Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17
1. Tchulani ntchito yapadera imene idzayambe pa March 17.
1 Chaka chilichonse, mwambo wa Chikumbutso umatithandiza kulengeza imfa ya Yesu. (1 Akor. 11:26) Choncho, tikufuna kuti anthu ena adzapezeke nawo pa Chikumbutso ndiponso kumvetsera nawo mmene Yehova anaperekera mwachikondi mphatso ya dipo. (Yoh. 3:16) Chaka chino, ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso idzayamba Loweruka pa March 17. Kodi mwakonzekera kudzagwira nawo mokwanira ntchito imeneyi?
2. Kodi tinganene chiyani pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso?
2 Zimene Tinganene: Zingakhale bwino kulankhula mwachidule. Tinganene kuti: “Takupezani. Tabwera kuti tidzakupatseni kapepala aka kokuitanirani inuyo ndi banja lanu lonse ku mwambo wofunika kwambiri umene umachitika kamodzi pa chaka. Chaka chino mwambowu udzachitika pa April 5 padziko lonse lapansi. Pa mwambowu padzakambidwa nkhani yochokera m’Baibulo yofotokoza phindu la imfa ya Yesu ndiponso zimene Yesuyo akuchita panopo. Kapepala aka kakusonyeza malo ndi nthawi imene mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino.” Pamene tikugawira timapepalati kumapeto kwa mlungu, tikhozanso kugawira magazini pakafunikira kutero.
3. Koti tingachite chiyani kuti tiitanire anthu ambiri ku Chikumbutso?
3 Itanani Anthu Ambiri Mmene Mungathere: Cholinga chathu ndi kuitana anthu ambiri mmene tingathere. Choncho, onetsetsani kuti mwaitana anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo, amene mumakachitako maulendo obwereza, achibale, amene mumagwira nawo ntchito, anzanu a kusukulu, oyandikana nawo nyumba ndiponso amene mumacheza nawo. Akulu adzakupatsani malangizo a zimene mungachite kuti mugawire timapepalati m’gawo lanu lonse. Ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutsoyi imakhala ndi zotsatira zabwino. Chaka chatha, mayi wina atafika pamalo a msonkhanowu, kalinde wina anauza mayiyo kuti akhoza kumuthandiza kuti akumane ndi munthu amene anamuitana. Koma mayiyu anafotokoza kuti palibe munthu wina aliyense amene akumudziwa pa msonkhanowo. Iye anati analandira kapepala koitanira anthu ku mwambowu kwa munthu wina amene anali kuyenda khomo ndi khomo m’mawa wa tsiku limenelo.
4. Tchulani zifukwa zotichititsa kugwira nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso?
4 Mwinatu munthu wina adzabwera pa Chikumbutso chifukwa cha kapepala kamene inuyo mungagawire. Kaya munthu wina adzabwera kapena ayi, koma kudzipereka kwanu kudzakhala umboni wapadera. Timapepala timene mudzagawire tidzalengeza kuti tsopano Yesu ndi mfumu yamphamvu. Mukadzagwira nawo mwakhama ntchito imeneyi mudzasonyeza onse okuonani, monga anthu a m’gawo lanu, ofalitsa anzanu ndiponso makamaka Yehova, kuti mumayamikira kwambiri mphatso ya dipo.—Akol. 3:15.