Bokosi la Mafunso
◼ Kodi nkoyenererabe kumachita phunziro la Baibulo la panyumba ndi mbale kapena mlongo wofooka molangizidwa ndi mmodzi wa Komiti Yautumiki Yampingo?
Akulu ali ndi ntchito yoŵeta mpingo, kuphatikizapo aliyense amene wafooka. Amachezera anthu oterowo ndi kuona chithandizo chimene afunikira kupatsidwa. Pamene kuli koyenera, zimenezi zingaphatikizepo kupatsa wofookayo mapindu a kukhala ndi phunziro la Baibulo. Buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, patsamba 103, limalongosola kuti Komiti Yautumiki Yampingo ingasankhe amene angapindule ndi makonzedwe ameneŵa.
Woyang’anira utumiki amaona amene angapereke chithandizocho moyenerera kwambiri, nkhani zimene ziyenera kuphunziridwa, ndiponso buku limene lingakhale lothandiza kwambiri. Mwina munthu amene anali kuphunzira naye poyamba kapena munthu amene wazoloŵerana naye ndi amene amamlemekeza angakhale munthu woyenera kuthandiza. Mlongo wokhoza ndi wofikapo angapemphedwe kuthandiza mlongo wofooka. Kaŵirikaŵiri sikudzakhala koyenerera kuti wofalitsa wina atsagane ndi munthu amene anagaŵiridwa kuchititsa phunzirolo. Pamene wagaŵiridwa, wofalitsa amene akuchititsa phunzirolo angaŵerengere nthaŵi, ulendo wobwereza, ndi phunziro.—Onani Utumiki Wathu Waufumu wa November 1987 masamba 1-2.
Popeza kuti wophunzirayo ndi munthu wobatizidwa, kaŵirikaŵiri phunzirolo silifunikira kuchitidwa kwanthaŵi yaitali. Cholinga ndi kuthandiza wofookayo kuyambanso kufika pamisonkhano yonse yampingo ndi kukhala wofalitsa wokhazikika wa uthenga wabwino. Woyang’anira utumiki adzayang’anira mmene maphunziro oterowo akupitira patsogolo. Chotulukapo cha chithandizo chachikondi chimenechi nchakuti abale ndi alongo ameneŵa akhale okhoza kusenza katundu wa iwo eni wa udindo wawo kwa Yehova ndi kukhala “ozika mizu ndi otsendereka” zolimba m’choonadi.—Aef. 3:17; Agal. 6:5.