Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/02 tsamba 3-6
  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 2/02 tsamba 3-6

‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’

1 Poyamikira chinthu chabwino chimene mwalandira, kodi simusonyeza mwa khalidwe ndi zochita? Ndithudi mumatero. Ponena za ubwino ndi kukoma mtima kumene Yehova amasonyeza kwa anthu, onani zimene mtumwi Paulo anachita. Anafuula kuti: “Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.” Kodi ‘mphatso yosatheka kuneneka’ imeneyi n’chiyani? Ndiyo “chisomo [chonse] choposa cha Mulungu” chimene watisonyeza, ndipo chisomo chachikulu kuposa china chilichonse chimene wasonyeza ndicho mphatso ya Mwana wake monga dipo la machimo athu.—2 Akor. 9:14, 15; Yoh. 3:16.

2 Kodi kuyamikira kwa Paulo kunali kwa pakamwa pokha? Ayi. Anasonyeza kuyamikira kwake m’njira zambiri. Ankadera nkhaŵa kwambiri moyo wauzimu wa Akristu anzake ndipo ankafuna kuchita zimene angathe kuti awathandize kupindula kwambiri ndi kukoma mtima kwa Mulungu. Za anthu ameneŵa, Paulo anati: “Ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Ates. 2:8) Kuwonjezera pa kuthandiza anthu amene anali kale mu mpingo kuti ateteze chipulumutso chawo, Paulo sanatope kulalikira uthenga wabwino. Anayenda maulendo ambiri apamtunda ndi apanyanja kuti apeze anthu “ofuna moyo wosatha.” (Mac. 13:48, NW) Kuyamikira kochokera pansi pamtima kwa Paulo pazonse zimene Yehova anamuchitira kunamulimbikitsa ‘kukwaniritsa [“kulalikira mokwanira,” NW] mawu a Mulungu.’—Akol. 1:25.

3 Kodi kuyamikira kwathu zonse zimene Yehova watichitira sikutilimbikitsa kuthandiza mwauzimu anthu amene akufunika thandizo mu mpingo wathu? (Agal. 6:10) Ndipo kodi sikutilimbikitsa kulalikira mokwanira uthenga wabwino wa Ufumu m’gawo lathu lonse?—Mat. 24:14.

4 Nthaŵi Yosonyeza Kuyamikira: Chaka chilichonse, Chikumbutso cha imfa ya Kristu chimatipatsa mpata wapadera wosonyeza kuyamikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira. Umenewu si msonkhano chabe kapena mwambo wa chikumbutso wamba. Yesu anati: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ (Luka 22:19) Chikumbutso cha imfa ya Kristu ndi nthaŵi yolingalira kuti Yesu ndi munthu wamtundu wanji. Ndi nthaŵi yozindikira kuti panopo ndi wamoyo ndi wamphamvu, anapatsidwa ulemerero ndi ufumu chifukwa cha moyo ndi nsembe yake yokhulupirika. Mwambo umenewunso ndi nthaŵi yosonyeza kugonjera umutu wa Kristu pamene akutsogolera zochitika mumpingo wachikristu. (Akol. 1:17-20) Anthu onse a Mulungu ayenera kupezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Chaka chino Chikumbutsochi chidzachitika Lachinayi pa March 28, 2002 dzuŵa litaloŵa.

5 M’Malaŵi muno tinali ndi chiŵerengero chapamwamba choposa zina zonse m’mbuyomu cha anthu amene anapezeka pa Chikumbutso, chokwana 156,462, chifukwa cha kuyesetsa kwa anthu Chikumbutsochi chisanachitike. Kodi chiŵerengero cha chaka chino chidzakhala chotani? Zidalira ‘kugwiritsitsa ntchito ndi kuyesetsa’ kwathu pothandiza anthu ambiri kudzapezekapo.—1 Tim. 4:10.

6 Komanso, kuwonjezera pa kupezeka pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, tingawonjezere zimene timachita mu utumiki wakumunda. Mosakayikira abale ndi alongo ambiri adzachita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena iŵiri. Panthaŵi ya Chikumbutso chaka chilichonse m’zaka zisanu zapitazi, miyezi ya March mpaka May, tinkakhala ndi apainiya othandiza pafupifupi 3,558. Kodi mungasinthe zochita zanu kuti mukhale ndi mpata wochita upainiya wothandiza chaka chino? Idzakhala njira yabwino kwambiri yosonyezera kuyamikira kwanu ndi mtima wonse mphatso yachikondi imene Mulungu anapereka ya nsembe ya Kristu. Yehova adzakudalitsani monga momwe chokumana nacho ichi chikusonyezera.

