Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/07 tsamba 3-5
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • ‘Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 2/07 tsamba 3-5

Lengezani Ulemerero wa Yehova

1. N’chifukwa chiyani timalengeza za ukulu ndi ulemerero wa Yehova?

1 “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.” (1 Mbiri 29:11) Kodi timasonyeza motani kuti timakonda ndi kuyamikira Yehova? Timachita zimenezi ‘polengeza zabwino zopambana za amene anatiitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Pet. 2:9) Sitingaleke kuuza ena za Mulungu wathu wamkulu! Tikhala ndi mpata wapadera kwambiri wolengeza ulemerero wa Yehova m’miyezi ya March, April, ndi May.

2. Kodi ndi ntchito yapadera yotani imene yakonzedwa pofuna kulengeza za Chikumbutso, ndipo ndani angachite nawo ntchitoyi?

2 Ntchito Yapadera Yolengeza za Chikumbutso: Lolemba, pa April 2, tidzalengeza ulemerero wa Yehova pochita mwambo wa Mgonero wa Ambuye. Kuyambira pa March 17 mpaka pa April 2, tidzayamba kugawira padziko lonse lapansi kapepala kapadera koitanira anthu ku mwambo wofunika kwambiriwu. Tikulimbikitsa aliyense kudzachita nawo ntchitoyi mmene angathere. Imeneyi idzakhala nthawi yabwino kwambiri kwa ophunzira Baibulo kuyamba kufalitsa uthenga wabwino ngati ali oyenerera. Ngati muli ndi ophunzira Baibulo kapena ana amene angayenerere, uzani akulu.

3. Kodi tinganene chiyani poitanira anthu ku Chikumbutso?

3 Ntchito imeneyi idzakhala yofanana ndi imene tinachita polengeza za Msonkhano wa Chigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Mipingo idzalandira timapepala tokwanira moti wofalitsa aliyense adzalandira timapepala 40. Pogawira timapepalati, osachulutsa zonena. Mwina mungangonena kuti: “Kapepalaka n’kokuitanirani ku mwambo wofunikira kwambiri wa pachaka. Tidzakulandirani ndi manja awiri. Zonse zalembedwa pa kapepalaka.” Komabe, ngati mwininyumbayo ali ndi mafunso, muyankheni. Mungagwiritse ntchito nkhani zakumapeto m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani zomwe zayambira pa tsamba 206, zonena za Chikumbutso. Loweruka ndi Lamlungu, tidzapitiriza kugawira magazini a mwezi umenewo limodzi ndi kapepalaka. Lembani mayina a anthu onse amene asonyeza chidwi ndipo konzani zodzabwererakonso.

4. Kodi tidzagawira bwanji timapepala tapadera toitanira anthu ku Chikumbutso?

4 Ngati zingatheke, tizidzapereka pamanja timapepalati kwa mwininyumba aliyense. Motero, lembani anthu onse amene simunawapeze pa khomo pawo, ndipo mudzapitenso. Ofalitsa a m’mipingo imene yatsala ndi timapepala tambiri angathe kusiya timapepalati pakhomo lililonse limene sanapezepo anthu ndipo atero kutatsala mlungu umodzi kuti Chikumbutso chichitike, koma asachite zimenezi mlungu umenewu usanafike. Onetsetsani kuti mwagawira timapepalati kwa anthu amene mumawayendera pa maulendo obwereza, amene mumaphunzira nawo Baibulo, abale anu, anzanu a kuntchito, anthu amene mwayandikana nawo, ndiponso anthu ena onse owadziwa.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamba panopa kukonzekera kudzachita upainiya wothandiza?

5 Upainiya Wothandiza: Kodi mungalengeze ulemerero wa Yehova mokwanira bwino pochita upainiya wothandiza m’miyezi ya March, April, ndi May? Kuti muchite zimenezi, mosakayikira mufunika kusintha zinthu zina ndi zina pa zochita zanu zatsiku ndi tsiku. (Aef. 5:15-17) Khulupirirani kuti ngati muchita zonse zomwe mungathe kuti muonjezere utumiki wanu kwa Yehova, mudzakhala ndi chimwemwe ndiponso Yehova adzakupatsani madalitso. (Miy. 10:22) Popeza nyengo ya Chikumbutso ikuyandikira, tiyenera kuyamba panopa kukonzekera.—Miy. 21:5.

6. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zomwe anachita mlongo wa zaka 90 yemwe anachita upainiya wothandiza chaka chatha?

