Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
1 Kuyambira m’September, mutu wa misonkhano yadera udzakhala wakuti “Imvani Mawu a Mulungu ndi Kuphunzira Kuwachita.” Mutu umenewu, wozikidwa pa Deuteronomo 31:12, 13, ukupereka maziko oyenera a programu yonse osonyezera maphunziro amene tifunikira kuwaphunzira ndi kuwagwiritsira ntchito.
2 Ngakhale kuti anthu ambiri lerolino amamvetsera mawu ouziridwa onyenga, pali kufunika kwakukulu kwakuti aliyense wa ife amve Mawu a Mulungu ndi kuphunzira kuwachita. (Luka 11:28; 1 Tim. 4:1) Programu ya msonkhano wadera yakonzedwa ndi cholinga chimenechi, kuti ipereke chilimbikitso ndi chithandizo kwa ofalitsa, mabanja, akulu, ndi apainiya. Pa Loŵeruka, padzakhala nkhani yosiyirana ya mbali zinayi yamutu wakuti “Kulimbana ndi Mavuto Athu—Mwa Kutchera Khutu ku Mawu a Mulungu.” Ndipo pa Sande mmaŵa, padzakhala nkhani yosiyirana yamutu wakuti “Mmene Malemba Amalangizira m’Chilungamo.” Programu yonse idzapereka chilimbikitso chauzimu chimene inu ndi banja lanu simuyenera kuphonya.
3 Pa Loŵeruka ndi pa Sande pomwe, padzaperekedwa malingaliro othandiza okhudza utumiki wakumunda limodzi ndi zitsanzo zake. Padzakhalanso zokumana nazo zolimbikitsa ndi zophunzitsa ndi kufunsa. Chotero, mwa kupezekapo ndi kumvetsera ndi cholinga cha kukagwiritsira ntchito zimene mudzaphunzira, mudzakhala m’malo abwino akutsatira mokwana malamulo a Mawu a Mulungu.
4 Mbali ina yapadera pamsonkhano waderawo idzakhala ubatizo wa abale ndi alongo odzipatulira chatsopano. Chilengezo chapoyera cha kudzipatulira kwawo chimenechi chikali kutali, ofuna ubatizo ayenera kuuza woyang’anira wotsogoza za chikhumbo chawo cha kubatizidwa kuti iye apange makonzedwe akuti akulu aonane nawo.
5 Nkhani yapoyera ya misonkhano yadera imeneyi ili ndi mutu wakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kutsogozedwa ndi Baibulo?” Itanani anthu okondwerera kuti adzapezekepo. Poyembekezera chilimbikitso ndi chithandizo chofunika kwambiri chimene inu ndi banja lanu mudzalandira, pangani makonzedwe otsimikizirika akuti mudzapezekepo pa programu yonse.