‘Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino’
1. Kodi ndi uthenga wabwino wotani umene tiyenera kuuza ena?
1 Tili ndi mwayi ‘wochitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu,’ m’dziko limene uthenga wabwino ndi wosowa. (Mac. 20:24) Uthenga wabwino umenewu umaphatikizapo kuuza anthu kuti posachedwapa ‘masiku otsirizawa’ akadzatha, padzabwera dziko latsopano lolungama la Yehova. M’dziko limenelo zinthu ‘zakale [zidzakhala] zitapita.’ (2 Tim. 3:1-5; Chiv. 21:4) Sikudzakhalanso matenda. (Yes. 33:24) Achibale ndi anzathu amene anafa adzatuluka m’manda achikumbutso. (Yoh. 5:28, 29) Dziko lonse lapansili lidzakhala paradaiso wokongola. (Yes. 65:21-23) Izi n’zinthu zochepa chabe za muuthenga wabwino zimene tiyenera kuuza anthu ena.
2. N’chifukwa chiyani nyengo ya Chikumbutso imatipatsa mwayi waukulu kwambiri wochitira umboni uthenga wabwino?
2 M’miyezi ya March, April ndi May tidzakhala ndi mwayi waukulu kwambiri wolalikira uthenga wabwino. M’madera ambiri a dziko lapansi nyengo imakhala yabwino kwambiri m’miyezi imeneyi moti munthu atha kukhala nthawi yaitali muutumiki. Komanso, mwambo wa Chikumbutso womwe ndi wofunika kwambiri pachaka, udzachitika padziko lonse Loweruka pa March 22, dzuwa litalowa. Tsopano ndi nthawi yoti tiyambe kukonzekera kuchita zambiri muutumiki wathu.
3. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zambiri muutumiki monga banja?
3 Upainiya Wothandiza: Kodi mungalinganize nthawi yanu kuti mudzachite upainiya wothandiza mwezi umodzi, miyezi iwiri, kapena yonse itatu? Bwanji osakambirana za nkhani imeneyi paphunziro lanu lotsatira labanja? Ngati banja litagwirizana, munthu mmodzi kapena angapo m’banjamo angachite upainiya wothandiza. (Miy. 15:22) Tchulani za nkhaniyi m’pemphero ndi kuona mmene Yehova angadalitsire khama lanu. (Miy. 16:3) Ngati palibe amene angachite upainiya wothandiza m’banjamo, aliyense angakhale ndi cholinga chochita zambiri muutumiki poyenda limodzi ndi anthu amene akuchita upainiya.
4. Ngati ndife apantchito, kodi tingapeze bwanji nthawi yochita upainiya wothandiza?
4 Ngati muli pantchito, mungathe kuchita upainiya mwa kulinganiza bwino nthawi yanu. Mwina mungamalalikire panthawi yopuma masana. Kapena mungapemphe gawo lakufupi ndi kunyumba kwanu kapena kuntchito kwanu ndi kumalalikira kwa ola limodzi kapena kuposerapo musanapite kuntchito kapena mutaweruka. Mwina mungapeze nthawi yambiri mwa kusunthira ku mwezi wa m’tsogolo zochita zina zosafunikira kwenikweni ndiponso mwa kulalikira Loweruka ndi Lamlungu tsiku lonse. Ena amatenga tchuthi cha tsiku limodzi kapena masiku awiri n’cholinga choti achite utumiki wakumunda.
5. Kodi mungathandize bwanji anthu okalamba kapena athanzi lofooka kuti achite upainiya?
5 Ngati ndinu wokalamba kapena wathanzi lofooka, mungathe kuchita upainiya wothandiza mwa kulowa mu utumiki nthawi yochepa tsiku lililonse. Pemphani Yehova kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Mlongo wina anakwanitsa kuchita upainiya wothandiza ali ndi zaka 106. Mothandizidwa ndi achibale ake a Mboni ndiponso ena mumpingo, iye ankalalikira nyumba ndi nyumba, ankapanga maulendo obwereza, ankapita ku maphunziro a Baibulo ndiponso kuchita mbali zina za utumiki. Iye anathandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu 10. Mlongoyu anati: “Ndikaganizira za mwayi waukulu womwe ndinali nawo wochita upainiya wothandiza, mtima wanga umadzala ndi chikondi komanso chiyamikiro kwa Yehova, Mwana wake, ndi gulu Lake lachikondi. Ndikunena mochokera pansi pamtima kuti ‘zikomo kwambiri Yehova.’”
6. Kodi zingatheke bwanji kuti achinyamata obatizidwa omwe adakali pa sukulu achite upainiya?
6 Ngati ndinu wachinyamata wobatizidwa ndipo mudakali pa sukulu, nanunso mungathe kulembetsa upainiya wothandiza. Mofanana ndi anthu apantchito, nanunso mungamalalikire nthawi yaitali Loweruka ndi Lamlungu. Mwina nanunso mungalowe m’munda ola limodzi kapena kuposerapo mukaweruka ku sukulu masiku ena. Kodi mudzakhala ndi tchuthi chilichonse chomwe mungagwiritse ntchito muutumiki? Ngati mukufuna kuchita upainiya wothandiza, lankhulani ndi makolo anu za nkhani imeneyi.
