Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/03 tsamba 3-4
  • Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 2/03 tsamba 3-4

Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira

1 Pokhala “mtsogoleri ndi wolamulira,” Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti adzathe kugwira ntchito yaikulu yolalikira imene inali m’tsogolo. (Yes. 55:4; Luka 10:1-12; Mac. 1:8) Mtumwi Petro anafotokoza ntchito imene Yesu anawapatsa iwo motere: “Anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni [mokwanira, NW] kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.” (Mac. 10:42) Kodi kuchitira umboni mokwanira kumatanthauza chiyani?

2 Tikhoza kuphunzirapo zambiri pa chitsanzo cha mtumwi Paulo. Panthaŵi imene anakumana ndi akulu a mpingo wa ku Efeso, iye anawakumbutsa kuti: ‘Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba, ndi kuchitira umboni [mokwanira, NW] Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.’ Ngakhale kuti Paulo anali ndi mavuto ambiri, iye anayesetsa kulalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene akanatha kuwafikira. Iye sanakhutire ndi kungouza anthu choonadi basi, koma anayesetsa kuwauza “uphungu wonse wa Mulungu.” Kuti athe kuchita zimenezi, iye anali wokonzeka kugwira ntchito mwakhama komanso kudzimana. Iye anapitiriza kunena kuti: ‘Sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wamtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni [mokwanira, NW] Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.’—Mac. 20:20, 21, 24, 27.

3 Kodi masiku ano tingatsatire motani chitsanzo cha Paulo? (1 Akor. 11:1) Tingatero mwa kufufuza anthu oyenerera uthenga wabwino ngakhale pamene tikulimbana ndi mavuto ena m’moyo wathu, komanso mwa kuyesetsa kulalikira kwa anthu a mitundu ndi zilankhulo zonse. Tingateronso mwa kuwathandiza mwakhama anthu onse omvetsera amene tapeza. (Mat. 10:12, 13) Kuti izi zitheke, pamafunika nthaŵi, khama, komanso kuwakonda anthuwo.

4 Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza? Miyezi ya March ndi April ingakhale nthaŵi yabwino kwambiri yoti inu muchitire umboni mokwanira polembetsa upainiya wothandiza. Chaka chatha, zinali zosangalatsa bwanji kuona abale ndi alongo ochuluka akudzipereka kuchita upainiya wothandiza!

5 Mlongo wina amene ali ndi zaka 80 komanso amene amavutika kwambiri chifukwa chakuti alibe thanzi labwino anakhudzidwa kwambiri ndi chilimbikitso chimene analandira ku gulu la Yehova. Ponena za chilimbikitso chimenechi, iye analemba kuti: “Chinadzutsanso chikhumbo chimene ndakhala nacho kwa nthaŵi yaitali mu mtima mwanga, ndipo ndinaona kuti sindingachitire mwina koma kuchita upainiya wothandiza basi, ngakhale kamodzi kokha.” Mlongoyu anaganiza zochita upainiya m’mwezi wa March. Iye ananena kuti: “Choyamba, ndinakhala pansi ndi kuwerengera mtengo. Ndinakambirana nkhaniyi ndi mwana wanga wamkazi podziwa kuti anafunikira kundithandiza. Ndinadabwa poona kuti pambuyo pake nayenso walembetsa upainiya.” M’mwezi umenewo, mlongo wachikulireyu anatha maola 52 ali mu utumiki. “Nthaŵi zambiri ndikaona kuti ndayamba kutopa, ndinkapemphera kwa Yehova kuti andilimbikitse. Pamapeto pa mweziwo, ndinali wosangalala chifukwa chokhutira kwambiri ndi zimene ndinachita, ndipo ndakhala ndikumuthokoza Yehova kwambiri chifukwa chondithandiza. Ndikufuna kuti ndidzachitenso zimenezi.” Zinthu zosangalatsa zimene zinam’chitikira mlongoyu zingalimbikitsenso ena amene akufunitsitsa kuchita upainiya wothandiza ngakhale kuti alibe thanzi labwino.

