Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/04 tsamba 3-5
  • Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Chitirani Umboni Bwino Lomwe za Uthenga Wabwino’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 2/04 tsamba 3-5

Pitirizani Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Yehova

1. Kodi ntchito zina zodabwitsa za Yehova zimene mumayamikira makamaka n’ziti?

1 Palibe amene angafanane ndi Mulungu wathu wamkulu, Yehova! Davide analemba kuti: “Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera [“wofanana ndi,” NW] Inu.” (Sal. 40:5) Ntchito zodabwitsa za Yehova zimaphatikizapo kupanga chilengedwe chonse, Ufumu wa Mesiya, kukoma mtima kwachikondi kumene amachitira anthu ake, ndi ntchito yolalikira padziko lonse. (Sal. 17:7, 8; 139:14; Dan. 2:44; Mat. 24:14) Kukonda kwathu Yehova ndi kuyamikira zonse zimene iye watichitira kumatilimbikitsa kuwauza ena za iye. (Sal. 145:5-7) Miyezi ya March, April, ndi May, tidzakhala ndi mpata wochita zimenezi mokwanira.

2. Kodi ifeyo timapindula motani tikamachita upainiya wothandiza?

2 Monga Mpainiya Wothandiza: Kodi mungakonze pulogalamu yanu kuti muthere maola 50 mu utumiki mwezi umodzi kapena ingapo pa miyezi yapadera imeneyi pamene tidzakhala kalikiliki pa ntchito? Mudzapindula kwambiri posintha zina n’zina pamoyo wanu. (Aef. 5:16) Ambiri apeza kuti chifukwa cha upainiya wothandiza, luso lawo mu utumiki limapita patsogolo. Mtima wawo umakhala m’malo kwambiri pofika pakhomo la munthu ndipo amatha kugwiritsa ntchito Baibulo momasuka. Chifukwa chothera nthaŵi yambiri mu utumiki, savutika kubwerera kwa anthu amene amaonetsa chidwi, ndipo ena amene m’mbuyomu analibe phunziro la Baibulo alipeza pochita upainiya wothandiza. Upainiya wothandiza ndi ntchito yosangalatsa chifukwa chakuti umafuna khama kuti tithandize ena.—Mac. 20:35.

3. Kodi zatheka bwanji ena kuchita upainiya wothandiza ngakhale kuti moyo wawo n’ngovutirapo?

3 Musafulumire kuganiza kuti ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu simungathe kuchita ntchito imeneyi. Mkulu wina wa ana aŵiri ndiponso amagwira ntchito tsiku lonse anachita upainiya wothandiza chaka chatha. Kodi zinatheka bwanji mbale wotanganidwa ameneyu kuchita zimenezo? Popeza kuti amagwira ntchito m’kati mwa mlungu, anakonza zokhala mu utumiki nthaŵi yaitali kumapeto kwa mlungu, kuyamba ndi ulaliki wa mumsewu nthaŵi ya 7 koloko m’maŵa, Loŵeruka lililonse. Ambiri mu mpingowo amene moyo wawo unali ngati wa mbaleyu anachitanso upainiya, ndipo anathandizana ndi kulimbikitsana. Mumpingo wina, mlongo wa zaka 99 analembetsa upainiya mwezi wa May atapemphedwa ndi mwana wake wamkazi kuti azigwira naye ntchito. Ena mumpingo anam’thandiza mlongo wokalambayu kupita khomo ndi khomo komanso ku maphunziro a Baibulo mwa kumuyendetsa panjinga ya opuwala. Mlongoyu anachitanso ulaliki wa patelefoni, wa mumsewu, ndi wolemba makalata. Iye akutsimikiza kuti zimene anachitazo sanazichite ndi mphamvu zake ayi koma ndi thandizo la Yehova.—Yes. 40:29-31.

4. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingazipende pokonza pulogalamu yochita upainiya wothandiza?

4 Lembani pulogalamu yogwirizana kwambiri ndi moyo wanu. Zitsanzo za ndandanda zimene zili munozi zingakuthandizeni. Kodi mumagwira ntchito tsiku lonse kapena kupita ku sukulu? Pulogalamu yoti muzilalikira kwambiri kumapeto kwa mlungu mwina ndi imene ingakukomereni inuyo. Ngati thanzi lanu silili bwino ndipo mulibe nyonga yokhala mu utumiki tsiku lonse, mwina pulogalamu yokulolani kuthera nthaŵi yochepa mu utumiki tsiku lililonse ndi imene ingakukomereni. Kambiranani ndi ena cholinga chanu chofuna kuchita upainiya wothandiza. Mwina iwonso angasankhe kukhala ndi cholinga chomwecho.

5. Kodi achinyamata angakhale ndi zolinga zotani miyezi ya March, April, ndi May?

5 Zimene Achinyamata Angachite: Yehova amasangalala achinyamata akamauza ena za ntchito zake zodabwitsa. (Sal. 71:17; Mat. 21:16) Ngati ndinu wachinyamata ndipo ndinu wobatizidwa, mwina mungachite upainiya wothandiza mwezi umene mumakhala patchuthi kusukulu. Ngati simungathe kuchita upainiya wothandiza, kodi mungakhale ndi cholinga chowonjezera utumiki ndi kupititsa patsogolo luso lanu miyezi imeneyi? Ngati mwakhala mukupita mu utumiki ndi makolo anu koma simunakhalebe wofalitsa wosabatizidwa, ino ndiyo nthaŵi yabwino yoti muyesetse kuti mukhale woyenerera. Musaganize kuti mufunika kuchita kukhala katswiri woyankha mafunso okhudza Baibulo kapena kuti mufunika kudziŵa zambiri ngati achikulire amene anabatizidwa kale. Kodi mukuzidziŵa ziphunzitso zikuluzikulu zoyambirira za m’Baibulo? Kodi mumatsatira miyezo ya makhalidwe abwino ya m’Baibulo? Kodi mukufuna kudziŵika monga wa Mboni za Yehova? Ndiye uzani makolo anu. Iwo angakonze zoti inuyo limodzi nawo mukaonane ndi akulu pofuna kudziŵa ngati mukukwanitsa ziyeneretso zake.—Onani buku la Utumiki Wathu, masamba 98-9.

6. Kodi tingawathandize bwanji ophunzira Baibulo kukhala ofalitsa uthenga wabwino?

6 Kuthandiza Ena Kulalikira: Ophunzira Baibulo amene akupita patsogolo angayenerere kugwira nafe ntchito monga ofalitsa miyezi ikudzayi imene tidzakhala ndi ntchito yapadera. Ngati muli ndi wophunzira Baibulo amene akupita patsogolo, uzani woyang’anira phunziro la buku lanu kapena woyang’anira utumiki kuti akuthandizeni. Mmodzi wa iwo angapite nanu ku phunzirolo kuti akaone mmene wophunzirayo akupitira patsogolo. Ngati wophunzirayo akuyenerera ndipo akufuna kukhala wofalitsa, woyang’anira wotsogolera angakonze zoti akulu aŵiri akumane ndi inu ndi wophunzira wanuyo. (Onani Nsanja ya Olonda, ya November 15, 1988, tsamba 17.) Wophunzirayo akavomerezedwa, yambani kum’phunzitsa mu utumiki mwamsanga.

7. Kodi ofalitsa osakhazikika ndi osalalikira angathandizidwe motani?

7 Oyang’anira phunziro la buku afunika kupereka chisamaliro chapadera kwa aliyense wosalalikira kapena wosakhazikika m’kagulu kawo. Apempheni kuti muyende nawo mu utumiki. Ngati akhala osalalikira kwa nthaŵi yaitali, ndi bwino kuti akulu aŵiri ayambe alankhula nawo kuona ngati akuyenererabe. (Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2000.) Kukangalika kwa mpingo miyezi imeneyi imene kudzakhala ntchito yapadera kungawalimbikitse kuyambiranso kulalikira mokhazikika pamoyo wawo.

8, 9. Kodi akulu angachite chiyani kulimbikitsa abale kuchita chidwi ndi ntchito yapaderayi?

8 Konzekerani Panopa Kudzachita Zambiri: Akulu, yambani panopa kulimbikitsa mpingo kuchita chidwi ndi upainiya wothandiza. Ndemanga zanu zolimbikitsa ndi chitsanzo chanu chabwino zingathandize kwambiri. (1 Pet. 5:3) Kodi ulendo watha chiŵerengero chapamwamba cha apainiya othandiza chinali chotani pampingo wanu? Kodi chingapose pamenepo chaka chino? Oyang’anira phunziro la buku ndi othandiza awo apeze njira zolimbikitsira onse m’kagulu kawo kuchita zochuluka. Oyang’anira utumiki angakonze misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda yowonjezereka. Udziŵitseni mpingo pasadakhale zimene zakonzedwa. Onetsetsani kuti ofalitsa okhoza apatsidwa udindo wotsogolera abale ndiponso kuti misonkhano yokonzekera utumiki ikuyamba ndi kutha panthaŵi yake. (Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2001.) Woyang’anira utumiki afunikanso kukonza zoti pakhale gawo lokwanira, magazini, ndi mabuku okwanira.

