Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 1
1. Kodi ntchito yapadera yoitanira anthu ku mwambo wa Chikumbutso idzayamba liti, ndipo n’chifukwa chiyani chaka chino ntchitoyi ichitike kwa nthawi yaitali?
1 Lachisanu, pa March 1, tidzayamba ntchito yapadera yomwe timaigwira chaka ndi chaka, yoitana anthu kuti adzakhale nafe pa mwambo wa Chikumbutso. Mwambo wa Chikumbutso udzachitika pa March 26, ndipo izi zikutanthauza kuti ntchito yapaderayi ichitika kwa nthawi yaitali poyerekezera ndi zaka za m’mbuyomu. Zimenezi zitipatsa mwayi woti tiitane anthu ochuluka, makamaka ngati mpingo wathu uli ndi gawo lalikulu kwambiri.
2. Kodi pali dongosolo lotani pa nkhani yotenga timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso ndiponso kugawira timapepalati?
2 Ntchitoyi Idzachitike Mwadongosolo: Akulu adzapereka malangizo okhudza mmene tingagwirire ntchitoyi m’gawo lonse. Iwo adzafotokozanso ngati zili zoyenera kusiya timapepalati panyumba zimene sitinapezepo anthu. Ngati tagawira timapepalati panyumba iliyonse ya m’gawo lathu ndipo timapepala tina tatsala, tikhoza kugawira mu ulaliki wathu wamunsewu kapena m’malo amene mumapezeka anthu ambiri. Woyang’anira utumiki adzaonetsetsa kuti timapepala tolembedwa mooneka bwino tiziikidwa pakauntala ya mabuku kapena ya magazini kuti ofalitsa azitha kutenga. Komabe, simuyenera kuika pakauntala timapepala tonse nthawi imodzi. Mlungu uliwonse, wofalitsa aliyense azitenga timapepala timene angagawire kwa mlungu wokhawo basi.
3. Kodi tiyenera kukumbukira mfundo ziti tikamagawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso?
3 Kodi Tizidzalankhula Zotani? Ndi bwino kulankhula mwachidule kwambiri n’cholinga choti tilankhule ndi anthu ambiri. Patsamba 4 pali chitsanzo chosonyeza zimene tinganene pogawira timapepalati m’gawo lathu. Komabe, sitikufunikira kuthamanga kwambiri tikapeza mwininyumba amene ali ndi chidwi kwambiri kapena amene ali ndi mafunso. Tikamagawira timapepalati Loweruka ndi Lamlungu, tizidzagawiranso magazini ngati zili zoyenera kutero. Koma pa March 2, tidzagwira ntchito yogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso m’malo moyambitsa maphunziro a Baibulo.
4. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kugwira nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso?
4 Tikukhulupirira kuti anthu ambiri amene tidzawaitane adzabwera ku Chikumbutso. Nkhani yomwe idzakambidwe idzafotokoza bwino kuti Yesu ndi ndani kwenikweni. (1 Akor. 11:26) Idzafotokozanso mmene imfa yake imatithandizira. (Aroma 6:23) Komanso nkhaniyi idzafotokoza momveka bwino chifukwa chake zili zofunika kwambiri kuti tiziganizira ndiponso kukumbukira zimene Yesu anatichitira. (Yoh. 17:3) Choncho, tiyeni tonsefe tiyesetse kugwira nawo mwakhama ntchito imeneyi yoitanira anthu ku Chikumbutso.