Ndandanda ya Mlungu wa February 20
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 20
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 2 ndime 8-15 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 58-62 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 61:1-11 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Kudzipereka Kwathu kwa Mulungu Chili Chizindikiro Choti Timamukonda Ndiponso Kumukhulupirira? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mulungu Amakuona Bwanji Kupatukana?—rs tsa. 385 ndime 4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Tchulani buku logawira m’mwezi wa March ndipo chitani chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene tingagawirire bukulo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Salimo 63:3-8 ndi Maliko 1:32-39. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 15: “Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17.” Mafunso ndi mayankho. Gawirani kapepala kamodzi koitanira ku Chikumbutso kwa aliyense, kenako mukambirane zimene zili m’kapepalako. Mukamakambirana ndime 2, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene mungagawirire kapepalaka. Mukamakambirana ndime 3, pemphani woyang’anira utumiki kuti afotokoze zimene zakonzedwa kuti mugawire timapepalati m’gawo la mpingo wanu.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero