Ndandanda ya Mlungu wa February 24
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 24
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 32-35 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani. Fotokozani zimene mpingo wanu udzachite zokhudza utumiki wakumunda Loweruka loyamba m’mwezi wa March. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro pogwiritsa ntchito chitsanzo chomwe chili patsamba 4.
Mph. 15: Kufunika Kochita Khama. Nkhani yochokera mu Buku Lapachaka la 2013, tsamba 45, ndime 1, mpaka tsamba 46 ndime 1, komanso tsamba 136 mpaka 137. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: “Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 22.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Perekani timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso kwa onse, ndipo kambiranani zomwe zili m’kapepalako. Tchulani mfundo zimene zingagwire ntchito pa mpingo wanu, zimene zili m’kalata ya malangizo yopita kwa akulu, ndipo fotokozani zimene mpingo wakonza, kuti mudzathe kugawira timapepalati m’gawo lanu lonse.
Nyimbo Na. 109 ndi Pemphero