7 Mlongo wina wapantchito analemba zimene anakumana nazo pamene anali kuchita upainiya wothandiza m’mwezi wa March chaka chathachi. Anati: “Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2001 unalimbikitsa tonse amene zochita zathu zinatilola kuchita upainiya wothandiza panthaŵi ya Chikumbutso. Popeza March anali ndi masiku a Loŵeruka asanu, zinagwirizana kwambiri ndi ndandanda yanga. Choncho ndinaganiza zopereka mafomu ofunsira upainiya.” Pamene amayamba mweziwo, anali ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba. Kodi anayambitsadi? Inde, analipeza akukwanitsa ola la 52 la muutumiki m’mwezi umenewo. Kodi anati chiyani? “Timapeza madalitso ambiri tikachita khama.”

8 Kodi ndi madalitso otani amene banja limapeza likachitira pamodzi upainiya? Banja lina la ana aŵiri limene linachita zimenezi mu April wachaka chatha, linapeza kuti ndi mwezi umene sadzauiŵala. Mayi anati: “Si mmene tinkasangalalira tsiku lililonse, popeza tinkachitira limodzi utumiki. Kukambirana tsiku lililonse zimene tachita mu utumiki kunapangitsa nthaŵi yachakudya chamadzulo kukhala yosangalatsa kwambiri.” Mwana wamwamuna wa m’banja limeneli anati: “Ndinasangalala kuloŵa mu utumiki wakumunda ndi bambo pakati pamlungu, popeza nthaŵi zambiri amagwira ntchito.” Bambowo anawonjezera kuti: “Monga mutu wa banja, ndinasangalala podziŵa kuti tinkagwirira pamodzi ntchito yofunika kwambiri m’nthaŵi yathu.” Kodi banja lanu lingachitire pamodzi upainiya? Bwanji osakambirana pabanja ndikuona ngati zingatheke kuti banja lanu lonse lichite upainiya wothandiza nthaŵi ya Chikumbutso imeneyi?

9 Kodi Tingapange Mwezi wa March Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse? Kumayambiriro a chaka cha 2000, Utumiki Wathu wa Ufumu unali ndi funso ili: “Kodi Tingapange Mwezi wa April Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?” Kodi yankho linali lotani? Panali ziŵerengero zapamwamba zatsopano zambiri. M’mwezi umenewu panali chiŵerengero chapamwamba choposa zina zonse cha ofalitsa, chokwana 45,068. Komanso, tinali ndi ziŵerengero zapamwamba za maphunziro a Baibulo ndi maulendo obwereza. Kodi mukukumbukira changu chimene mpingo wanu unali nacho pa zochitika zambiri zauzimu m’mwezi wapadera umenewu? Kodi chaka chino tingachite zofananazo kapena zoposerapo? Tonse titachita zinthu mogwirizana tingapange March 2002 kukhala “Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse.” Chifukwa chiyani tikuti March?

10 Pali zifukwa ziŵiri zimene zikupangitsa kuti mwezi wa March ukhale mwezi wapadera pogwira ntchito. Choyamba, Chikumbutso chidzachitika kumapeto a March, zomwe zidzatipatsa mpata waukulu kumayambiriro a mweziwu woitanira anthu ambiri ku mwambowu. Chachiŵiri, March chaka chino ali ndi mapeto a mlungu asanu, zimene zidzapatsa mpata anthu apantchito kapena apasukulu wochita upainiya wothandiza. Bwanji osakhala pansi ndi kukonza ndandanda yomwe mungakwanitse kuitsatira, mogwiritsa ntchito kalendala imene ili mu mphatika ino? Upainiya wothandiza ungakhale wosavuta kusiyana ndi mmene mukuganizira. Mwachitsanzo, kungokhala maola 8 mu utumiki wakumunda mapeto alionse a mlungu m’mweziwu, ndiye kuti mwezi wonsewo mudzafunika maola 10 okha owonjezera kuti mukwanitse maola 50.

11 Kodi akulu angachite chiyani kuti athandize mpingo wonse ‘kulalikira Mawu a Mulungu mokwanira’? Alimbikitseni pamene mukukamba nkhani pamsonkhano ndiponso pamene mukucheza nawo. Oyang’anira maphunziro a Buku a Mpingo pamodzi ndi othandizira awo angalankhule ndi aliyense m’gulu lawolo ndi kum’thandiza. Kungowalimbikitsa ndi mawu ochepa okha kapena kuwauza malingaliro othandiza n’zomwe zikufunika. (Miy. 25:11) Ambiri adzaona kuti kungosintha pang’ono zimene amachita, angasangalale ndi mwayi wotumikira monga apainiya othandiza. M’mipingo yambiri, akulu ndi atumiki otumikira ochuluka, ngati si onse, ndi akazi awo anapereka chitsanzo chabwino mwa kuchitira pamodzi upainiya nthaŵi ya Chikumbutso. Izi zalimbikitsa ofalitsa ambiri kuchitanso upainiya wothandiza. Chifukwa cha matenda kapena zovuta zina, ofalitsa ena sangathe kuchita upainiya, koma angalimbikitsidwe kusonyeza kuyamikira kwawo mwa kuchita zochuluka mu utumiki momwe angathere pamodzi ndi mpingo wonse.