6 Mbale wina amene anachotsedwa ntchito mwadzidzidzi anagwiritsa ntchito mwayi umenewo kuti achite upainiya wothandiza. M’kati mwa mweziwo, iye anadzazidwa koopsa ndi changu cholalikira, ndipo pamapeto pake anali atayambitsa phunziro latsopano la Baibulo. “Unali mwezi wapadera kwabasi!” anatero mbaleyu poganizira zimene zinam’chitikirazi. Anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya poona kuti Yehova anam’tsogolera ndi kum’thandiza. Zoonadi, Yehova anam’tsanulira madalitso ambiri mbale ameneyu chifukwa cha khama limene anachita mu utumiki, ndipo inunso adzakudalitsani chimodzimodzi.—Mal. 3:10.

7 Kwa abale ndi alongo ambiri, kuchita upainiya wothandiza si chinthu chophweka. Komabe, ngakhale kuti ali ndi udindo wambiri kuntchito ndi m’banja, komanso ali ndi mavuto osiyanasiyana pamoyo wawo, ambiri akwanitsa kuchita upainiya wothandiza. Kuchitira umboni mokwanira nthaŵi zambiri kumafuna kudzimana, komanso kumatithera nthaŵi ndi nyonga zathu zopereŵera n’kale, koma madalitso amene timalandira sangafanane ndi chinthu china chilichonse.—Miy. 10:22.

8 Miyezi ya March ndi April ndi yabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza. M’mwezi wa March muli mawikendi asanu. Pogwiritsa ntchito mawikendi ameneŵa komanso maola akumadzulo, ena opita kuntchito angathe kuchita nawo upainiya wothandiza. Kuphatikiza apo, mukhoza kulalikiranso pa maholide amene ali m’mwezi wa April. Ena mwina adzakhala ali pa holide ya kusukulu kapena kuntchito, imene ingawathandize kukwanitsa maola 50 amene akufunika. Kuti mudzathere maola 50 mu utumiki m’mwezi wa March kapena April, kodi mungagwiritse ntchito njira imodzi yochitira upainiya wothandiza mwa njira zimene zandandalikidwa m’nkhani ino? Kambiranani ndi ena njira imene mwasankha. Mwina ena mwa iwo angalimbikitsidwe kuloŵa nanu limodzi mu utumiki. Ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza m’miyezi imeneyi, khalani ndi nambala ya maola amene mukufuna kuti mukwanitse, ndipo athandizeni amene angathe kuchita upainiya. Konzekeranitu pakadali pano kuti mudzathe kuchita zambiri mu utumiki m’miyezi ya March ndi April.

9 Sonyezani Kuti Mumayamikira Chikumbutso: Chaka chilichonse pa nyengo ya Chikumbutso, kuyamikira nsembe ya dipo kumapangitsa ambiri ‘kuchita machawi’ mwa kuchita upainiya wothandiza. (Aef. 5:15, 16) Ku Malaŵi kuno, chaka chatha kunali apainiya othandiza 3,247 m’mwezi wa March ndipo 3,141 m’mwezi wa April. Zimenezi zikutanthauza kuti, m’miyezi iŵiri imeneyi, panali apainiya othandiza pafupifupi 3,194 mwezi uliwonse. Yerekezerani nambala imeneyi ndi apainiya othandiza pafupifupi 2,253 amene analipo mwezi uliwonse kwa miyezi yonse ya m’chaka cha utumiki chimenecho. Nyengo ya Chikumbutso ino tilinso ndi mwayi wapadera woti tisonyeze kuti timayamikira kuchokera pansi pa mtima nsembe ya dipo ya Kristu mwa kuchita zochuluka mu utumiki wa kumunda.

