‘Dzina la Mulungu Liyeretsedwe’
1. Kodi mutu wa msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2012 ndi woti chiyani ndipo wachokera pati?
1 Tilitu ndi mwayi waukulu wodziwika ndi dzina la Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova. Mulungu ndi amene anatipatsa dzina lakeli. Kuyambira m’chaka cha 1931, ifeyo monga Mboni za Yehova, takhala tikudziwika ndi dzina lapadera la Yehova. (Yes. 43:10) Yesu, yemwe ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, ankaona dzina la Mulungu kukhala lofunika kwambiri ndipo analiika pamalo oyamba m’pemphero lachitsanzo. (Mat. 6:9) Mawu a Yesu amenewa ndi pamene pachokera mutu wa msonkhano wathu wadera wa chaka chautumiki cha 2012. Mutu wake ndi wakuti, “Dzina la Mulungu Liyeretsedwe.” Ngati mukudziwa masiku a msonkhano wanu wadera, kodi mwalemba kale pakalendala yanu ndiponso mwayamba kukonzekera kuti mukapezekepo?
2. Kodi tiyembekezere kukaphunzira zotani ku msonkhano wadera?
2 Zimene Tikamve: Loweruka, tikamvetsera nkhani yakuti, “Dziwitsani Ena Dzina la Mulungu Pochita Utumiki wa Nthawi Zonse.” Nkhani imeneyi ikafotokoza chifukwa chake utumiki wa nthawi zonse uli wopindulitsa pa moyo. Tikamvetseranso nkhani yosiyirana ya mutu wakuti, “Pewani Kunyozetsa Dzina la Yehova.” Nkhani imeneyi idzatithandiza kupewa misampha inayi imene ingatikole. Nkhani ya mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Dzina la Mulungu Liyenera Kuyeretsedwa?” idzayankha mafunso akuti, Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kulalikira mwakhama ngakhale pamene anthu sakuonetsa chidwi kwenikweni? ndiponso lakuti, N’chiyani chingatithandize kuti tizichita utumiki mogwira mtima? Lamlungu, tidzamvetsera nkhani yosiyirana ya mbali zinayi imene idzafotokoze mmene tingayeretsere dzina la Mulungu mwa zimene timaganiza, zolankhula zathu, zosankha zathu ndiponso khalidwe lathu. Alendo amene adzabwere adzasangalala kumvetsera nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Yehova Adzayeretsa Dzina Lake pa Aramagedo.”
3. Kodi tili ndi mwayi wotani ndipo msonkhano wadera udzatithandiza bwanji?
3 Posachedwapa, Yehova achitapo kanthu kuti ayeretse dzina lake. (Ezek. 36:23) Padakali pano, tili ndi mwayi wopititsa patsogolo zinthu zonse zimene dzina la Yehova limaimira. Tikukhulupirira kuti msonkhano wadera umenewu udzathandiza aliyense wa ife kukwaniritsa udindo wathu waukulu wodziwika ndi dzina la Mulungu.