Bokosi la Mafunso
◼ Kodi munthu amene wakhala wozilala kwa nthaŵi yaitali angathandizidwe motani kuti ayenererenso kukhala wofalitsa uthenga wabwino?
Pamene munthu wozilala aonetsa umboni wakuti ali wofunitsitsa moona mtima kuyambanso kutumikira Yehova, imakhala nkhani yosangalatsa kwambiri. (Luka 15:4-6) Mwachidziŵikire, munthuyo analola kutsutsa kwa ena kapena zosangalatsa za moyo kusokoneza phunziro laumwini, kufika pamisonkhano, ndi kutenga mbali mu utumiki wakumunda. Kodi tingathandize motani kuti iyeyo ayambenso kupita patsogolo mwauzimu?
Tonse tiyenera kuchitapo kanthu potsimikizira woteroyo kuti tili naye ndi chikondi chenicheni chachikristu. Akulu adzafufuza mwachangu kuti adziŵe zosoŵa zake zauzimu. (Yak. 5:14, 15) Ngati kuzilalako kunali kwa nthaŵi yaifupi, angangofunikira chithandizo cha wofalitsa wofikapo kuti am’yambitsenso kuloŵa mu utumiki wakumunda. Komabe, ngati wozilalayo wakhala asakusonkhana ndi mpingo kwa nthaŵi yaitali, padzafunikira chithandizo chokulirapo. Kuti akulitse chikhulupiriro ndi chiyamikiro, kungakhale bwino kupanga naye phunziro la Baibulo m’buku loyenerera. Zikakhala choncho, woyang’anira utumiki adzapempha wofalitsa wofikapo kuti azichititsa phunzirolo. (Aheb. 5:12-14; onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 1998.) Ngati mukudziŵa munthu wina wofunikira chithandizo choterocho, dziŵitsani woyang’anira utumiki mumpingo wanu.
Musanapemphe munthu amene anazilala kale kwambiri kuti ayambenso kuloŵa mu utumiki, ndi bwino kuti akulu aŵiri ayambe akumana naye kuti am’pende ndi kuona ngati ali woyenerera kukhala wofalitsa Ufumu. Iwo adzatsatira dongosolo lofanana ndi lija logwiritsa ntchito popenda atsopano ofuna kukhala ofalitsa uthenga wabwino. (Onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, tsamba 17.) Wozilalayo ayenera kukhala ndi chikhumbo chochokera pansi pamtima cholalikira uthenga wabwino kwa ena. Afunikiranso kukwaniritsa ziyeneretso zoyambirira zofotokozedwa patsamba 98-9 m’buku la Uminisitala Wathu ndipo ayenera kumafika pamisonkhano mokhazikika.
Kukhala ndi dongosolo labwino lauzimu kungathandize kwambiri wobwererayo kuti alimbitse ndi kuteteza unansi wake wamtengo wapatali ndi Yehova ndi kuyendabe panjira ya ku moyo wosatha. (Mat. 7:14; Aheb. 10:23-25) Kuikirapo “changu chonse” ndi kukulitsa mikhalidwe yachikristu yokhalitsa kudzam’teteza kuti asadzakhalenso wophunzira wachikristu ‘waulesi kapena wopanda zipatso.’—2 Pet. 1:5-8.