Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/07 tsamba 8
  • Musaiwale Ofooka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musaiwale Ofooka
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • “Bwererani Kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Athandizeni Kubwerera Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 2/07 tsamba 8

Musaiwale Ofooka

1. N’chifukwa chiyani timapita kukalimbikitsa anthu amene anafooka?

1 Kodi mukudziwa munthu wina aliyense amene anafooka? Munthuyo mwina anasiya kusonkhana ndi mpingo ndipo anatengeka pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro. Mwina mungakumane ndi munthu woteroyo pamene mukulalikira khomo ndi khomo. Tiyenera kukumbukira kuti munthuyo adakali m’bale wathu wauzimu. Tikufuna kumutsimikizira kuti timam’konda ndiponso kum’thandiza kuti abwerere ku mpingo komanso ‘kwa m’busa ndi woyang’anira miyoyo yathu.’—1 Pet. 2:25.

2. Kodi tingalimbikitse bwanji munthu wofooka?

2 Asonyezeni Chidwi: Kuimba telefoni kapena kukamuona kwa nthawi yochepa kungatsimikizire munthu amene anafooka kuti timam’kumbukirabe. Koma kodi tingamuuze chiyani? Kungomuuza munthuyo kuti timamuganizira kungakhale kolimbikitsa. Kambiranani naye zinthu zabwino ndiponso zolimbikitsa. (Afil. 4:8) Tingatchule mfundo imene inatisangalatsa pa msonkhano wina waposachedwapa. Tingamuitanirenso ku msonkhano wa mpingo kapena msonkhano waukulu umene ukubwera m’tsogolo ndi kumuuza kuti tidzam’sungira malo okhala kapena kum’thandiza mayendedwe.

3. Kodi zinayenda bwanji kuti mlongo wina ayambenso kulimbikira?

3 M’gawo lina wofalitsa anapeza mlongo wina amene anakhala wofooka kwa zaka zoposa 20. Ngakhale kuti mlongo wofookayo sankafuna kuvomera phunziro la Baibulo, wofalitsayo anapitirizabe kumuyendera, ndi kumam’siyira magazini atsopano. Pambuyo pa msonkhano wachigawo, wofalitsayo anakambirana ndi mlongo wofookayo zina mwa mfundo zikuluzikulu za pamsonkhano umenewo, ndipo pamapeto pake anayambanso kulimbikira.

4. Tingachitenji ndi munthu amene wayambiranso kubwera ku misonkhano?

4 Wina Akabwerera: M’bale amene anafooka akayambanso kubwera ku misonkhano, kodi tiyenera kuchita naye motani? Kodi Yesu anatani nawo ophunzira ake chifukwa cha zomwe iwo anachita panthawi inayake pom’siya yekha? Mwachikondi, iye anawatchula kuti “abale” ake ndipo anasonyeza kuti amawakhulupirira. Iye anawapatsanso ntchito yofunika. (Mat. 28:10, 18, 19) Patangopita nthawi yochepa, iwo anatanganidwa ndi kulalikira uthenga wabwino “mwakhama.”—Mac. 5:42.

5. Tchulani zinthu zimene tiyenera kuuza akulu zokhudza munthu wofooka.

5 Tisanapemphe kuti tiziphunzira Baibulo ndi munthu wina amene anafooka, kapena tisanapemphe m’bale amene wakhala wofooka kwa nthawi yaitali kuti apite nafe muutumiki, tiyenera kufunsa kaye malangizo kwa akulu. Ngati takumana ndi wofalitsa wofooka m’gawo lathu, tiyenera kudziwitsa akulu kuti athandizepo.

6. Kodi n’chisangalalo chotani chimene tingakhale nacho pothandiza anthu amene anafooka?

6 Baibulo limasonyeza mosapita m’mbali kuti, anthu amene adzapulumuke ndi okhawo omwe adzapirire mpaka mapeto. (Mat. 24:13) Choncho, dziwani anthu amene anakhumudwa n’kuyamba kutengeka pang’onopang’ono mpaka kusiya chikhulupiriro. Ngati timatsanzira Yehova pokhala oleza mtima ndi anthu amenewa n’kuwasonyeza chikondi mwa kuchita zinthu zowaganizira, tingasangalale kuwaona akuyambiranso utumiki wawo wopatulika limodzi nafe.—Luka 15:4-10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena