Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?
1 Lachitatu madzulo, pa April 19, lidzakhala tsiku lofunika kwambiri m’chaka chathu chautumiki. Patsiku limenelo, pamene dzuŵa likuloŵa nthaŵi yosiyanasiyana padziko lonse, mpingo uliwonse ndi gulu la Mboni za Yehova padziko lonse lidzachita Chikumbutso cha Imfa ya Kristu. Kaya timakhala kudera lomwe dzuŵa limaloŵa mofulumira kusiyana ndi malo ena, kukumbukira nsembe ya Yesu Kristu chidzakhala chochitika chapadera kwambiri cha pachaka. Tsiku la Chikumbutso pa Kalendala ya 2000 ya Mboni za Yehova pa mwezi wa April lili ndi chizindikiro.
2 Mwezi wonse wa April ukutipatsa mpata wabwino kwambiri wosonyeza ndi mtima wonse kuyamikira kwathu kukoma mtima kumene Yehova anasonyeza mwa nsembe ya Mwana wake. Motani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akor. 5:14, 15) Inde, m’April tingasonyeze kuti sitikukhalanso ndi moyo kwa ife tokha, koma kwa iye amene anatifera, tikumapanga zimenezi monga atumiki a Ufumu m’mwezi wathu wabwino kuposa yonse!
3 Lembetsani Upainiya Wothandiza m’April: Mtumwi Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino pamene anati: “Sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.” (Mac. 20:24) Tili ndi mwayi womwewo wochitira umboni za Yehova Mulungu. Pachifukwa chimenechi, tikufuna kupanga mwezi wa April kukhala mwezi wathu wabwino kuposa yonse mu ntchito ya upainiya wothandiza!
4 Popeza uli ndi mapeto a mlungu asanu, mwezi wa April 2000 udzakhala mwezi wabwino kwambiri kwa anthu ambiri kuchita upainiya. M’mbuyomo mu April 1997, pamene tinafika chiŵerengero chathu chapamwamba choposa ziŵerengero zina zonse za apainiya othandiza, anthu 3,999 amene anachita nawo inaimira 10 peresenti ya chiŵerengero chonse cha ofalitsa. Patatha zaka ziŵiri, chiŵerengero cha ofalitsa amene anapereka lipoti mu April 1999 chinawonjezeka kwambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti tingathe kuposa chiŵerengero chapamwamba cham’mbuyomu cha apainiya othandiza. Komanso, chiŵerengero cha maola ofunika chinachepetsedwa, zimene zikupangitsa mbali imeneyi ya utumiki kukhala yosavuta kwa anthu ena ambiri mu mpingo. Wofalitsa aliyense wobatizidwa ayenera kupenda mwapemphero ngati angathe kuchita upainiya wothandiza m’April muno.
5 Mwa kugwiritsa ntchito mwezi wa April pa Kalendala ya 2000, mu mphatika ino, konzani ndandanda yanu pakalipano ya mwezi wamaŵa. Sankhani masiku amene mungadzaloŵe nawo mu utumiki wakumunda, ndipo phatikizani maola onse amene mukuona kuti mungathere mu ntchito yolalikira mwezi umenewu. Phatikizanipo nthaŵi imene mungathere pochitira umboni ena mokonzekera ndi mwamwayi momwe. Kodi onse pamodzi akukwana maola 50 ofunika kwa apainiya othandiza? Ngati sakukwanira maola ofunikawo, kodi mungasinthe zina ndi zina pandandanda yanu kuti muwombole nthaŵi yochitira upainiya wothandiza? Mudzafunika kukwanitsa ola limodzi lokha ndi mphindi 40 patsiku mu utumiki kuti mukwanitse maola 50 pamwezi.
6 Popeza kuti tsopano maola ofunika kwa apainiya okhazikika achepetsedwanso, kodi mwakhala mukuganiza zoyamba utumiki wanthaŵi zonse? Ngati mukukayikira kuti mutha kukwanitsa maola 70 ofunika kwa apainiya okhazikika, bwanji osachita upainiya wothandiza mu April ndi kuika cholinga chanu kukhala kukwanitsa maola 70? Mukaona kuti mukhoza kukwanitsa, ndiye kuti mukhoza kufunsira upainiya wokhazikika nthaŵi yomweyo.—Onani Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 113-14.
7 Tenganimo Mbali Mokwanira Monga Wofalitsa wa Uthenga Wabwino: Tonse, ofalitsa ndi apainiya omwe, chikondi chathu chenicheni pa Mulungu ndi mnansi chimatisonkhezera kuchita ndi mtima wonse zomwe tingathe mu utumiki wa Yehova malinga ndi mikhalidwe yathu yaumwini. (Luka 10:27) Chotero timasonyeza kuti “tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupira.” (1 Tim. 4:10) N’chifukwa chake tiyenera kuyembekezera kuona tonse tikutengamo mbali mu April, aliyense akuchita mokwanira mu ntchito ya Ufumu.