12 Kuti zinthu ziyende bwino zimadalira kuti akulu akonzekere. Mlungu wonsewo misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda izichitika panthaŵi yabwino. Ngati n’kotheka, woyang’anira utumiki adzauza abale oyeneretsedwa nthaŵi ikadalipo kuti adzatsogolere misonkhano yonse ya utumiki. N’kofunika kukonzekera bwino kuti misonkhano imeneyi isapitirire mphindi 10 kapena 15, zomwe zikuphatikizapo kugaŵa gululo, kutchula gawo lokalalikiramo, ndi pemphero. (Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2001.) Ndandanda ya utumiki ya mwezi umenewo aifotokoze momveka ku mpingo ndipo aikhome pa bolodi la chidziŵitso.

13 Pakhale gawo lokwanira. Woyang’anira utumiki akumane ndi mbale wosamalira magawo kuti akonze zolalikira m’magawo amene safoledwa pafupipafupi. Lalikirani kwambiri kwa anthu amene sapezeka panyumba, lalikirani m’misewu ndi kusitolo lililonse, ndiponso chitani ulaliki wa madzulo. Ngati n’kofunika, ofalitsa ena angathandizidwe kuchita ulaliki wa patelefoni.

14 Athandizeni Kuyambanso Kutumikira: Kodi alipo amene azirala polalikira uthenga wabwino mu gawo la mpingo wanu? Oterowo akadali mbali ya mpingo ndipo akufunika thandizo. (Sal. 119:176) Popeza mapeto a dziko lakale lino ali pafupi kwambiri ndipo dziko latsopano layandikira, tili ndi zifukwa zomveka zolimbikirira kuthandiza anthu amene azirala. (Aroma 13:11, 12) Chaka chilichonse, m’zaka zisanu zapitazi, anthu oposa 731 ankavomera kuthandizidwa ndipo akhalanso achangu. Kodi tingatani kuti tithandize anthu ena ambiri kukhalanso ndi chikondi ndi chidaliro chimene anali nacho poyamba?—Aheb. 3:12-14.

15 Bungwe la akulu lidzafunika kukambirana momwe lingathandizire amene azirala m’zaka zingapo zapitazi. (Mat. 18:12-14) Mlembi aone Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa la wofalitsa aliyense ndikuona amene azirala. Yesetsani kuwathandiza mwa maulendo aubusa. Mkulu angapemphe wofalitsa amene poyamba ankacheza kwambiri ndi munthu woziralayu kuti am’thandize, kapena angapemphe ofalitsa ena. Mwina wofalitsayo ankaphunzira ndi munthu amene waziralayu ndipo angasangalale kupatsidwa mwayi wothandiza mwapadera panthaŵi imeneyi. Tikukhulupirira kuti ambiri mwa amene anazirala adzalimbikitsidwa kuyambanso kulalikira uthenga wa Mulungu. Ngati akuyenerera, palibe nthaŵi yabwino kuyamba kulalikira kuposa ya Chikumbutso.—Kuti mumve zambiri onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2000.

16 Kodi Ena Ndi Oyenera Kulalikira? Yehova akupitiriza kudalitsa anthu mwa kubweretsa “zofunika za amitundu onse.” (Hag. 2:7) Chaka chilichonse anthu ambiri amayenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa. Kodi iwo ndi ndani? Ana a Mboni za Yehova komanso ophunzira Baibulo olimbikira. Kodi timadziŵa bwanji kuti ndi oyenerera kukhala ofalitsa a uthenga wabwino?

17 Ana a Mboni za Yehova: Kwa zaka zochuluka ana ambiri akhala akupita mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi makolo awo, ngakhale kuti si ofalitsa osabatizidwa. Mwezi wa March ndi mwezi wabwino kuti akhale ofalitsa osabatizidwa. Kodi mungadziŵe bwanji ngati mwana wanuyo akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa? Buku la Olinganizidwa Kukwaniritsa Utumiki Wathu, patsamba 100 limanena kuti, ndi “pamene mwana ali wa chitsanzo chabwino m’khalidwe lake ndipo amalankhula poyera za chikhulupiriro chake pokambirana ndi ena uthenga wabwino, posonkhezereka kuchokera pansi pa mtima.” Ngati mukuona kuti mwana wanu akuyenerera, lankhulani ndi m’modzi wa akulu a mu Komiti ya Utumiki ya Mpingo.

