Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/13 tsamba 2
  • Mwayi Winanso Wotamanda Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwayi Winanso Wotamanda Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Konzekerani Panopo Kuwonjezera Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 6/13 tsamba 2

Mwayi Winanso Wotamanda Yehova

1. Kodi pakonzedwa zotani zimene zingatithandize kuti ‘tizitamanda kwambiri Yehova’?

1 Kuyambira mwezi wa March chaka chino, ofalitsa akumakhala ndi mwayi wochita upainiya wothandiza wa maola 30 m’miyezi ya March ndi April komanso pa nthawi imene woyang’anira dera akuchezera mpingo wawo. Ngati masiku amene woyang’anira dera akuchezera mpingo akuyambira m’mwezi wina kukathera m’mwezi wina, ofalitsa amene akufuna kuchita upainiya wothandiza wa maola 30, angasankhe kuchita upainiyawo m’mwezi uliwonse pa miyezi iwiriyo. Apainiya onse othandiza angakhale nawo pa msonkhano wonse umene woyang’anira dera amachita ndi apainiya okhazikika komanso apadera. Izi zikutanthauza kuti, ngati poyamba sitinkatha kukwanitsa kuchita upainiya wa maola 50, tsopano tingathe ‘kutamanda kwambiri Yehova’ pochita upainiya wothandiza wa maola 30 kanayi pa chaka.—Sal. 109:30; 119:171.

2. Kodi amene azichita upainiya pa nthawi imene woyang’anira dera akuchezera, azikhala ndi mwayi wotani?

2 Pa Nthawi Imene Woyang’anira Dera Akuchezera Mpingo Wanu: Ofalitsa ambiri azikhala ndi mwayi wochita upainiya wothandiza pa nthawi imene woyang’anira dera akuchezera mpingo wawo ndipo azilimbikitsana naye akayendera limodzi mu utumiki. (Aroma 1:11, 12) Apainiya ena othandiza amene ali pa ntchito, angakonze zotenga ofu tsiku limodzi mkati mwa mlungu n’cholinga choti adzayende mu utumiki ndi woyang’anira dera. Ena angamupemphe kuti adzayende naye mu utumiki Loweruka kapena Lamlungu. Komanso apainiya othandiza azilimbikitsidwa kwambiri akakhala nawo pa msonkhano limodzi ndi apainiya okhazikika.

3. N’chifukwa chiyani tingati nthawi ya Chikumbutso ndi yabwino kuchita upainiya wothandiza?

3 M’mwezi wa March ndi April: Ofalitsa amene ankachita upainiya wa maola 30 mwezi umodzi pa nthawi ya Chikumbutso, tsopano ali ndi mwayi wowonjezera ‘nsembe zimene amapereka potamanda’ Mulungu. (Aheb. 13:15) Miyezi iwiri yonseyi, wa March ndi wa April, ndi nthawi yabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza. Chaka chilichonse pa nthawiyi, timagwira ntchito yosangalatsa kwambiri yogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Komanso popeza pa nthawi ya Chikumbutso ofalitsa ambiri amakonda kuwonjezera nthawi imene amalowa mu utumiki, tingakhale ndi mwayi woyenda mu utumiki ndi anthu osiyanasiyana. Pambuyo pa Chikumbutso, timabwereranso kwa anthu amene anafika pa mwambowu n’cholinga choti tikawalimbikitse kuti adzabwerenso ku nkhani yapadera ya onse. Kodi simungakonde kugwiritsa ntchito mwayi umenewu kuchita upainiya wothandiza?—Luka 6:45.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena