Zimene Mungachite Kuti Mudzasangalale M’nyengo ya Chikumbutso
1. Kodi njira ina imene ingakuthandizeni kukhala wosangalala m’nyengo ya Chikumbutsoyi ndi iti?
1 Kodi mukufuna kudzasangalala kwambiri m’miyezi ya March, April ndi May? Chinthu chimodzi chimene chingakuthandizeni kuti mudzasangalale ndi kuwonjezera utumiki wanu pochita upainiya wothandiza ngati mungakwanitse. Kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji kukhala wosangalala?
2. Kodi kuchita zambiri mu utumiki kungatithandize bwanji kukhala osangalala?
2 Kuchita Zambiri mu Utumiki Kungakuthandizeni Kukhala Wosangalala Kwambiri: Yehova anatilenga m’njira yoti tizisangalala tikamamulambira komanso tikamapeza zosowa zathu zauzimu. (Mat. 5:3) Anatilenganso kuti tizisangalala chifukwa chopatsa anthu ena zinthu zathu. (Mac. 20:35) Kulalikira kumatithandiza kuchita zinthu ziwiri zonsezi, zomwe ndi kulambira Mulungu komanso kuthandiza anthu. N’zosadabwitsa kuti munthu amene amalalikira kwambiri amakhalanso wosangalala kwambiri. Komanso, tikamalalikira kwambiri timawonjezera luso lathu mu utumiki. Ndipo tikakhala ndi luso limeneli timachepetsa mantha. Tikamathera nthawi yambiri tikuchita utumiki timakhala ndi mwayi wolalikira kwa anthu ambiri komanso woyambitsa maphunziro a Baibulo. Zonsezi zimapangitsa kuti tizisangalala tikakhala mu utumiki.
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mwezi wa March komanso April ndi nthawi yabwino kuchita upainiya wothandiza?
3 March komanso April ndi miyezi yabwino kwambiri kudzachita upainiya wothandiza chifukwa tingasankhe kudzachita upainiya wa maola 30 kapena 50. Komanso, kungoyambira Loweruka pa March 22 mpaka tsiku la Chikumbutso, Lolemba pa April 14, tidzakhala ndi mwayi wogwira nawo ntchito yoitanira anthu ku mwambowu. Mpingo uliwonse udzasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi “mogwirizana” pomwe uzidzayesetsa kugawira timapepalati m’gawo lake lonse pa nthawiyi.—Zef. 3:9.
4. Kodi mungachite chiyani ngati mukufuna kudzachita upainiya wothandiza?
4 Yambani Kukonzekera Panopa: Ngati simunayambe kukonzekera, mungachite bwino kuonanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu komanso kuona zimene mungasinthe kuti mudzachite zambiri pa nyengo imeneyi. Mungachite bwinonso kuipempherera nkhaniyi. (Yak. 1:5) Kambiranani nkhaniyi ndi anthu a m’banja lanu komanso ena mumpingo. (Miy. 15:22) Mungadabwe kuona kuti ngakhale kuti mumadwaladwala kapena mumapanikizika ndi ntchito, inunso mungathe kuchita upainiya wothandiza.
5. Tikadzachita zambiri mu utumiki pa nyengo ya Chikumbutso, kodi zotsatira zake zidzakhala zotani?
5 Yehova amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (Sal. 32:11) Tikadzayesetsa kuwonjezera zochita mu utumiki pa nyengo ya Chikumbutso, tidzasangalala kwambiri komanso tidzasangalatsa Atate wathu wakumwamba.—Miy. 23:24; 27:11.