira kudzalimbikitsa ena mu mpingo.—1 Ates. 5:11.
18 Thandizani Atsopano Kupita Patsogolo: M’kati mwa chaka cha utumiki chimene chapitachi, pankachitika maphunziro a Baibulo apanyumba okwana 42,394 pa avareji m’Malawi muno mwezi uliwonse. Pakapita nthaŵi, ambiri mwa ophunzira ameneŵa afika podzipatulira ndi kubatizidwa. Komabe, asanafike pa cholinga chimenechi, tifunika kuwathandiza kuti ayenerere kukhala ofalitsa uthenga wabwino. Mbali imeneyi n’njofunika pophunzitsa atsopano kuti akhale otsatira Yesu Kristu. (Mat. 9:9; Luka 6:40) Kodi muli ndi wophunzira Baibulo amene ndi wokonzeka kutero?
19 Ngati simukutsimikiza za kupita patsogolo kwa wophunzira wanu, pemphani woyang’anira phunziro lanu la buku kapena woyang’anira utumiki kuti akuthandizeni. Mwina mungakhale naye pamene mukuchititsa phunziro. Abale ameneŵa ali ndi luso limene lingawathandize kudziŵa mmene wophunzira akupitira patsogolo mwauzimu. Angakhalenso ndi malingaliro amene angathandize wophunzira kupitiriza kupita patsogolo mwauzimu.
20 Ngati wophunzira wanu akusonyeza chidwi chofuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo mukuona kuti akuyenerera, lankhulani ndi woyang’anira wotsogolera. Woyang’anira wotsogolera adzakonza zoti akulu aŵiri akumane ndi inuyo pamodzi ndi wophunzira wanuyo kuti aone ngati akuyenerera, pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa masamba 98-99 a buku la Utumiki Wathu. (Onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 1998, tsamba 17.) Ngati wophunzira wayeneretsedwa kukhala wofalitsa, yambani kum’phunzitsa kulalikira nthaŵi yomweyo. Mpingo udzadziŵitsidwa kuti wophunzirayo ndi wofalitsa wosabatizidwa, akangopereka lipoti la utumiki wa kumunda. Tikulakalaka kuti ofalitsa atsopano ambiri, achinyamata ndi achikulire omwe, atafika pochita zimenezi pa miyezi imeneyi pamene timakhala ndi ntchito yaikulu.
21 Kukonzekera Kumathandiza Kuchita Zochuluka: Kukonzekereratu kungatithandize kuti tipambane pa ntchito yathu nyengo ya Chikumbutso imeneyi. (Miy. 21:5) Pali zinthu zambiri zofunika kuti akulu azisamalire.
22 Kuti akulu athandize mpingo kuchita zochuluka mu utumiki, ayenera kuchita zotheka pokonzeratu zokhala ndi misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda m’kati mwa mlungu wonse ndiponso pamapeto pa mlungu. Woyang’anira utumiki ayenera kutsogolera pokonza zimenezi. Kodi misonkhano ina yokonzekera utumiki ingakonzedwe kuti izikhala m’mamaŵa, kumasana, kapena chakumadzulo? Mudziŵitse mpingo zimene zakonzedwa. Zingakhale zothandiza ngati ndandandayo itaikidwa pa bolodi la chidziŵitso.
23 Akulu atsimikizire kuti zimene akonza pa Chikumbutso zakonzedwa bwino tsiku la April 16 lisanafike. Zimenezi zingaphatikizepo kukambirana za mmene mungagwiritsire ntchito Nyumba ya Ufumu ndi mipingo ina imene ingasonkhane pa Nyumba ya Ufumuyo, komanso kuyeretsa Nyumba ya Ufumuyo, kusankha akalinde ndi oyendetsa zizindikiro, ndi kupeza zizindikiro. Mpingo uyenera kudziŵitsidwa za nthaŵi ndi malo a Chikumbutso ndi kusintha kulikonse pa nthaŵi ya misonkhano ya mlunguwo. Kusamalira zinthu zimenezi mwakhama kudzathandiza kuti mwambowu ‘uchitike moyenera ndi molongosoka.’—1 Akor. 14:40.
24 Mitu ya mabanja ingafune kuti pa phunziro lawo la banja akambirane mmene banja lingachitire nawo ntchito yapadera imeneyi nyengo ya Chikumbutsoyi. Kodi banja lanu lonse lingachite upainiya wothandiza? Kapena kodi banja lanu lingathandize mmodzi kapena angapo kuchita upainiya wothandiza? Ngati zimenezi n’zosatheka, khalani ndi zolinga zapadera monga banja kuti muthere nthaŵi yambiri mu utumiki. Kodi m’banja lanu muli wachinyamata amene, ngati mutamulimbikitsa pang’ono ndi kumuthandiza, angayenerere kukhala wofalitsa wosabatizidwa? Kodi banja lanu lingaitane anthu angati ku Chikumbutso chaka chino? Kukonzekera bwino kudzabweretsa madalitso ndi chisangalalo m’banja lanu.
25 Nthaŵi Yotsalayi N’njofunika Kuigwiritsa Ntchito bwino: Polembera Akristu a m’zaka 100 zoyambirira, mtumwi Petro anawakumbutsa kufunika kochita changu chifukwa mapeto a dziko la Ayuda anali atayandikira. (1 Pet. 4:7) Lerolinonso umboni ukusonyeza kuti mapeto a dziko lonse ayandikira. Tsiku ndi tsiku, moyo wathu uzisonyeza kuti tikudziŵa zimenezi. Monga atumiki achangu a Yehova, tiyenera kuika mtima pa ntchito yofunika changu yolengeza uthenga wabwino.—Tito 2:13, 14.
26 Ino ndiyo nthaŵi yoti tisonyeze changu pa ntchito! Sinkhasinkhani zimene Yehova wakuchitirani, wachitira banja lanu, ndiponso mpingo wanu. Ngakhale kuti sitingamubwezere zinthu zabwino zambiri zimene watichitira, tingalambire Yehova ndi mtima wonse. (Sal. 116:12-14) Tikayesetsa mwakhama, adzatifupa ndi kutidalitsa. (Miy. 10:22) Tiyenitu tonse tikhale ‘achangu pa zinthu zabwino’ nyengo yapadera imeneyi, “kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu.”—1 Pet. 3:13; 4:11.
[Bokosi patsamba 3]
Amene Anapezeka pa Chikumbutso Padziko Lonse
1999 14,088,751
2000 14,872,086
2001 15,374,986
2002 15,597,746
[Bokosi patsamba 4]
Kodi Mudzaitana Ndani pa Chikumbutso?
□ A m’banja lathu ndi achibale
□ Achinansi ndi odziŵana nawo
□ Anzathu a kuntchito ndi a kusukulu
□ Amene timachitako maulendo obwereza ndi ophunzira Baibulo
[Bokosi patsamba 5]
Thandizani Amene Afika pa Chikumbutso
□ Alandireni mwansangala
□ Ayendereni Chikumbutso chikapita
□ Apempheni kuphunzira nawo Baibulo
□ Aitaneni ku nkhani yapadera
[Bokosi patsamba 6]
Kodi Zolinga Zanu N’zotani Nyengo ya Chikumbutso Ino?
□ Yesetsani kuti wina amene munamuitana adzapezeke pa Chikumbutso
□ Yenererani kukhala wofalitsa wa uthenga wabwino
□ Mukhale ndi maola amene mukufuna kudzathera mu utumiki
□ Wongolerani luso lanu pa mbali inayake ya utumiki
□ Tumikirani monga mpainiya wothandiza