10 Pamene deti la April 16 likuyandikira, sinkhasinkhani zimene Chikumbutso chimatanthauza kwa inu. Ganizirani zinthu zimene zinachitika kutatsala nthaŵi yochepa kuti Kristu aphedwe, komanso zimene zinali kum’vutitsa maganizo ndi mtima panthaŵi imeneyi. Sinkhasinkhaninso za chimwemwe chimene chinali patsogolo pa Yesu, ndi mmene chinamuthandizira kupirira mazunzo amene anakumana nawo. Ganizirani za udindo umene Yesu ali nawo pakadali pano monga Mutu wa Mpingo, woyang’anira ntchito yolalikira ndi yopanga ophunzira. (1 Akor. 11:3; Aheb. 12:2; Chiv. 14:14-16) Ndiyeno onetsani kuyamikira kwanu pa zonse zimene Kristu wakuchitirani mwa kuchita nawo ntchito yolalikira yochuluka monga momwe mungathere.

11 Limbikitsani Ena Kuchitira Umboni Mokwanira: Mwa kuchita nawo upainiya wothandiza, akulu ndi atumiki otumikira amakhala ndi mpata wabwino wolimbikitsira ena. Pogwira ntchito limodzi ndi abale mu utumiki wa kumunda komanso pochita maulendo aubusa, amakhala ndi mwayi wabwino woti athe kuwalimbikitsa abaleŵa kuchita nawo ntchito yapadera imeneyi monga momwe angathere. Tiyeni tonse tiiganizire nkhani imeneyi ndi kuitchula m’pemphero, kuti pamodzi, tithe kulimbikitsana kuchitira umboni mokwanira.

12 Ngakhale kuti akulu onse ndi atumiki otumikira adzagwira ntchito limodzi ndi mpingo pochita zowonjezereka mu miyezi ya March ndi April, woyang’anira utumiki makamaka ndi amene ayenera kuchita chidwi ndi zonse zokhudza kuyendetsa bwino ntchito yolalikira m’miyezi imeneyi. Ayenera kupeza malo abwino, masiku abwino, komanso nthaŵi yabwino yochitira misonkhano yoloŵera m’munda. Zimenezi zikhale zokomera abale ambiri, ndipo zizilengezedwa ku mpingo pafupipafupi. Mukhoza kukonza zoti anthu aziloŵa m’munda nthaŵi zingapo patsiku, kuti aliyense akhale ndi mwayi wochita nawo ulaliki wosiyanasiyana. Mungakalalikire ku malo amalonda, mumsewu, kunyumba ndi nyumba, kapena kuchita maulendo obwereza, ndi kulalikira pa telefoni. Chinanso, woyang’anira utumikiyu ayenera kuonetsetsa kuti mpingo uli ndi mabuku, magazini komanso gawo lokwanira m’miyezi yonseyi.

13 M’mwezi wa March tidzagaŵira buku la Chidziŵitso ndi cholinga chofuna kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 muli malangizo abwino osonyeza mmene tingagaŵire buku la Chidziŵitso. M’mwezi wa April tidzagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Gwiritsani ntchito njira zimene zili pa danga lakuti “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” Aliyense aziyesetsa kukonzekera bwino kuti athe kuchitira umboni mokwanira.

14 Ndife anthu amwayi kwambiri chifukwa chogwira ntchito motsogozedwa ndi Mutu wa Mpingo, Kristu Yesu, komanso chifukwa cha mwayi wapadera umene tili nawo wolalikira uthenga wabwino kwa ena. Pamene miyezi ya March ndi April ikuyandikira, tiyeni tidzayesenso kuipanga kukhala miyezi yathu yabwino koposa yonse pamene tikumvera lamulo la Yesu loti tilalikire ndi kuchitira umboni mokwanira.

[Bokosi patsamba 4]

Njira Zosiyanasiyana Zochitira Upainiya Wothandiza M’miyezi ya March ndi April 2003

Tsiku Maola

Lolemba 1 2 ​— —​ 2 ​—

Lachiŵiri 1 ​— 3 —​ ​— —​

Lachitatu 1 2 ​— 5 —​ ​—

Lachinayi 1 ​— 3 —​ ​— —​

Lachisanu 1 2 ​— —​ ​— —​

Loŵeruka 5 4 3 5 6 7

Lamlungu 2 2 3 2 2 3

March 56 56 54 55 50 50

April 50 50 51 53 ​— —​

Kodi mungagwiritse ntchito imodzi mwa njira izi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena