Ndandanda ya Mlungu wa February 27
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 27
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 2 ndime 16-23 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 63-66 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa March.
Mph. 15: Thandizani Anthu Amene Sakhulupirira Baibulo. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 58 mpaka 62. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri.
Mph. 10: “Dzina la Mulungu Liyeretsedwe.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani masiku a msonkhano wadera ngati akudziwika.
Nyimbo Na. 100 ndi Pemphero