7. Kodi akulu angatani pofuna kulimbikitsa mpingo kuchita utumiki panyengo ya Chikumbutso?
7 Muzilimbikitsa Ena: Chitsanzo chabwino chimene akulu angasonyeze chingalimbikitse kwambiri mpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Iwo angakonze zoti pazikhala misonkhano yowonjezera yokonzekera utumiki wakumunda kaamba ka amene akufuna kulowa m’munda m’mawa kapena akaweruka ku sukulu kapenanso ku ntchito. Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti pali ofalitsa oyenerera oti azichititsa misonkhanoyo. Ayenera kuonetsetsanso kuti pali gawo lokwanira komanso mabuku ndi magazini okwanira ogwiritsa ntchito m’miyezi imeneyi.
8. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitika pa mpingo wina?
8 Pampingo wina, akulu anayamba kulimbikitsa ofalitsa kulembetsa upainiya wothandiza kudakali miyezi yambiri. Mlungu uliwonse ankadziwitsa mpingo chiwerengero cha ofalitsa amene avomerezedwa kuchita upainiya wothandiza. Izi zinathandiza ena ofuna kuchita zambiri muutumiki kuona kuti pali anthu ambiri amene angagwire nawo ntchito. Anakonzanso zoti m’mawa kwambiri ndiponso madzulo pazikhala misonkhano yowonjezera yokonzekera utumiki wakumunda. Zotsatira zake zinali zakuti ofalitsa 53 analembetsa upainiya wothandiza mu April. Chiwerengero chimenechi chinali pafupifupi theka la mpingo wonse.
9. Kwa anthu amene ayenerera kukhala ofalitsa a uthenga wabwino, n’chifukwa chiyani nyengo ya Chikumbutso ndi yabwino kwambiri kuyamba kulalikira?
9 Thandizani Ena Kulalikira: Achinyamata ndiponso anthu ena akayenerera kukhala ofalitsa, angapemphedwe kulowa mu utumiki wakumunda ndi ofalitsa ena amene anayamba kale. Mwayi umenewu ungapezeke pa nyengo ya Chikumbutso pamene ambiri mumpingo amawonjezera utumiki wawo. Kodi pali munthu wina amene mukuphunzira naye Baibulo ndipo akupita patsogolo komanso moyo wake ukugwirizana ndi malamulo olungama a Yehova? Kodi muli ndi ana akhalidwe labwino omwe akupita patsogolo koma sanakhale ofalitsa? Anthu oterewa akasonyeza chidwi chokhala ofalitsa osabatizidwa ndipo inu mukuona kuti akuyenerera, dziwitsani mkulu wina aliyense. Woyang’anira wotsogolera adzakonza zoti akulu akambirane nanu za nkhaniyi limodzi ndi mwana kapena wophunzira wanuyo.
10. Kodi akulu angachite chiyani pothandiza abale ndi alongo osalalikira?
10 Miyezi ikubwerayi idzakhalanso yabwino kwambiri kwa abale ndi alongo osalalikira kuti ayambirenso kulalikira limodzi ndi mpingo. Oyang’anira Maphunziro a Buku a Mpingo ndiponso akulu ena ayenera kuyesetsa kuyendera anthu amenewa ndi kuwapempha mokoma mtima kuti adzayende nawo muutumiki. Ngati akhala osalalikira kwa nthawi yaitali, akulu awiri ayenera kulankhula nawo kaye kuti aone ngati ali oyenerera kulowa mu utumiki.—km-CN 11/00 tsa. 3.
11. Kodi n’chiyani chimasonyeza bwino kwambiri “kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu”?
11 Konzekerani Chikumbutso: Dipo limasonyeza bwino kwambiri “kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.” (Mac. 20:24) Padziko lonse, anthu mamiliyoni ambiri amtima woyamikira adzasonkhana Loweruka pa March 22, dzuwa litalowa kuti akumbukire imfa ya Khristu. Tikufuna kudzaitana ndi kuthandiza anthu onse amtima wabwino kuti adzabwere pa mwambo wofunikawu umene umachitira umboni za kukoma kwa m’chisomo kumene Yehova akusonyeza anthu.
12. Kodi tiyenera kuitana ndani ku Chikumbutso?
12 Lembani mayina a anthu amene mukufuna kudzawaitana. Mosakayikira pamndandandawo padzakhala mayina a achibale, anthu oyandikana nawo nyumba, anzanu a kuntchito kapena a kusukulu, anthu amene munkaphunzira nawo Baibulo ndi amene mukuphunzira nawo panopa ndiponso anthu ena onse omwe mumawayendera nthawi zonse. Ngati anthu ena omwe mwawaitana ali ndi mafunso okhudza Chikumbutso, mungagwiritse ntchito nkhani yopezeka m’zakumapeto yonena za Mgonero wa Ambuye pamasamba 206 mpaka 208 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kuchita zimenezi kungathandize kuti muyambe nawo phunziro la Baibulo chifukwa chakuti kudzakupatsani mwayi wowasonyeza buku limene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu Baibulo.