6 Chaka chatha, mlongo wina wa zaka 90 anasangalala ndi mwayi wochita nawo upainiya wothandiza. Mlongoyu anati: “Ngakhale kuti ndimakonda kwambiri kulima ndipo ndinkafuna kuyamba kudzala mbewu, ndinazindikira kufunika koyamba kaye kuchita zinthu zofunika kwambiri. Pofuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo, ndinasankha kuchita upainiya wothandiza mu March.” Kodi mlongoyu anadalitsidwa chifukwa cha khama lakeli? “Ndimaona kuti ndine woyanjana kwambiri ndi anthu a mumpingo, ndipo zimenezi zandichititsa kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova,” akutero mlongoyu. Kodi ifenso sitingaone bwinobwino zinthu pamoyo wathu n’kusintha zina ndi zina kuti tiziika zinthu zofunika kwambiri patsogolo monga anachitira mlongoyu?

7. Kodi kuchita upainiya wothandiza n’kovuta?

7 Kuchita upainiya wothandiza n’kumakwanitsa maola 50 si kovuta monga mmene mungaganizire. Pempherani kwa Yehova kuti muthe kuonanso bwinobwino zochita zanu za tsiku ndi tsiku. Kenaka konzani ndandanda yosonyeza mmene mungachitire zinthuzo, ndipo lembani ndandandayo pa kalendala yanu yosonyeza zinthu zauzimu zimene mukufuna kumachita tsiku ndi tsiku. Inuyo mumadzidziwa nokha bwino kwambiri. Ngati thupi lanu lili lofooka pazifukwa zosiyanasiyana monga matenda, mwina mungachite bwino kumangolalikira kwa maola ocheperapo tsiku lililonse. Ngati mumagwira ntchito yolembedwa kapena muli pa sukulu, mungakwanitse kuchita upainiya wothandizawu, pomalalikira madzulo kapenanso Loweruka ndi Lamlungu.

8. N’chiyani chimene chinathandiza mwamuna wina ndi mkazi wake kuchita upainiya wothandiza?

8 Anthu ambiri akwanitsa kuchitira pamodzi upainiya wothandiza ndi banja lawo. M’zaka za m’mbuyomu, mwamuna wina ndi mkazi wake ankazengereza kulembetsa upainiyawu popeza ankaona kuti sangakwanitse chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Kodi iwo anatani ndi nkhaniyi? “Tinapemphera kwa Yehova kuti atithandize kukwaniritsa zimene takhala tikuzilakalaka kwa nthawi yaitalizi.” Kenako atakonzekera bwinobwino, iwo anakwanitsa kuchita upainiyawu. Ndiyeno anati: “Zinali zosangalatsa. Tinadalitsidwa kwambiri zedi. Ndipo tikukupemphani kuti nanunso muyese kuchita utumiki umenewu. Ngati ife tinakwanitsa, inunso mungakwanitse.”

9. Kodi mungachite chiyani paphunziro lanu la banja lotsatira pokonzekera miyezi yapadera yomwe ikubwerayi?

9 Paphunziro lanu la banja lotsatira, mungapatule nthawi yoti mukambirane mmene mungaonjezerere utumiki wanu m’miyezi ikubwerayi. Ngakhale zitakhala zosatheka kuti nonse m’banjamo muchite upainiya wothandiza, mwina munthu mmodzi angathe kutero. Zimenezi zingatheke ndi thandizo komanso mgwirizano wa anthu ena onse m’banjamo. Ngati zimenezi sizingatheke, banja lonse lingagwirizane kuti lizithera nthawi yaitali mu utumiki m’miyezi yapadera imeneyi.

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuuza ena za cholinga chathu chochita upainiya wothandiza m’nyengo ya Chikumbutso?

10 Thandizanani: Mukamalimbikira kwambiri utumiki, mumalimbikitsanso ena. Mukamacheza ndi ena, lankhulani za cholinga chanu chofuna kuchita upainiya wothandiza. Zimenezi zingalimbikitse ena kuti nawonso afunsire upainiyawu. Kuonjezera pamenepa, anthu amene anachitapo upainiyawu m’mbuyomu angakuthandizeni maganizo kuti mukonze zinthu bwino pamoyo wanu ndiponso mukhale ndi ndandanda yabwino imene ingakuthandizeni kuti mukwanitse upainiyawu. (Miy. 15:22) Ngati mungakwanitse kuchita upainiya wothandiza, bwanji osapempha wofalitsa wina, makamaka amenenso angakwanitse, kuti muchitire pamodzi utumiki wosangalatsawu?

11. Kodi akulu angathandize bwanji anthu ena kuti adzachite upainiya wothandiza m’miyezi ikubwerayi?

11 Akulu ambiri amakonzekera kudzachita nawo utumiki wapaderawu. (Aheb. 13:7) Zimenezitu zimalimbikitsa mpingo kwabasi! Akulu amalimbikitsanso ena mwa zimene amalankhula akamacheza ndi anthu. Kungolankhula mwachikondi mawu olimbikitsa ochepa chabe, kapena kunena mfundo zothandiza, kungachititse ena kuyamba upainiya wothandiza. Woyang’anira utumiki adzakonza misonkhano ina yowonjezera, yokonzekera utumiki wa kumunda. Misonkhano imeneyi idzathandiza kuti aliyense azilalikira nawo mu ulaliki wa kagulu, ngakhale madzulo anthu ataweruka kuntchito kapena kusukulu. Akulu nthawi zonse azilengeza misonkhano imeneyi kumpingo. Woyang’anira utumikiyo azidzaonesetsanso kuti ofalitsa onse ali ndi gawo lolalikiramo lokwanira bwino ndiponso mabuku okwanira.

12. Ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza, kodi ndi zinthu zotani zimene mungakwanitsebe kuchita?

12 Ngakhale ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza chifukwa cha zovuta zina, mukhozabe kulimbikitsa anthu amene alembetsa upainiyawu ndiponso kuwapempherera. (Miy. 25:11; Akol. 4:12) Mwina mungakonze zowonjezera tsiku limodzi m’kati mwa mlungu kuti muzichita utumiki pamodzi ndi apainiya. Kapenanso mukhoza kumathera nthawi yaitali mu utumiki kusiyana ndi mmene mumachitira masiku onse.

13. Kodi pali cholinga chotani chimene chakhazikitsidwa m’Malawi muno, ndipo mpingo wanu ungathandize motani kuti cholinga chimenechi chikwaniritsidwe?

13 Cholinga Chokhala ndi Apainiya Othandiza 5,000 mu April: Chiwerengero chapamwamba kwambiri cha apainiya othandiza m’Malawi muno chinali 3,747, m’mwezi wa April, m’chaka cha 2006. Choncho, tili ndi cholinga chotheka kuchikwaniritsa chodzakhala ndi apainiya othandiza 5,000 m’mwezi wa April ukubwerawu. Tikhoza kukwaniritsa cholinga chimenechi ngati m’mipingo yonse, wofalitsa mmodzi pa ofalitsa 13 aliwonse atachita nawo upainiya wothandiza. Ndipotu m’mipingo ina muli ofalitsa ochuluka amene angathe bwinobwino kuchita upainiyawu. Choncho mipingo yambiri ingakwaniritse cholinga chimenechi mosavuta. Ngati zitatero, tangoganizirani chisangalalo ndiponso changu chimene chingakhalepo mumpingo mwanu komanso mmene zimenezi zingathandizire m’gawo lanu.

14. N’chifukwa chiyani mwezi wa April uli mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza?

14 N’chifukwa chiyani mwezi wa April uli wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza? Chifukwa choti Chikumbutso chidzachitika ku mayambiriro kwa mweziwu, ndipo zimenezi zidzatipatsa mpata wabwino wopanga maulendo obwereza kwa anthu amene anapezeka pa Chikumbutso. Tizidzagawira magazini, n’cholinga chogawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa ulendo obwereza n’kuyambitsa phunziro la Baibulo. Choncho, kuchita upainiya wothandiza m’mwezi wa April kudzatipatsa mpata woyambitsa maphunziro a Baibulo. Kuwonjezera apo, mwezi wa April uli ndi masiku a Lamlungu asanu ndiponso tsiku limodzi la holide. Kwa anthu amene amagwira ntchito zolembedwa ndiponso amene ali pa sukulu, zimenezi n’zothandiza kuti alembetse upainiyawu.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita changu panopa pamene tikuyandikira nyengo ya Chikumbutso?

15 Nyengo iliyonse ya Chikumbutso ikadutsa, timakhala titasuntha ndi chaka chimodzi kuyandikira kumapeto kwenikweni kwa dongosolo lino la zinthu. Tatsala ndi nthawi yochepa kwambiri youza anthu ena za Mulungu wathu wamkulu. (1 Akor. 7:29) Uwu ndi mwayi wapadera kwambiri wotamanda Atate wathu wa kumwamba. Ndipotu nyengo ya Chikumbutsoyi ikangodutsa, n’zosatheka kuti mwayiwu ubwererenso. Tiyeni tikonzekere panopa kuti tichite zonse zimene tingathe m’miyezi ya March, April, ndi May kuti tidzalengeze ulemerero wa Yehova!

[Bokosi patsamba 4]

Kodi Tingakhale ndi Apainiya Othandiza 5,000 M’mwezi wa April?

◼ Onaninso bwino zochita zanu za tsiku ndi tsiku kuti muziika patsogolo zinthu zofunika kwambiri

◼ Kambiranani cholingachi pamodzi ndi banja lanu

◼ Uzani ena zolinga zanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena