Pologalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
Kodi ndi mapindu otani amene mumapeza pakali pano chifukwa choyenda ndi Yehova? Kodi mungakanize motani chiyeso choti n’kulola zinthu zimene sizili zateokalase zichotse zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’moyo wanu? (Mat. 6:33) Kodi zimakuvutani kusiyanitsa chabwino ndi choipa m’dziko limene limapangitsa choipa kuoneka chabwino? (Aheb. 5:14) Mfundo zimenezi zikakambidwa kumsonkhano wadera wakuti “Pindulani Tsopano Lino mwa Kuyenda m’Njira za Mulungu,” kuyambira mu September 1999.—Sal. 128:1.
Chochitika chatsopano tsiku Loŵeruka pamsonkhano wadera umenewu ndi chitsanzo cha Msonkhano wa Utumiki. Woyang’anira dera wanu adzadziŵitsa mipingo zimene zakonzedwa kotero kuti onse adzabwere okonzeka kusangalala kwambiri ndi pologalamuyi.
Nkhani yamutu wakuti “Apainiya—Penyani Bwino Umo Muyendera” idzatisonyeza mmene tingakhalire anzeru ndi ololera kuti tipeze nthaŵi yochitira utumiki waupainiya. (Aef. 5:15-17) Nkhani yamutu wakuti “Chenjerani ndi Njira Zimene Zimaoneka Ngati Zoyenera” idzatiphunzitsa mmene tingatsimikizire m’mbali iliyonse ya moyo wathu chimene chili choyenera kwa Mulungu. Nkhani yakuti “Mmene Maulosi Okwaniritsidwa Amatikhudzira” idzatithandiza kudzaza m’maganizo ndi m’mitima yathu chikondi cha Mawu a Mulungu. Nkhani yapoyera yakuti “Njira za Mulungu—Sikupindulitsa Kwake!” idzagogomezera mapindu amene akupezeka pakali pano chifukwa chotsatira zinthu zolungama zimene Yehova amafuna.
Kodi mukukhumba kusonyeza poyera mwa ubatizo wa m’madzi kuti mukufuna kuyenda m’njira za Mulungu monga mmodzi wa atumiki ake odzipatulira? Ngati ndi choncho lankhulani ndi woyang’anira wotsogoza kuti apange makonzedwe ofunikira.
Onetsetsani kuti musadzaphonye msonkhano wadera wapanthaŵi yakewu. Dzapezekeni pa mapologalamu onse amasiku aŵiri, popeza “wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.”—Sal. 128:1.