Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
1 Mutu umene udzakambidwa m’programu yatsopano ya msonkhano wadera yoyambira mu September n’ngwakuti “Dikirani, Chirimikani, Limbikani.” Wazikidwa pa mawu a mtumwi Paulo achilimbikitso kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba olembedwa pa 1 Akorinto 16:13.
2 Programuyo idzayamba mwa kufotokoza kufunikira kwathu kwa kudzipenda kwauzimu kosalekeza. Kusunga kaimidwe kolimba pa chimene chili chabwino mu “masiku otsiriza” ano kumafunikiritsa kupenda moona mtima unansi wathu ndi Yehova ndi kaimidwe kathu ndi gulu lake la padziko lapansi. (2 Tim. 3:1) Tidzakumbutsidwa za chiyamikiro cha Mulungu kaamba ka ntchito yathu yonse yamphamvu. Tifunikira kulangizidwa za mmene tingawongolere mikhalidwe yathu Yachikristu ndi kusunga khalidwe labwino.
3 Kufunika kwa kukhala achangu mu ntchito ya kupanga ophunzira pamene tikukalimira kupita patsogolo kwauzimu ndi mathayo kudzagogomezeredwanso. Malingaliro othandiza onena za mmene munthu aliyense payekha ndi mabanja angasungire programu yokhazikika ya kudya mwauzimu adzaperekedwa m’nkhani zosiyanasiyana, zitsanzo, ndi makambitsirano.
4 Pa Loŵeruka oyembekezera ubatizo oyenerera adzakhoza kupanga chilengezo chapoyera cha kudzipatulira kwawo mwa ubatizo wa m’madzi. Ndiyeno, pa Sande tonsefe tidzafuna kukhalapo kaamba ka nkhani yapoyera, ya mutu wakuti “Kodi Kaimidwe Kanu ndi Mulungu Nkotani?”
5 Programuyo idzamalizidwa ndi chilimbikitso cha kukhalabe ochirimika m’chikhulupiriro, ochitirana wina ndi mnzake mu mzimu wa chikondi ndi mtendere nthaŵi zonse. Msonkhano wadera uli umodzi wa mipata yapadera imene Yehova amagaŵira kwa tonsefe kuti “tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24, 25) Pangani makonzedwe otsimikizirika a kupezekapo pa programu yonse pa masiku onse aŵiri.