Thandizo la Panthaŵi Yake
1 Pamene mtumwi Petro anazindikira kuti okhulupirira anzake akufunikira kulimbikitsidwa, zinamukhudza kwambiri ndipo anawakumbutsa ndi kuwalimbikitsa mwachikondi. (2 Pet. 1:12, 13; 3:1) Analimbikitsa “iwo amene adalandira chikhulupiriro” kuti apitirize kukulitsa makhalidwe awo auzimu ndipo adawakumbutsa kuti “musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Pet. 1:1, 5-8) Cholinga cha Petro chinali kuwathandiza kuchita zotheka kuti maitanidwe ndi masankhulidwe awo ochokera kwa Yehova akhale otsimikizirika kuti ‘apezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chirema.’ (2 Pet. 1:10, 11; 3:14) Limeneli linali thandizo la panthaŵi yake kwa ambiri a iwo.
2 Masiku ano, oyang’anira achikristu amatideranso nkhaŵa anthu a Mulungufe ngati mmene anachitira Petro. Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, atumiki ambiri a Yehova akulimbana ndi mavuto osiyanasiyana. (2 Tim. 3:1) Chifukwa cha mavuto osatherapo a zachuma, a m’banja komanso a m’moyo, ena amamva ngati mmene anamvera Davide. Iye anati: “Zoipa zosaŵerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.” (Sal. 40:12) Mavuto ameneŵa akhoza kukula koopsa mpaka kufika poti anthu ameneŵa angayambe kunyalanyaza zinthu zauzimu zofunika, ndiponso angaleke kuchita nawo utumiki wachikristu. Komabe, ngakhale ali ndi mavuto otere, iwo ‘sanaiwale malamulo a [Yehova].’ (Sal. 119:176) Ino ndi nthaŵi yabwino yoti akulu apereke thandizo lofunikira kwambiri kwa anthu ameneŵa.—Yes. 32:1, 2.
3 Kuti athe kuchita zimenezi, akulu alimbikitsidwa kuti ayesetse kwambiri kuthandiza abale ndi alongo amene pakadali pano anasiya kuchita nawo ntchito yolalikira. Ntchito imeneyi yagundika kale, ndipo ipitirira mpaka mwezi wonse wa March. Oyang’anira maphunziro a buku a mpingo akupemphedwa kuyendera anthu amene anasiya kuloŵa m’munda ndi kukawalimbikitsa mwauzimu ndi cholinga choti ayambenso kuloŵa nawo m’munda ndi mpingo. Ngati kuli kofunika, angakonze zoti wina achite naye munthuyo phunziro la Baibulo. Abale ndi alongo ena angapemphedwe kuti athandizepo. Ngati mwapemphedwa kuti muchite zimenezi, mungamuthandizedi munthu amene anasiya kuloŵa m’mundayu, makamaka ngati mukupereka thandizo lanu mwachifundo komanso momvetsetsa.
4 Zimakhaladi zinthu zosangalatsa kwambiri pamene wina ayambiranso ntchito yolalikira limodzi ndi mpingo. (Luka 15:6) Pamene tikuyesetsa kulimbikitsa anthu amene anasiya kuloŵa m’munda, tidzakhala tikulankhula “mawu oyenera a panthaŵi yake”—Miy. 25:11.