18 Ophunzira Baibulo Oyeneretsedwa: Wophunzira Baibulo akaphunzira ndi kupezeka pa misonkhano kwa nthaŵi ndithu, angafune kukhala wofalitsa Ufumu. Ngati ndi inu amene mumachita naye phunziro, lingalirani mafunso aŵa: Kodi akupita patsogolo mogwirizana ndi msinkhu ndi maluso ake? Kodi anayamba kuuza ena chikhulupiriro chake mwamwayi? Kodi akuvala umunthu “watsopano”? (Akol. 3:10) Kodi akukwanitsa zofunika kwa ofalitsa osabatizidwa, zimene zili m’buku la Olinganizidwa, pa masamba 97-9? Ngati ndi choncho, uzani Komiti ya Utumiki ya Mpingo kuti ikonze zoti akulu aŵiri adzakumane nanu pamodzi ndi wophunzirayo. Ngati akuyenerera, akulu aŵiri aja adzamuuza kuti angayambe kulalikira poyera.

19 Bwanji Miyezi ya April ndi May? Iyinso idzakhala miyezi yapadera yochita ntchito yochuluka mu utumiki wakumunda. Ambiri amene achita upainiya wothandiza mu March angathe kuchitanso mu April ndi/kapena May. Mu April ndi May, cholinga chachikulu mu utumiki chidzakhala kugaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Amakhudza kwambiri miyoyo ya anthu amene amaŵerenga magaziniŵa. Magazini ameneŵa athandiza kwambiri kuchulukitsa anthu m’gululi kumene kwakhala kukuchitika padziko lonse. Tidzayesetsa mu April ndi May kugaŵira magazini kwa anthu ambiri. Konzani zodzagwira nawo ntchitoyi mokwanira.

20 Chifukwa cha kuchuluka kwa ntchito yolalikira imene mwakonza, kodi mukufuna kuwonjezera magazini amene mumatenga ku mpingo? M’chaka chonse cha utumiki, Loŵeruka lililonse ndi Tsiku lathu la Magazini, limene timagaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Komano, popeza anthu ambiri adzakhala akuchita utumiki waupainiya wothandiza ndipo ena tonse tidzakhala tikugaŵira magazini kwa miyezi iŵiri yathunthu, kudzakhala bwino kuwonjezera magazini amene mumalandira ku mpingo. Ngati ndi choncho, dziŵitsani mwamsanga mtumiki wa magazini mu mpingo wanu. Komanso mtumiki wa mabuku aonetsetse kuti pali mathiratiki okwanira a Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo kuti onse agwiritse ntchito.

21 Ambiri ayamikira mbali ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu yakuti “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” Kodi mukugwiritsa ntchito zimenezi mwa kuphunzira zitsanzo za ulaliki wa magazini? Bwanji mlungu uliwonse osagwiritsa ntchito nthaŵi ina ya phunziro lanu la Baibulo la banja kuyeserera zitsanzo zimenezi?

22 Gwiritsani Ntchito Mokwanira Nthaŵi ya Chikumbutso Imeneyi: Monga mtumwi Paulo, tiyeni tim’sonyeze Yehova momwe timayamikirira ‘mphatso yake yosatheka kuneneka’ mwa kutenga mbali mokwanira mu ntchito zauzimu zimene zakonzedwa panthaŵi ya Chikumbutso imeneyi. Zimenezi ndi zinthu monga (1) kupezeka pa mwambo wofunika kwambiri pachaka, wokumbukira Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, Lachinayi, pa March 28, 2002; (2) kuthandiza amene azirala kuti akhalenso ndi “chikondi [chawo] choyamba” (Chiv. 2:4; Aroma 12:11); (3) kuthandiza ana athu ndi wophunzira Baibulo aliyense amene akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa; ndi (4) kuyesetsa kuchita mokwanira ntchito yolalikira, ngakhale kuchita upainiya wothandiza mu March ngakhale miyezi inanso.—2 Tim. 4:5.

23 Tikupemphera kuchokera pansi pamtima kuti tonse tilalikire mokwanira uthenga wabwino wa Ufumu panthaŵi ya Chikumbutso imeneyi, chotero tikumasonyeza kuti timayamikira kwambiri zonse zimene Yehova watichitira.

[Bokosi patsamba 6]

Ndandanda Yanga ya Utumiki Wakumunda ya Mwezi wa March 2002

Lamlungu Lolemba Lachiŵiri Lachitatu Lachinayi Lachisanu Loŵeruka

1 2

Tsiku la Magazini

3 4 5 6 7 8 9

Tsiku la Magazini

10 11 12 13 14 15 16

Tsiku la Magazini

17 18 19 20 21 22 23

Tsiku la Magazini

24 25 26 27 28 29 30

CHIKUMBUTSO Tsiku la Magazini

DZUŴA

31 LITALOŴA

Kodi mu March mungapatule maola 50 kuti muchite upainiya wothandiza?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena