Konzekerani Panopo Kuwonjezera Utumiki Wanu
1. Kodi nyengo ya Chikumbutso imatipatsa mwayi wotani, ndipo tingakonzekere bwanji?
1 Chaka chilichonse nyengo ya Chikumbutso imatipatsa mwayi ‘wotamanda kwambiri Yehova.’ (Sal. 109:30) Kodi inuyo muwonjezera utumiki wanu m’mwezi wa March monga njira imodzi yosonyezera kuti mumayamikira Mulungu amene ndi Wopereka dipo? Inotu ndi nthawi yabwino yoti muyambe kukonzekera.—Miy. 21:5.
2. Kodi inuyo ndiponso ena munamva bwanji ndi kuchepetsedwa kwa maola a upainiya wothandiza m’mwezi wa April chaka chatha?
2 Upainiya Wothandiza: Chaka chatha, abale ndi alongo anasangalala kwambiri atamva kuti akhoza kuchita upainiya wothandiza wa maola ochepa m’mwezi wa April. M’bale wina analemba kuti: “Panopo ndikuphunzira kusekondale ndipo zakhala zikundivuta kuchita upainiya wokhazikika. Tsopano ndilembetsa upainiya wa maola 30, koma ndiyesetsa kuti ndidzakwanitse maola 50 m’mwezi wa April.” Mlongo wina amene amagwira ntchito anati: “Maola 30! Amenewa okha ndiye ndikwanitsa.” Atalengeza za upainiya wothandiza wa maola ochepawu, munthu wina amene kale anali mpainiya ndipo panopa ali ndi zaka zopitirira 80 anati: “Imeneyi ndi nthawi imene ndakhala ndikuyembekezera. Yehova akudziwa kuti nthawi imene ndakhala ndikusangalala kwambiri pa moyo wanga ndi imene ndinkachita upainiya.” Ena amene sanakwanitse kuchita upainiya wothandiza anachita zambiri mu utumiki.
3. Tchulani zifukwa zimene tingachitire upainiya wothandiza m’miyezi ya March, April ndi May?
3 Chaka chino, mwezi wa March ndi mwezi wabwinonso kuchita upainiya wothandiza chifukwa tikhalanso ndi mwayi wopereka maola 30 kapena 50. Kuwonjezera pamenepa, kuyambira Loweruka pa March 17, tidzakhala ndi mwayi wogwira nawo ntchito yapadera yoitanira anthu ku mwambo wa Chikumbutso umene udzachitike pa April 5. Ofalitsa ambiri adzasangalala kuchita zambiri mu utumiki moti adzafuna kuchita upainiya wothandiza wa maola 50 m’miyezi ya April ndi May.
4. Kodi tingatani kuti tichite zambiri mu utumiki ndipo pangakhale zotsatira zotani?
4 Mukamadzachita Kulambira kwa Pabanja mlungu wamawa, bwanji osadzakambirana zimene aliyense m’banja mwanu angachite kuti awonjezere utumiki wake pa nyengo ya Chikumbutso? (Miy. 15:22) M’pempheni Yehova kuti adalitse khama lanu. (1 Yoh. 3:22) Pamene mukuchita zambiri mu utumiki, mudzakhala mukutamanda kwambiri Yehova komanso mudzakhala wosangalala kwambiri.—2 Akor. 9:6.