Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?
1. N’chifukwa chiyani nyengo ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kwambiri yowonjezera utumiki wathu?
1 Nyengo ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kwambiri yowonjezera utumiki wathu. Pa nthawi imeneyi, timaganizira kwambiri za chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza potitumizira Mwana wake kuti akhale nsembe ya dipo. (Yoh. 3:16) Zimenezi zimatichititsa kuti tiziyamikira kwambiri Yehova. Zimatichititsanso kuti tikhale ndi mtima wofunitsitsa kuuza ena za Yehovayo ndiponso zimene akuchitira anthu. (Yes. 12:4, 5; Luka 6:45) Pa nyengoyi timasangalalanso chifukwa timagwira ntchito yapadera yoitanira anzathu komanso anthu osiyanasiyana a m’gawo lathu ku mwambo wa Chikumbutso. Pambuyo pa Chikumbutso, timayesetsa kuthandiza anthu amene anafika pa mwambowu kuti chidwi chawo chipitirize kukula. Kodi inuyo simungawonjezere utumiki wanu pochita upainiya wothandiza m’miyezi ya March, April kapenanso May?
2. N’chifukwa chiyani tikunena kuti mwezi wa March ndi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza?
2 Mwezi wa March Ukhale Wapadera: Mwezi wa March ndi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza. Anthu amene adzalembetse upainiya adzakhala ndi mwayi wosankha kupereka maola 30 kapena 50. Komanso woyang’anira dera akadzachezera mpingo wanu m’mwezi umenewu, apainiya othandiza adzakhala ndi mwayi wokhala nawo pa msonkhano wonse umene iye amachita ndi apainiya okhazikika ndiponso apadera. Kuwonjezera pamenepa, ntchito yapadera yoitanira anthu ku mwambo wa Chikumbutso womwe udzachitike pa March 26, 2013, tidzaigwira kwa nthawi yaitali kuposa zaka za m’mbuyomu ndipo idzayamba pa March 1. Chinthu chinanso n’chakuti mwezi wa March uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu. Choncho, bwanji osaganizira zochita nawo upainiya wothandiza kuti mweziwu ukhale wapadera kwambiri chaka chino?
3. Kodi tingatani pokonzekera kuwonjezera utumiki wathu?
3 Yambani Panopa Kukonzekera: Ino ndi nthawi yabwino yoti muonenso bwinobwino ndandanda yanu kuti muone ngati mungasinthe zina n’zina kuti mudzathe kuchita upainiya. Kuti zimenezi zitheke, pamafunikanso kuchita zinthu mogwirizana ndi banja lanu lonse. Choncho pa kulambira kwanu kwa pabanja, patulani nthawi yoti mukambirane zolinga zimene banja lanu lili nazo ndipo kenako mukonze ndandanda. (Miy. 15:22) Ngati simungakwanitse kuchita upainiya wothandiza, musakhumudwe. Mukhoza kungosintha zinthu zina n’zina n’cholinga choti muzithera nthawi yambiri mu utumiki. Kuwonjezera pa Loweruka ndi Lamlungu, mukhoza kupatula tsiku lina limodzi mkati mwa mlungu kuti muzilowa mu utumiki.
4. Kodi tikawonjezera utumiki wathu m’miyezi ya March, April ndiponso May, tingapeze madalitso otani?
4 Tikawonjezera utumiki wathu m’miyezi ya March, April ndiponso May, tidzakhala ndi madalitso ambiri. Chimwemwe chomwe timakhala nacho chifukwa chotumikira Yehova komanso chifukwa chokhala ndi mtima wopatsa, chidzakula kwambiri. (Yoh. 4:34; Mac. 20:35) Chinthu chinanso chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amasangalala ndi mtima wathu wololera kudzimana zinthu zina n’cholinga chofuna kuthandiza ena.—Miy. 27:11.