13. Kodi Yehova anadalitsa motani khama la ofalitsa awiri amene anakonza zoitanira anthu ena ku Chikumbutso?
13 Mlongo wina analemba mayina a mabanja 48 oti awaitane. Iye ankati akawaitana, ankakhwatcha dzina lawo papepala lake ndi kulembapo tsiku limene wawaitana. Mlongoyo anasangalala kwambiri kuona anthu 26 amene anawaitana atabwera ku Chikumbutso. M’bale wina yemwe ali ndi sitolo anaitana wantchito wake yemwe kale anali wansembe. Munthuyo anabweradi ndipo pambuyo pa Chikumbutso anati, “Pa ola limodzi limeneli, ndaphunzira zambiri za Baibulo kuposa zimene ndinaphunzira zaka 30 zimene ndakhala Mkatolika.” Pasanapite nthawi yaitali chichitikireni Chikumbutsocho, munthuyo anavomera kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
14. Kodi ndi ntchito yapadziko lonse yotani yomwe idzayambe pa March 1?
14 Ntchito Yapadera: Kuyambira Loweruka pa March 1 mpaka Loweruka pa March 22, padziko lonse padzakhala ntchito yogawa timapepala tapadera toitanira anthu ku Chikumbutso. Tikulimbikitsa ofalitsa onse kuti adzayesetse kuchita nawo mokwanira ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Zingadzakhale bwino kwambiri kuti eninyumba tidzawapatse pamanja timapepalati m’malo mowasiyira pakhomo. Komabe, ngati muli ndi gawo lalikulu, akulu angaone ngati mungamadzasiye timapepalato mosamala panyumba zomwe simunapezepo anthu. Koma Loweruka ndi Lamlungu tizidzagawiranso magazini atsopano.
15. Kodi tingadzanene zotani pogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso?
15 Popeza kuti tidzakhala ndi nthawi yochepa yogawira timapepalati, ndi bwino kungolankhula mwachidule. Komanso tidzaonetsetse kuti ndife aubwenzi ndi ansangala. Munganene kuti: “Tikudziwitsa anthu za mwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike pa March 22. Tikuyesetsa kuitanira aliyense ku mwambowu ndipo landirani kapepala kanu kokuitanirani ku mwambo umenewu. Zonse zokhudza mwambowu zili pa kapepala kameneka.” Mwininyumba angathe kulandira kapepalako ndi kunena kuti adzabwera kapena angakhale ndi mafunso. Tidzaonetsetse kuti tabwererako kwa onse amene adzasonyeze chidwi.
16. Kodi ndi nkhani yotani imene ikusonyeza phindu la ntchito yoitanira anthu a m’gawo lathu ku Chikumbutso?
16 Chaka chatha msilikali wina anapeza kapepala komuitanira ku Chikumbutso pakhomo pake. Anaganiza zopita ku mwambowu koma anayenera kuyamba wapempha kwa bwana wake. Atasonyeza bwanayo kapepalako, iye anakhala kaye chete kenako n’kunena kuti makolo ake ndi Mboni ndipo panthawi ina iye ankapita nawo kumisonkhano. Bwanayo analoleza msilikaliyo kuti apite ku Chikumbutsoko komanso iye anapita naye limodzi.
17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitinaphonye cholinga cha kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu?
17 Sonyezani Kuyamikira: Pamene tikuyandikira nyengo ya Chikumbutso cha 2008, tiyeni tonsefe tiziganizira za kukoma mtima kwa m’chisomo kumene Yehova watisonyeza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ifenso tikukudandaulirani kuti musalandire kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtima kumeneko.” (2 Akor. 6:1) Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitinaphonye cholinga cha kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu? Paulo analemba kuti: “Koma tikudzichitira umboni mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.” (2 Akor. 6:4) Motero timasonyeza kuyamikira mphatso ya Yehova mwa khalidwe lathu labwino ndiponso kukhala achangu polalikira uthenga wabwino. M’nyengo ya Chikumbutso imene ikubwerayi tidzakhala ndi mwayi waukulu kwambiri wowonjezera utumiki wathu, pochitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino.
[Bokosi patsamba 3]
Ndani Angathe Kuchita Nawo Upainiya Wothandiza?
◼ Mabanja
◼ Anthu apantchito
◼ Anthu okalamba ndi athanzi lofooka
◼ Amene ali pa sukulu
[Bokosi patsamba 4]
Pogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso:
◼ Lankhulani mwachidule ndi mwansangala
◼ Onetsetsani kuti mwabwererako kwa onse amene anasonyeza chidwi
◼ Gawirani magazini Loweruka ndi Lamlungu