Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2
1. Kodi tidzayamba liti kugawira timapepala toitanira ku Chikumbutso chaka chino, ndipo kodi ntchito yapachaka imeneyi ndi yofunika bwanji?
1 Kuyambira pa April 2 mpaka pa April 17, tidzakhala tikugawira timapepala toitanira anthu ku mwambo wofunika kwambiri pa chaka, umene ndi Chikumbutso cha imfa ya Khristu. M’mbuyomu anthu ambiri achidwi anabwera kudzakhala nawo pa mwambowu titawaitana pa nthawi ya ntchito yapachaka imeneyi. Mwachitsanzo, pa tsiku la Chikumbutso, mayi wina anaimba telefoni ku ofesi ya nthambi. Iye anati: “Ndangofika kumene panyumba ndipo ndapeza kapepala kondiitanira ku Chikumbutso pansi pa chitseko. Ndikufuna ndipiteko, koma sindinamvetse za nthawi yake yeniyeni.” M’bale amene anayankha telefoniyo anafotokoza pamene panalembedwa nthawi pa kapepalako. Pamapeto pake, mayiyo analonjeza kuti, “Madzulo ano ndipita ku mwambo wanuwu.”
2. Kodi tinganene chiyani pogawira kapepala koitanira ku Chikumbutso?
2 Mmene Tidzagwirire Ntchitoyi: Popeza tili ndi nthawi yochepa yoti tigawire timapepalati m’gawo lathu lonse ndi bwino kulankhula mwachidule. Mwina tinganene kuti: “Takupezani. Ife tikuitana banja lanu lonse ku mwambo wofunika kwambiri umene umachitika kamodzi pa chaka. Chaka chino mwambo umenewu udzachitika Lamlungu pa April 17 padziko lonse lapansi. [Kenako perekani kapepalako kwa mwininyumbayo.] Tsiku limeneli tidzakumbukira imfa ya Yesu. Pa mwambowu padzakambidwa nkhani yochokera m’Baibulo imene idzafotokoze mmene tingapindulire ndi dipo la Yesu. Kapepalaka kakusonyeza malo ndi nthawi imene msonkhowu udzachitike m’dera lathu lino.”
3. Kodi tingachite chiyani kuti tiitane anthu ambiri ku Chikumbutso?
3 Ngati mpingo wanu uli ndi gawo lalikulu, akulu angakuuzeni ngati mungafunike kusiya timapepalati panyumba zimene simunapezepo anthu, koma pamalo osaokera kwa wina aliyense. Onetsetsani kuti mwaitana anthu amene mumakachitako maulendo obwereza, achibale, amene mumagwira nawo ntchito, anzanu a kusukulu ndiponso amene mumacheza nawo. Pamene mukugawira timapepalati kumapeto kwa mlungu, mukhozanso kugawira magazini pamene pakufunikira kutero. Kodi mungachite upainiya wothandiza mwezi wa April kuti muchite nawo zambiri pa ntchito yosangalatsa imeneyi?
4. N’chifukwa chiyani tikufuna kuti anthu achidwi adzapezeke pa Chikumbutso?
4 Anthu achidwi amene adzabwere pa mwambowu adzalimbikitsidwa kwambiri. Adzamva za chikondi chimene Yehova anasonyeza popereka dipo. (Yoh. 3:16) Adzaphunzira mmene Ufumu wa Mulungu udzapindulitsira anthu. (Yes. 65:21-23) Adzalimbikitsidwanso kuti akumane ndi akalinde kuti apemphe munthu woti aziphunzira nawo Baibulo kuti adziwe zambiri. Tikukhulupirira kuti anthu ambiri a mtima wabwino ndiponso achidwi adzabwera pa tsiku la Chikumbutso.