Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/97 tsamba 3-5
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Lalikirani ndi Kuchitira Umboni Mokwanira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 2/97 tsamba 3-5

Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika

Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza m’March? m’April? m’May?

1 “Alaliki 1,000 Akufunika” unali mutu wa nkhani yofalitsidwa m’kope la Nsanja ya Olonda lachingelezi la April 1881. Inali kupempha amuna ndi akazi onse odzipatulira, “amene Ambuye wawapatsa chidziŵitso cha choonadi Chake,” kuti agwiritsire ntchito nthaŵi iliyonse imene angapeze, kukhala ndi phande pakufalitsa choonadi cha Baibulo. Awo amene anali okhoza kupereka theka la nthaŵi yawo kapena yoposapo pantchito ya Ambuye yokhayokha analimbikitsidwa kuchita ntchito yodzifunira monga alaliki akopotala—olambulira njira apainiya alero.

2 Ngakhale kuti nthaŵi zasintha kuchokera m’ma 1800, choonadi chimodzi chakhalabe choncho—atumiki odzipatulira a Mulungu akufuna kupitiriza kugwiritsira ntchito nthaŵi yochuluka yomwe angapeze pakufalitsa uthenga wabwino. Kutumikira monga apainiya othandiza kumachititsa ofalitsa a mpingo kuwongolera luso lawo pamene athera nthaŵi yowonjezereka mu utumiki wa Ufumu.—Akol. 4:17; 2 Tim. 4:5.

3 Kuchokera pamene upainiya wothandiza unayamba, abale ndi alongo zikwi mazana ambiri asangalala nawo. Mosalefuka ndi chizunzo chankhanza cha zaka zambiri, changu pambali imeneyi ya utumiki waupainiya chinakula kwambiri kwakuti chiŵerengero chapamwamba koposa cha apainiya othandiza chinafika pa 220 m’gawo la nthambi ya Malaŵi mu 1985. Ziŵerengero zimenezi zakwerabe molimbikitsa pamene ofalitsa ochita upainiya wothandiza anawonjezeka kufika pa 2,548 mu 1995. Lero tikhozadi kubwereza ntchito yabwino imeneyi paphukuto mu 1997.

4 Tikukulimbikitsani kukhala ndi chonulirapo cha kuchita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena yoposapo m’miyezi ya March, April, ndi May. Nchifukwa ninji tikuphatikizapo March? Chifukwa chakuti chaka chino Chikumbutso cha imfa ya Kristu chidzakhalako pa Sande, March 23. Palibe njira ina yabwino kwambiri imene tingathere milungu yoyamba Chikumbutso chisanafike kuposa kukhala ndi phande mwachangu pantchitoyi yolalikira Ufumu imene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Kristu, anayamba. Mwa mulu waukulu wa umboni umene udzaperekedwa m’March, tingaitanire anthu ambiri amene akufuna kuti adzagwirizane nafe pokumbukira imfa ya Kristu. March adzakhalanso wapadera chifukwa chakuti, kwa nthaŵi yoyamba, tidzagaŵira buku latsopano, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Ndiponso, mwezi wa March uli ndi masiku a Loŵeruka asanu ndi masiku a Sande asanu, kutilola kugwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda pakutha kwa milungu. Ndiyeno, m’miyezi ya April ndi May, kupitirizabe kuyesayesa mwachangu mu utumiki kudzatilola kubwerera kwa amene anasonyeza chidwi ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba atsopano, kugwiritsira ntchito brosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Tidzafolanso gawo lathu mosamalitsa ndi magazini atsopano apanthaŵi yake a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! makamaka pakutha kwa milungu.

5 Kodi Ndani Ayenera Kuchita Upainiya Wothandiza?: Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, tsamba 113-4, limalongosola kuti: “Iliyonse imene ingakhale mikhalidwe yanu ya inu mwini, ngati muli wobatizidwa, muli ndi mkhalidwe wabwino wamakhalidwe, mungalinganize kufitsa chofunika chothera maola 60 pamwezi mu uminisitala wakumunda ndipo mukukhulupirira kuti mukatha kutumikira mwezi umodzi kapena yambiri monga mpainiya wothandiza, akulu a mpingo adzakondwera kulingalira chopemphera chanu cha mwaŵi wa utumiki umenewu.” Kodi mwaŵi umenewu mungaupezere mpata m’March? m’April? m’May?

6 Kaonedwe kabwino ka mabungwe a akulu limodzinso ndi chichirikizo chamtima wonse cha ofalitsa onse ziyenera kuchititsa chiitano chimenechi cha apainiya othandiza 3,000 kumvedwa mwachipambanodi. (Aheb. 13:7) Mitu yonse ya mabanja ikulimbikitsidwa kudziŵiratu motsimikiza kuti ndi angati m’banja lawo amene angaloŵe upainiya wothandiza m’mwezi umodzi kapena yoposapo m’miyezi ikudzayi.—Sal. 148:12, 13; yerekezerani ndi Machitidwe 21:8, 9.

7 Musafulumire kunena kuti simungathe kuchita upainiya wothandiza chifukwa cha ntchito yanu yolembedwa ya nthaŵi zonse, ndandanda ya kusukulu, mathayo a banja, kapena mathayo ena a Malemba. Kwa ena kutengamo mbali kungakhale kovuta kwambiri; komabe, mwa kulinganiza zinthu bwino limodzi ndi dalitso la Yehova, iwo angapambane. (Sal. 37:5; Miy. 16:3) Lolani chikhumbo chanu cha kukhala ndi phande mu utumiki waupainiya kulamulira mikhalidwe yanu; musalole mikhalidwe yanu kulamulira chikhumbo chanu cha kuchita upainiya. (Miy. 13:19a) Chifukwa chake, pokhala ndi chikondi chachikulu pa Yehova ndi anthu anzawo, ambiri amatha kusintha ndandanda ya moyo wawo wa mlungu ndi mlungu kuti afutukule utumiki wawo mwezi uliwonse pawokha. (Luka 10:27, 28) Awo amene amalimbikira mwamphamvu mu utumiki wa Ufumu adzalandira madalitso ambiri.—1 Tim. 4:10.

8 Zimene Upainiya Wothandiza Umakwaniritsa: Kuyesayesa kochokera mumtima kumene atumiki a Mulungu zikwi zambiri amachita kuti achite upainiya wothandiza kumachititsa mfuu yaikulu yotamanda Yehova. Pamene olengeza Ufumu ameneŵa alimbikira kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu owonjezereka, amayandikira kwambiri kwa Yehova mwaumwini chifukwa chakuti amaphunzira kumdalira kwambiri kuti awapatse mzimu wake ndi dalitso.

9 Kukhala ndi apainiya othandiza, okhazikika, ndi apadera achangu pakati pathu kumadzetsa mzimu watsopano wachangu mumpingo. Changu chawo chimayambukira ena pamene asimba zokumana nazo zawo za m’munda. Zimenezi zimasonkhezera ena kuti asanthulenso zinthu zawo zofunika kwambiri ndi kutheka kwake kokhala ndi phande lalikulu pantchito yofunika koposa ya utumiki. Mlongo amene anabatizidwa ali ndi zaka 70 anayamba upainiya wothandiza wosalekeza nthaŵi yomweyo. Atamfunsa pambuyo pa zaka zingapo chifukwa chimene anali kulimbikirabe kwambiri mu utumiki monga mpainiya wothandiza mwezi uliwonse, pausinkhu umenewo, ananena kuti anaona monga kuti zaka 70 zoyamba za moyo wake zinatayika, ndipo sanafune kutayanso zaka zilizonse zotsala za moyo wake!

10 Aliyense wokhala ndi phande pantchito ya upainiya wothandiza amakulitsa luso kwambiri mu utumiki. Mboni ina yachichepere inavomereza kuti: ‘Ndikali mwana wamng’ono ndinali kutsagana ndi makolo anga m’ntchito yawo yolalikira. Utumiki wakumunda unalidi wosangalatsa. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, ndinazindikira kuti kusukulu ndinali wosiyana ndi khamu lonse. Ndiyeno ndinaipidwa ndi kulankhula za choonadi ndi ophunzira anzanga. Polalikira kunyumba ndi nyumba, ndinayamba kuopa kukumana ndi wina amene ndimamdziŵa kusukulu. Ndikhulupirira kuti vuto langa linali kuopa anthu. [Miy. 29:25] Nditamaliza sukulu, ndinasankha kuyesa upainiya wakanthaŵi. Chotulukapo chake chinali chakuti kulalikira kunakhala kosangalatsa kuposa ndi kale lonse. Sindinakuonenso ngati maseŵero osangalatsa, ndipo sikunalinso mtolo wolemetsa. Pamene ndinali kuona ophunzira Baibulo anga akupita patsogolo m’choonadi, ndinadzimva wokhutira kwambiri poona umboni wakuti Yehova Mulungu anali kuchirikiza zoyesayesa zanga.’ Wachichepereyu anapitabe patsogolo natumikira monga mpainiya wokhazikika.

