Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 22
Chaka chino ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso idzayamba Loweruka pa March 22. Tonse tikulimbikitsidwa kuti tidzagwire nawo ntchitoyi. Kumapeto kwa mlungu, tizidzagawiranso magazini atsopano kwa anthu amene asonyeza chidwi. Loweruka loyamba la mwezi wa April, ntchito yaikulu idzakhala kugawira timapepalati m’malo moyambitsa maphunziro a Baibulo. Komabe, tikapeza munthu wachidwi, tidzayesetse kuyambitsa phunziro. Woyang’anira utumiki angaone ngati kulalikira m’malo amene mumapezeka anthu ambiri kungathandize kuti mpingo wawo ufikire anthu ambiri a m’gawo lawo. Panopa lembani mayina a anthu amene mumadziwana nawo, achibale, omwe mumagwira nawo ntchito, maulendo obwereza komanso anzanu a kusukulu amene mukufuna kuti adzapezeke pa mwambowu, n’cholinga choti tikadzayamba ntchitoyi mudzawapatse kapepala kowaitana. Tikukhulupirira kuti anthu ambiri adzakhala nafe pa mwambo wokumbukira chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza anthufe.—Yoh. 3:16; 15:13.