9 Chaka chatha akulu a mpingo wina anayamba pasadakhale komanso ndi mtima wonse kulimbikitsa upainiya wothandiza, ndipo ambiri mwa iwo analembetsa. Anakonza misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda yowonjezera—wina umayamba 5:30 m’maŵa kukonzekera ulaliki wa mumsewu, wina wa oŵeruka kusukulu umayamba 3 koloko masana, ndipo wachitatu wa oŵeruka kuntchito umayamba 6 koloko madzulo. Ndiponso, anakonza misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda itatu Loŵeruka lililonse. Mpingowo unalabadira zimenezo ndipo unali ndi apainiya othandiza 66 mu April!

10. Kodi mabanja angachite chiyani kuti akonzekere kudzachita zambiri?

10 Bwanji osapatula nthaŵi paphunziro lanu la banja lotsatira kuti mudzakhazikitse zolinga zotheka zoti mudzakwaniritse miyezi ikudzayi? Mwa kugwirizana bwinobwino komanso dongosolo labwino, ena kapena onse m’banja angathe kuchita upainiya wothandiza. Ngati zimenezo sizitheka, khalani ndi zolinga zowonjezera ntchito mwa kukhala ndi nthaŵi yambiri yothera mu utumiki masiku onse kapena mwa kupita mu utumiki nthaŵi zambiri. Nkhani imeneyi muziitchula m’mapemphero m’banja lanu. Dziŵani kuti Yehova adzakudalitsani chifukwa cha khama lanu.—1 Yoh. 3:22.

11. (a) Kodi nsembe ya Kristu inatheketsa zinthu ziti zodabwitsa? (b) Kodi pampingo pathu pano Chikumbutso chidzachitika nthaŵi yanji ndipo chidzachitikira kuti?

11 Ntchito ya Mulungu Yodabwitsa Koposa: Njira yaikulu imene Yehova anaonetsera chikondi chake ndiyo kutipatsa Mwana wake monga mphatso kuti atiperekere dipo. (1 Yoh. 4:9, 10) Nsembe ya dipo ndiyo maziko alamulo owombolera anthu ku uchimo ndi imfa. (Aroma 3:23, 24) Chifukwa cha magazi a Yesu, pangano latsopano linayamba kugwira ntchito, ndipo zinatheka kuti anthu opanda ungwiro akhale ana a Mulungu oyembekezera kukalamulira mu Ufumu wa kumwamba. (Yer. 31:31-34; Marko 14:24) Makamaka, kumvera kwa Yesu kwangwiro kunayeretsa dzina la Yehova. (Deut. 32:4; Miy. 27:11) Lamlungu, pa April 4, dzuŵa litaloŵa, kudzakhala mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu padziko lonse lapansi.

12. Kodi kupezeka pa mwambo wa Mgonero wa Ambuye kungawapindulitse motani anthu achidwi?

12 Mwambo wa Mgonero wa Ambuye umachititsa ntchito zodabwitsa za Yehova kuonekera kwambiri. Nkhani yake imatithandiza kumvetsa ndi kuyamikira zimene Yehova anachita mwa kupereka dipo. Anthu achidwi opezekapo adzatha kuona ntchito zina zodabwitsa za Mulungu. Adzaona umodzi ndi chikondi chachikulu zimene Yehova waphunzitsa anthu ake kuti akhale nazo. (Aef. 4:16, 22-24; Yak. 3:17, 18) Chifukwa chopezeka pa mwambo wofunika kwambiri umenewu maganizo a munthu akhoza kusintha kwambiri. N’chifukwa chake tikufuna kuti anthu ambirimbiri adzapezekepo.—2 Akor. 5:14, 15.

13, 14. Kodi tiyenera kuitana ndani kuti abwere ku Chikumbutso, nanga tingawaitane motani?

13 Kuitana Ena Kuti Adzapezekepo: Yambani nthaŵi yomwe ino kukonzekera mwa kulemba mayina a amene mukufuna kuitana. Muphatikizepo achibale anu osakhulupirira, achinansi, anthu amene mukuwadziŵa kuntchito kapena kusukulu, maphunziro anu a Baibulo akale ndi apanopa, ndi onse amene mumapitako pamaulendo obwereza. Oyang’anira phunziro la buku ayenera kuphatikizapo wofalitsa aliyense wosalalikira pa mpambo wawo wa mayina.