11 Kunena zoona ndi maso, pamene ambiri mumpingo atumikira monga apainiya othandiza, gawo limafoledwa mosamalitsa. Mbale amene amagaŵira ndime angapemphe thandizo la apainiya othandiza kuti afole ndime zosafoledwa kaŵirikaŵiri. Kunyamula chakudya chamasana ndi kuchita utumiki tsiku lonse kudzawatheketsa kugwira ntchito m’mbali zakutali za gawo.

12 Akulu Pangani Makonzedwe Pasadakhale: M’miyezi yonse itatu ikudzayi, makonzedwe ayenera kupangidwa ondandalika mitundu yosiyanasiyana ya ntchito yochitira umboni panthaŵi zosiyanasiyana za mlungu, kuphatikizapo masana mochedwa ndi kuchiyambi cha madzulo, kotero kuti ambiri atengemo mbali. Kuwonjezera pantchito ya kunyumba ndi nyumba ya nthaŵi zonse, phatikizanipo nthaŵi ya umboni wa m’khwalala, kugwira ntchito m’gawo lamalonda, ndi kupita kwa amene sanali panyumba. Mwakutero, akulu amathandiza awo amene akuchita upainiya kukhala ndi phande mu utumiki limodzi ndi mpingo panthaŵi imene idzakhala yabwino ndi yoyenera kwambiri kwa apainiya. Mpingo uyenera kuuzidwa za makonzedwe onse a utumiki wakumunda. Makonzedwe a kukumana kwa utumiki ayenera kulinganizidwa bwino kwambiri. Ndiponso, gawo lokwanira liyenera kukhalapo ndipo magazini ndi mabuku ena okwanira ayenera kuodedwa pomwepo.

13 Konzani Ndandanda Yanu ya Utumiki: Mbale wina, amene poyamba ankaopa kuchita upainiya wothandiza, anati: “Kunena zoona nzopepuka kwambiri kuposa ndi mmene ndinkati zidzakhalira. Zimangofuna ndandanda yabwino.” Patsamba lakumbuyo la mphatika ino, kodi mwaona chitsanzo cha ndandanda ya mpainiya wothandiza imene ingagwire ntchito kwa inu? Maola 15 mlungu uliwonse mu utumiki ndiyo nthaŵi yokha yofunika kwa apainiya othandiza.

14 Kuti atumikire monga apainiya othandiza, akazi okwatiwa osalembedwa ntchito ndi ogwira ntchito m’chipani chachiŵiri kambiri angalinganize kuti azipita mu utumiki wakumunda mmaŵa. Ana a sukulu ndi ogwira ntchito m’chipani chachitatu nthaŵi zambiri angachite ntchito yolalikira masana mochedwa. Ogwira ntchito yolembedwa yanthaŵi zonse apeza kuti nkotheka kutenga tsiku limodzi lopuma pantchito mlungu uliwonse kapena kuchita utumiki masiku athunthu pakutha kwa mlungu, kuwonjezera pa umboni wamadzulo. Ambiri amene nthaŵi zambiri amatha kuchita utumiki wawo wakumunda kokha pakutha kwa mlungu amasankha miyezi imene ili ndi mapeto a milungu athunthu asanu. Chaka chino, ndi mmene zakhalira ndi March, ndiponso August ndi November. Mwa kugwiritsira ntchito ndandanda yosadzaza patsamba 6 imene yaperekedwa monga chitsogozo, lingalirani mwapemphero ndi mosamala za ndandanda yanu ya utumiki imene idzakhala yogwira ntchito malinga ndi mkhalidwe wanu.

15 Ubwino wina wa upainiya wothandiza ndi wakuti mukhoza kumasinthasintha. Mungasankhe miyezi imene mukufuna kuchita upainiyawo, ndipo mungatumikire kwa nthaŵi zimene mufuna. Ngati mukufuna kuchita upainiya wothandiza wosalekeza koma simutha, kodi mwaganiza za kulembetsa patapita mwezi umodzi uliwonse chaka chonse? Kumbali ina, ena atha kutumikira mosalekeza monga apainiya othandiza kwa nthaŵi zazitali.