8 Tisaiwale langizo la Yesu: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” Atatha kunena zimenezi, Yesu anaitana ophunzira ake 12 ndi kuwatumiza kokalalikira. (Mat. 9:37, 38; 10:1, 5, 7) Patapita pafupifupi chaka chimodzi, ophunzira 12 aja ataphunzitsidwa bwino m’ntchito yolalikira, Yesu “anaika ena makumi asanu ndi aŵiri, nawatuma,” nawapatsa malangizo ofananawo: “Dzinthu dzichuluka, . . . potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.” (Luka 10:1, 2) Buku la Baibulo la Machitidwe limanena mmene Yehova anayankhira mapemphero amenewo. Pa Pentekoste wa 33 C.E., chiŵerengero cha ophunzira chinakula mpaka pafupifupi 120. Kenako, anafika ziŵerengero zapamwamba zotsatizana za ophunzira 3,000 ndi 5,000. (Mac. 1:15; 2:41; 4:4) Zitatha zimenezo, “chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu.” (Mac. 6:7) Mofananamo, nthaŵi yamakono ino, tiyenera kupitiriza kupempha Ambuye kuti atipatsebe olalikira Ufumu ambiri! Mogwirizana ndi mapemphero athu, wofalitsa wampingo aliyense ayenera kupanga makonzedwe enieni kuti aziloŵa nawo mu utumiki mwezi uliwonse.
9 Chonde onani bwinobwino mwezi wa April pa Kalendala ya 2000. Popeza masiku aŵiri oyambirira a mwezi ndi Loŵeruka ndi Lamlungu, kodi mungakonze zopita nawo mu utumiki mapeto a mlungu umenewo, mukumayambirira mwezi umenewo? Kodi mungachirikize “Tsiku la Magazini” lililonse m’mwezi umenewu ndi gulu lanu la Phunziro la Buku la Mpingo? Bwanji zokhala mu utumiki ola kapena kuposerapo Lamlungu lililonse? Musaiwale kupezerapo mwayi mipata yonse imene muli nayo yochitira umboni mwamwayi kuntchito, kusukulu ndi pamene muli mu ntchito zina zatsiku ndi tsiku. Ikani chizindikiro pamasiku amene mungathere nthaŵi yambiri mu utumiki. Gwiritsani ntchito kalendala imeneyi kulembapo maola anu a muutumiki wakumunda mwezi umenewu.
10 April idzakhala nthaŵi yabwino kwa onse amene ali oyeneretsedwa ndipo amene akulu awavomereza kuyamba kutumikira monga ofalitsa osabatizidwa. Ngati mukuphunzira Baibulo ndi wina wake, kodi munthu ameneyo wapita patsogolo mokwanira kwakuti mungauze woyang’anira wotsogolera kuti am’pende kukhala wofalitsa wa uthenga wabwino? Ngati muli ndi ana osabatizidwa, kodi munakambiranako ndi akulu ponena za kupita kwawo patsogolo mwauzimu? Kodi imeneyi singakhale nthaŵi yawo yabwino yoyamba kufalitsa?—Onani Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 97-100.
11 Poyesetsa kupanga mwezi wa April 2000 kukhala mwezi wathu wabwino kuposa yonse, tonsefe tiyenera kutenga mbali mu utumiki ndiyeno m’kupereka lipoti la mu utumiki wakumunda pakutha pamwezi. (Yerekezani ndi Marko 6:30.) Ofalitsa atsopano osabatizidwa amene akuloŵa nawo mu utumiki wakumunda koyamba ayenera kulimbikitsidwa kupereka lipoti la ntchito yawo panthaŵi yake. Mwa kuchita mbali yathu, tingathandize kwambiri lipoti la April ndiponso kukweza mfuu ya chitamando imene idzapita kwa Yehova mwa khama lathu pochitira umboni.
12 Bwerani ndi Ena ku Chikumbutso: Kodi Sizidzakhala zotisangalatsa kuona chiŵerengero chatsopano chapamwamba cha opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu cha 2000? Inde! Chifukwa zidzatanthauza kuti anthu ambiri kuposa nthaŵi zina zonse asonkhana nawo kudzasonyeza kuyamikira kwawo njira yaikulu yosonyeza chikondi imene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anatichitira! (Yoh. 3:16; 15:13) Pangani makonzedwe ena alionse amene ali ofunika kuti china chilichonse chisadzalepheretse inu ndi banja lanu kupezeka pa Chikumbutso.
