Zochitika mu Utumiki Wakumunda
“Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zek. 8:23) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa chifukwa anthu ambiri akulowa m’gulu la anthu a Yehova. Chaka chatha panachitika misonkhano yachigawo 73 ndipo anthu amene anapezeka pamisonkhano imeneyi anali okwana 256,658. Tinasangalala kwambiri kuona anthu atsopano okwana 2,844 akubatizidwa m’madzi posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova.