Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
1 Programu yatsopano ya msonkhano wadera kuyambira mu September idzakhala ndi mutu wakuti “Pezani Chimwemwe Chachikulu m’Kupatsa.” (Mac. 20:35) Chimwemwe chafotokozedwa kukhala “mkhalidwe wa kupeza bwino ndi chikhutiro.” Anthu ochuluka lerolino amagwiritsira ntchito chikondwerero chilichonse chimene angapeze m’moyo, ndipo pamene atero, kaŵirikaŵiri chimakhala chakanthaŵi. Chimenecho sindicho chimwemwe choona. Komabe, Yehova amatiphunzitsa mmene tingapindulire ife eni kosatha. (Yes. 48:17; 1 Yoh. 2:17) Programu yatsopano ya msonkhano wadera idzagogomezera mmene tingapezere chimwemwe chachikulu mwa kupatsa mwauzimu.
2 Tidzaphunzira njira zothandiza m’zimene tingadziperekere ife eni mu utumiki. Zina za nkhani zimene zidzaperekedwa ndi oyang’anira oyendayenda zili ndi mitu yakuti: “Kupanga Mabwenzi ndi Chuma Chosalungama,” “Lemekezani Makonzedwe a Mulungu a ‘Mphatso za Amuna,’” ndi “Landirani Mbali Zambiri za Chimwemwe Choona.” Awo amene akufuna kubatizidwa pamsonkhanowu ayenera kuuza woyang’anira wotsogoza kuti iyeyo asankhe akulu aŵiri openda nawo mafunso aubatizo. Kutumikira Yehova mu unansi woyera kudzabweretsa chimwemwe chachikulu kwa obatizidwa chatsopano.
3 Kuzindikira moyenera ulamuliro wa Yehova kumabweretsanso chimwemwe choona ndi chisungiko. Anthu onse afunikira kudziŵa zimenezi. Nchifukwa chake, nkhani yaikulu pamsonkhano wadera idzafotokoza mutu wakuti “Gwirizanani ndi Anthu a Mulungu Achimwemwe.” Tsimikizirani kuitana awo onse amene asonyeza chidwi pa choonadi kufika pa nkhani imeneyi. Sanapeze chisungiko chenicheni ndi chimwemwe chokhalitsa mu ulamuliro wa anthu m’dziko lino limene likugona mu mphamvu ya Satana. (Mlal. 8:9) Koma ndi chisangalalo chotani nanga chimene adzapeza pa kukhala oyanjana ndi anthu achimwemwe a Yehova!—Sal. 144:15b.
4 Mosasamala kanthu za mikhalidwe yomaipa mowonjezereka m’dongosolo lino la zinthu, awo amene ali ndi chimwemwe chachikulu m’kupatsa mwauzimu sadzagwiritsidwa mwala ndi Mulungu wachimwemwe. (1 Tim. 1:11, NW) Programu yatsopano ya msonkhano wadera idzasonyeza zimenezi kukhala choncho. Musaiphonye!