13 Tsopano ndi nthaŵinso yoyamba kuitanira ena ku Chikumbutso. Lembani ndandanda ya anthu amene mukufuna kuti adzapezekepo. Phatikizanipo aliyense amene munaphunzira naye Baibulo papitapo, amene mukuphunzira nawo pakalipano, ndi maulendo anu obwereza onse. Pandandandapo lembaniponso anzanu akuntchito, kusukulu, ndi amene mumakhala nawo pafupi, komanso aliyense amene mumachita naye malonda. Osaiŵala kuphatikizapo anzanu ena ndi achibale anu. Mukatha kulemba ndandandayo, yambani kuitana mosangalala aliyense payekha. Tchulani bwinobwino nthaŵi ndi malo amene kukachitikire Chikumbutso. Pamene tsiku la April 19 likuyandikira kwambiri, akumbutseni amene ali pandandanda yanuwo, kaya kupita kwawo kapena kuwaimbira telefoni. Dziperekeni kudzayenda nawo limodzi usiku umenewo popita ku Chikumbutso.
14 Mogwirizana ndi malangizo a Sosaite a m’mbuyomo, bungwe la akulu lidzayesetsa kulimbikitsa ofalitsa onse ofooka m’gawolo kuti adzapezeke pa Chikumbutso. (Mat. 18:12-14) Akulu adzayenera kupenda kalata ya Sosaite ya February 2, 1999. Mlembi wampingo ayenera kulemba ndandanda ya ofalitsa onse ofooka, ndiyeno woyang’anira utumiki adzasankha akulu oti akawayendera ndi kuwaitanira ku Chikumbutso. Mwinamwake kukawalimbikitsa mofulumira, anthu ofooka ameneŵa angathandizidwe kukhalanso achangu mu utumiki wakumunda, ngakhalenso m’April. Kudzakhala kolimbikitsa kwa iwo kuitanidwa ndi wofalitsa wozoloŵera utumiki kuti aloŵe naye limodzi mu utumiki wakumunda.
15 Limbikitsani Anthu Kuchirikiza Kwambiri Mwezi wa April! Zidzafunika kuti onse akulu, atumiki otumikira, ndi mitu ya mabanja agwirizane kuti tipange mwezi wa April 2000 kukhala mwezi wathu wabwino kuposa yonse. Akulu adzachita khama kulinganiza zinthu zonse bwinobwino ndi kutsogolera. (Aheb. 13:7) Padzafunika makonzedwe oyenera okonzekera misonkhano ya utumiki wam’munda m’kati mwa mlungu ndi kumapeto a mlungu. Ndandanda yonse imene yakonzedwa m’April iyenera kuikidwa pa bolodi la chidziŵitso. Padzafunika kum’patsa wina ntchito yosamalira msonkhano uliwonse wokonzekera utumiki. Payenera kukhala gawo lokwanira logwirizana ndi kukula kwa gulu lililonse.
16 Mu April tidzagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Poyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, bulosha la Mulungu Amafunanji lidzaperekedwa kwa onse osonyeza chidwi. Chotero, payenera kukhala magazini ndi mabulosha ambiri.
17 Pamapeto pa mwezi, ochititsa maphunziro a buku onse ndi othandizira awo onse adzafunikira kulimbikitsa aliyense wa m’gulu lawo kupereka malipoti autumiki mwamsanga mwezi ukatha. Zimenezi zingachitike ngakhale Lamlungu, pa April 30. Ndiyeno, pamene mlembi akuŵerengera malipoti, ngati waona kuti ofalitsa ena sanapereke, angawakumbutse mwachikondi kuti apereke pasanafike pa May 6, pamene adzatumiza lipoti la mpingo ku Sosaite. Angapemphe ochititsa maphunziro a buku kum’thandiza kufikira wofalitsa aliyense payenkha.
18 Kwa anthu a Mulungu, nthaŵi ya Chikumbutso ndi nyengo yofunika kwambiri pachaka. Iyenera kukhala nthaŵi yotanganidwa kwambiri kwa tonsefe mu utumiki wa Yehova. Idzatero ngati aliyense monga wofalitsa wa uthenga wabwino adzatengamo mbali mokwanira, ngati amene angalembetse kuchita upainiya angatero, ndipo ngati tichita khama kubwera ndi ena ku Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Tiyeni tipempherere madalitso ochuluka a Yehova pamene tikuyesetsa kupanga mwezi wa April 2000 kukhala mwezi wathu wabwino kuposa yonse, ku thamo ndi ulemerero wa Mulungu!—Aheb. 13:15.
[Bokosi patsamba 3]
Apainiya Othandiza
Chiŵerengero Chathu Chapamwamba Choposa Ziŵerengero Zonse: 3,999
(April 1997)
[Bokosi patsamba 4]
Chiŵerengero cha Ofalitsa Onse
Chiŵerengero Chathu Chapamwamba Choposa Ziŵerengero Zonse: 43,864
(October 1999)
[Bokosi patsamba 5]
Opezeka pa Chikumbutso
Chiŵerengero Chathu Chapamwamba Choposa Zonse: 125,415
(1997)