14 Gwiritsani ntchito timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, ndipo taipani kapena lembanipo mwaudongo nthaŵi ndi malo a Chikumbutso. Mwina mungafune kugwiritsa ntchito pempho limene likupezeka patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya March 15, 2004, kapena Galamukani! ya April 8, 2004. Ndiyeno April 4 ikamayandikira, akumbutseni amene munalemba pampambo wanuwo, mwa kupitako kapena kuwaimbira telefoni.

15. Kodi tingaonetse motani mtima wochereza alendo usiku wa Chikumbutso?

15 Pa Chikumbutso: Yesetsani kufika mofulumira usiku wa Chikumbutso. Onetsani mtima wochereza alendo mwa kupatsa atsopano moni wochokera pansi pa mtima. (Aroma 12:13) Mudzakhala ndi udindo wapadera kwa alendo amene munaitana. Alandireni bwino, ndi kuwaonetsa kwa ena mumpingo. Mwina mungawathandize kupeza pokhala pafupi ndi inu. Ndipo ngati ena alibe Baibulo kapena buku la nyimbo, konzani zoti inuyo kapena wina aonere nawo limodzi. Mwambowu ukatha, khalani okonzeka kuyankha mafunso alionse amene iwo angafunse. Ngati ena n’koyamba kupezekapo, afunseni ngati akufuna kudziŵa zambiri zokhudza Mawu a Mulungu ndi zolinga zake. Apempheni kuchita nawo phunziro la Baibulo la panyumba.

16. Kodi tingachite chiyani kuti tithandize amene anapezekapo pa Chikumbutso kuti apite patsogolo mwauzimu?

16 Pitirizani Kuthandiza Amene Anapezekapo: Milungu ingapo Chikumbutso chitapita, amene anapezekapo angafunikire thandizo lina. Anthu ameneŵa akuphatikizapo aja amene kale anali kusonkhana mokhazikika koma tsopano amangogwirizana ndi mpingo mwa kamodzikamodzi. Akulu adzakhala tcheru kuonetsetsa kuti anthu ngati ameneŵa asanyalanyazidwe, ndipo angafune kudziŵa kuti chinachitika n’chiyani kuti anthuwo asiye kupita patsogolo mwauzimu. Athandizeni kuona kuti nthaŵi imene tikukhalayi m’pofunika kuchita changu. (1 Pet. 4:7) Athandizeni onse kuona kuti kutsatira langizo la m’Malemba losonkhana pamodzi mokhazikika ndi anthu a Mulungu kuli ndi phindu.—Aheb. 10:24, 25.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kulalikira ntchito zodabwitsa za Yehova?

17 Ntchito za Yehova n’zodabwitsa kwambiri moti sitingathe kuzimvetsa zonse, ngakhale titakhala ndi moyo kosatha. (Yobu 42:2, 3; Mlal. 3:11) Choncho, sitidzasoŵa m’pang’ono pomwe zifukwa zom’tamandira. Nyengo ino ya Chikumbutso, tingaonetse mtima woyamikira ntchito zodabwitsa za Yehova mwa kuyesetsa kufutukula utumiki wathu.

[Tchati patsamba 5]

Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza mwa Kugwiritsa Ntchito Imodzi mwa Ndandandazi?

March M L* Ŵ* T* N S Ŵ Chiwo.

cha Mwezi

Tsiku Lililonse 2 1 1 1 1 1 5 51

Masiku Aŵiri 0 5 0 5 0 0 0 50

Mapeto a

Mlungu Okha 5 0 0 0 0 0 8 52

Mapeto a Mlungu

ndi Masiku Aŵiri

M’kati mwa Mlungu 2 0 0 2 0 2 6 50

April M L Ŵ T N* S* Ŵ Chiwo.

cha Mwezi

Tsiku Lililonse 2 1 1 1 1 1 5 50

Masiku Aŵiri 0 0 0 0 5 5 0 50

Mapeto a Mlungu Okha 5 0 0 0 0 0 8 52

Mapeto a Mlungu

ndi Masiku Aŵiri

M’kati mwa Mlungu 2 0 0 2 0 2 6 50

May M* L* Ŵ T N S Ŵ* Chiwo.

cha Mwezi

Tsiku Lililonse 2 1 1 1 1 1 4 51

Masiku Aŵiri 0 5 0 0 0 0 5 50

Mapeto a Mlungu Okha 3 0 0 0 0 0 7 50

Mapeto a Mlungu

ndi Masiku Aŵiri

M’kati mwa Mlungu 2 0 0 2 0 2 5 51

*Asanu m’mwezi umodzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena