Ndandanda ya Mlungu wa February 11
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 11
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 19-24 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu 26-28 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 27:24-44 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kuleza Mtima Kwa Mulungu Kukuthandiza Bwanji Kuti Anthu Adzapulumuke?—2 Pet. 3:9, 15 (Mph. 5)
Na. 3: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Mumakonda Kunena Kwambiri za Maulosi’—rs tsa. 390 ndime 8-tsa. 391 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 6:19-21 ndi Luka 16:13. Kenako mukambirane mmene malemba amenewa angatithandizire pa utumiki wathu.
Mph. 20: “Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Mukamaliza kukambirana ndime yachiwiri, funsani mwachidule ofalitsa awiri amene akonza zochita upainiya wothandiza m’mwezi wa March. Mmodzi akhale woti ali pa ntchito yolembedwa ndipo winayo akhale woti amadwaladwala kapena ndi wokalamba. Kodi adzasintha zinthu zotani pa moyo wawo kuti adzathe kuchita upainiya? Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu chitani chitsanzo chosonyeza mwamuna ndi mkazi wake kapena banja lokhala ndi ana likuchita kulambira kwa pabanja. Kenako akambirane zimene angachite kuti adzawonjezere utumiki wawo.
Nyimbo Na. 122 ndi Pemphero