Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
1. Kodi n’cholinga chotani chomwe tingakhale nacho m’chaka chautumiki chatsopano?
1 Ngati tifuna kuti tipite patsogolo mwauzimu tiyenera kukhala ndi zolinga. Kodi m’chaka chautumiki chatsopano mudzakhala ndi zolinga zotani? Cholinga chabwino kwambiri ndicho kuchita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena kuposapo. Popeza ntchito yosangalatsa imeneyi nthawi zambiri imafuna kukonzekera nthawi idakalipo, ino ndiyo nthawi yabwino yoyamba kuchita zimenezi. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira upainiya wothandiza kukhala cholinga chathu?
2. Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhalira ndi cholinga chochita upainiya wothandiza?
2 Zifukwa Zochitira Upainiya Wothandiza: Upainiya wothandiza umatithandiza kusangalatsa Atate wathu wakumwamba “mowonjezereka” pamene tigwiritsa ntchito nthawi yochuluka muutumiki wa kumunda. (1 Ates. 4:1) Tikamaganizira zimene Yehova watichitira, timalimbikitsidwa kuuza ena za iye. (Sal. 34:1, 2) Yehova amaona ndipo amayamikira kwambiri zinthu zimene timachita modzimana kuti tichite zambiri muutumiki wake. (Aheb. 6:10) Timakhala ndi chimwemwe kwambiri kudziwa kuti tikusangalatsa Yehova chifukwa chogwira ntchito mwakhama.—1 Mbiri 29:9.
3, 4. Kodi timapindula motani tikachita upainiya wothandiza?
3 Nthawi zambiri mukamachita chinthu kawirikawiri, chinthucho chimakhala chosavuta ndiponso chosangalatsa. Mukamathera nthawi yochuluka muutumiki muzitha kulankhula momasuka polalikira khomo ndi khomo. Mudzakhala aluso poyambitsa kukambirana ndiponso pogwiritsa ntchito Baibulo. Mukamalankhula za chikhulupiriro chanu nthawi zambiri, chikhulupirirocho chimalimba kwambiri. Anthu ambiri amene analibe phunziro la Baibulo, ayambitsa limodzi nthawi imene akuchita upainiya wothandiza.
4 Upainiya wothandiza ungatilimbikitsenso kusiya kuchita zinthu zauzimu mwamwambo. Mbale wina amene kale anali mpainiya wokhazikika ataona kuti ankathera nthawi yochuluka pantchito yake, analembetsa upainiya wothandiza wa mwezi umodzi. Iye anati: “Ndinadabwa kwambiri kuona mmene ndinalimbikitsidwira mwauzimu m’mwezi umodzi umenewo. Motero, ndinasankha kuchita upainiya wothandiza mosalekeza ndipo m’kupita kwa nthawi zimenezi zinandithandiza kuti ndikhalenso mpainiya wokhazikika.”
5. Kodi tingathetse bwanji maganizo odzikayikira?
5 Pewani Kuzengereza: Anthu ena amazengereza kuchita upainiya wothandiza chifukwa amadziona kuti alibe luso polalikira. Ngati zimenezi n’zomwe zikukulepheretsani, Yehova angakuthandizeni monga mmene anachitira ndi Yeremiya. (Yer. 1:6-10) Ngakhale kuti Mose anali“wa m’kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera Yehova anam’gwiritsa ntchito kuchita chifuniro Chake.” (Eks. 4:10-12) Ngati mukudzikayikira, pempherani kwa Yehova kuti akulimbikitseni.
6. Kodi mungathe bwanji kuchita upainiya wothandiza ngakhale kuti mumavutika ndi matenda kapena ndinu wotanganidwa?
6 Kodi mumazengereza kulembetsa chifukwa cha kuvutika ndi matenda kapena kutanganidwa? Ngati ndinu wolemala, kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene mulili kungakuthandizeni kuti muthe kuchita upainiya wothandiza. Ngati ndinu otanganidwa kwambiri, mwina mungalinganize kuchita zinthu zosafunikira kwambiri mwezi wina. Anthu ena omwe akugwira ntchito ya tsiku lonse atha kupatula nthawi yochita upainiya wothandiza mwa kutenga tchuthi cha tsiku limodzi kapena awiri.—Akol. 4:5.
7. N’chifukwa chiyani n’kothandiza kupemphera kwa Yehova za kuchita upainiya wothandiza?
7 Zimene Mungachite: Muuzeni Yehova kuti mukufuna kuchita upainiya ndipo m’pempheni kuti akudalitseni pamene mukuyesayesa kuwonjezera utumiki wanu. (Aroma 12:11, 12) Angakuthandizeni kusankha bwino mukamasintha zinthu pandandanda yanu. (Yak. 1:5) Ngati mulibe chidwi chochita upainiya wothandiza, pemphani Yehova kukuthandizani kuti muzisangalala ndi ntchito yolalikira.—Luka 10:1, 17.
8. Kodi lemba la Miyambo 15:22 lingakuthandizeni motani kuti muthe kuchita upainiya wothandiza?
8 Kambiranani monga banja cholinga chochita upainiya wothandiza. (Miy. 15:22) Mwina a m’banja angathandize munthu mmodzi pabanjapo kuti achite upainiya wothandiza. Ndipo kambiranani ndi anthu ena mumpingo kuti mukufuna kuchita upainiya, makamaka aja amene ali ndi zolinga zofanana ndi zanu. Zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi chidwi kwambiri chofuna kuchita upainiya wothandiza.
9. Kodi ndi miyezi iti imene mungafune kuchita upainiya wothandiza?
9 Mukamaona ndandanda yanu yautumiki m’chaka cha utumiki chatsopano, kodi ndi liti pamene mukuganiza kuti mungachite upainiya wothandiza? Ngati mumagwira ntchito tsiku lonse kapena mumapita ku sukulu, mungaganizire za miyezi imene ili ndi tchuthi kapena imene ili ndi masiku a Loweruka ndiponso a Lamlungu asanu. Mwachitsanzo, miyezi ya September, December, March, ndi August ili ndi masiku a Loweruka ndiponso a Lamlungu asanu. Mwezi wa May uli ndi masiku a Loweruka asanu, ndipo mwezi wa June ulinso ndi masiku a Lamlungu asanu. Ngati mumavutika ndi matenda, onani miyezi imene nthawi zambiri imakhala ndi nyengo yabwino. Mungachitenso upainiya mwezi umene woyang’anira dera adzatumikira mpingo wanu. Ndipo nthawi imene iye azichezera mpingo wanu mudzakhala ndi mwayi wopezeka pa chigawo choyambirira cha msonkhano umene amachita ndi apainiya okhazikika. Popeza kuti chaka cha mawa Chikumbutso chidzachita pa March 22, miyezi ya March, April ndi May ingakhale yabwino kwambiri kuchita upainiya. Mukasankha mwezi kapena miyezi imene mukufuna kuchita upainiya wothandiza, mulembenso ndandanda imene idzakuthandizani kuti mukwanitse maola ofunika.
10. Kodi mungachite chiyani ngati mukuona kuti simungathe kuchita upainiya wothandiza?
10 Ngakhale kuti mukuona kuti m’chaka cha utumiki chikubwerachi simungathe kuchita upainiya, mungakhalebe ndi mzimu waupainiya. Pitirizani kuchita zonse zimene mungathe muutumiki, mukudziwa kuti Yehova amasangalala mukamamutumikira ndi mtima wonse. (Agal. 6:4) Thandizani ndiponso limbikitsani anthu amene akuchita upainiya wothandiza. Ndipo mwina mungasinthe ndandanda yanu kuti muzitumikira limodzi ndi amene akuchita upainiya tsiku limodzi lina pamlungu.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama muutumiki?
11 Anthu a Yehova akudziwa kuti ayenera kuchita khama. Tili ndi ntchito imene tifunikira kuchita ndipo ntchitoyi ndi yolalikira uthenga wabwino. Moyo wa anthu uli pangozi, ndipo nthawi yotsala ndi yochepa. (1 Akor. 7:29-31) Kukonda Mulungu ndi anansi athu kudzatilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe muutumiki. Tingathe kuchita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi m’chaka chautumiki chatsopano ngati tiyesetsa ndiponso kukonzekera bwinobwino kukadali nthawi. Kuchita zimenezi kungakhale cholinga chabwino kwambiri.