16 Kukonzekera Upainiya Wanthaŵi Zonse: Ambiri amene ali ndi mzimu waupainiya amafuna kutumikira monga apainiya okhazikika, koma amakayikira ngati ali nayo nthaŵi, mikhalidwe yoyenera, kapena nyonga yoti achite motero. Mosakayikira ambiri amene akuchita upainiya wokhazikika tsopano anayamba achita upainiya wothandiza monga wowakonzekeretsa kuchita ntchito ya nthaŵi zonse. Mwa kuwonjezera ola limodzi lokha tsiku lililonse pandandanda yake yaupainiya wothandiza, kapena tsiku limodzi lathunthu mlungu uliwonse, munthu akhoza kukwaniritsa nthaŵi yaupainiya wokhazikika. Kuti mudziŵe ngati zimenezo nzotheka kwa inu, bwanji osayesa kuthera maola 90 mu utumiki m’mwezi umodzi kapena yoposapo m’miyezi ya upainiya wothandiza? Nthaŵi imodzimodziyo, mudzapanga maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo, zimene zidzakulolani kuchita utumiki waupainiya wokwana bwino.

17 Mlongo wina anasangalala kuchita upainiya wothandiza wosalekeza kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Kwa nthaŵi yonseyo chonulirapo chake chinali kuloŵa utumiki waupainiya wokhazikika. Pokhala ndi cholinga chimenecho, anayesa ntchito zolembedwa zinayi zosiyanasiyana pofuna kupeza mpata umene ukanamlola kukwanitsa maola 90 ofunika kwa apainiya okhazikika. Mwezi uliwonse, ankalemba ndandanda imodzi kapena ziŵiri kuti aone ngati zingatheke. Koma atazipenda, ankaona kuti utumiki wanthaŵi zonse sunali wotheka kwa iye. Komabe, anapitiriza kupempha Yehova kuti amtsogoze. Ndiyeno tsiku lina pamene anali kukonzekera Msonkhano Wautumiki, anaŵerenga nkhani ina mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1991 imene inati: “M’malo moika chigogomezero chopambanitsa pachiyeneretso cha maola, bwanji osasumika chidwi pamwaŵi wowonjezereka wakukhala ndi phande m’ntchito yotuta? (Yoh. 4:35, 36)” Iye akusimba kuti: “Ndinaŵerenganso chiganizochi kasanu kapena kasanu ndi kamodzi, ndipo ndinatsimikiza kuti limeneli linali yankho la Yehova. Pamenepo ndinasankha kuloŵa utumiki waupainiya wokhazikika.” Ngakhale kuti ntchito yake yolembedwa ya maola ochepa sinali kumpatsa nthaŵi, anapereka fomu yake yofunsirapo upainiya wokhazikika. Patapita mlungu umodzi ndandanda yake inasintha, ndipo anapatsidwa maola ogwira ntchito yolembedwa amene anamkhalira bwino kwambiri. Anamaliza kuti, “Kodi limeneli si dzanja la Yehova?,” nawonjezera kuti: “Ukapempha Yehova chitsogozo chake ndipo chafika, usachithaŵe—chilandire.” Ngati mukufunitsitsa kuchita upainiya wokhazikika, mwinamwake pakutha kwa miyezi itatu ya upainiya wothandiza m’March, April, ndi May akudzayo, mudzakhulupirira kuti nanunso mungakhale ndi chipambano mu utumiki wanthaŵi zonse.

18 Tili otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa changucho ndipo adzachirikiza zoyesayesa za anthu ake pamene akufalitsa uthenga wabwino wa chipulumutso m’nthaŵi yamasika yantchito yapaderayi. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Kodi mudzayankha chiitano cha apainiya othandiza 3,000 mwa kukhala ndi phande m’March? m’April? m’May?

[Bokosi patsamba 3]

Mmene Mungapambanire Monga Mpainiya Wothandiza

■ Khalani ndi chidaliro chakuti mudzachita zimene mukufuna

■ Pempherani kwa Yehova kuti adalitse zoyesayesa zanu

■ Pemphani wofalitsa winanso kuchita nanu upainiya

■ Konzani ndandanda yogwira ntchito ya utumiki

■ Ombolani magazini okwanira

■ Chirikizani makonzedwe a mpingo a utumiki

■ Pezani mpata wolalikira mwamwaŵi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena