Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/10 tsamba 1
  • Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 22
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 2/10 tsamba 1

Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso

1. Kodi ndi ntchito iti yapadera yomwe ichitike pokonzekera mwambo wa Chikumbutso?

1 Yesu anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” (Luka 22:19) Pomvera lamulo limeneli, anthu olambira Yehova adzasonkhana pamodzi ndi anthu achidwi pa March 30, 2010, kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Ndipo kuyambira pa March 13 mpaka pa March 30, tikhala tikugawira timapepala tapadera toitanira anthu kumwambo umenewu.

2. Kodi tizitani pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso?

2 Mmene Mungagawirire: Mungapereke kapepalako kwa mwininyumba kuti aone zithunzi ndiyeno munganene kuti: “Pa March 30 madzulo, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi adzasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Ndabwera kudzakupatsani kapepala kanu pamodzi ndi banja lanu, kokuitanirani kumwambo umenewu. Mukhoza kubweranso ndi a zinzanu.” Ngati nˈzotheka mungawerenge lemba la Luka 22:19 kuti aone lamulo limene limatiuza kuchita mwambowu. Mungamuuzenso nthawi ndi malo kumene kuchitikire mwambowu kwanuko. Koma ndi bwino kuchita zimenezi mwachidule chifukwa musaiwale kuti tili ndi nthawi yochepa yoti tigawire timapepalati m’gawo lathu lonse.

3. Kodi ndi anthu ati amene tingawaitane?

3 Ngati mpingo wanu uli ndi gawo lalikulu, akulu akhoza kuuza ofalitsa kuti azisiya timapepalati panyumba zimene sanapezepo anthu paulendo woyamba. Ngati m’poyenera, mungagawirenso magazini pamodzi ndi kapepalaka. Yesetsani kuitana anthu achidwi amene munapangako maulendo obwereza, amene mumaphunzira nawo Baibulo, anzanu akuntchito, kusukulu, achibale, oyandikana nawo nyumba ndiponso anthu amene mumadziwana nawo.

4. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chikondi cha Yehova potipatsa nsembe ya dipo?

4 Konzekerani Kuwonjezera Utumiki: Nthawi ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kwambiri yowonjezera zimene timachita mu utumiki. Kodi mungasinthe zinan’zina pamoyo wanu kuti muthe kuchita upainiya wothandiza? Kodi muli ndi ana kapena anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo omwe akupita patsogolo mwauzimu? Ngati zili choncho, uzani akulu kuti aone ngati ana kapena anthuwo ali oyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa n’cholinga choti agwire nawo ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso. Kuyamikira Yehova chifukwa choti anatikonda potipatsa nsembe ya dipo, kutichititsa kupezeka pa Chikumbutso komanso kuitana anthu ambiri, mmene tingathere, kuti adzakhale nawo pamwambowu.—Yohane 3:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena