Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
“Kukumbukira Kufulumira kwa Tsiku la Yehova” ndiwo mutu wa msonkhano wadera wa masiku aŵiri umene udzayamba mu September. (2 Pet. 3:12) Wakonzedwa kuti udzutse changu chathu. Okhala padziko lapansi posachedwapa adzaona ziweruzo za Yehova. Kodi ndani adzapulumuka “tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse”? Okhawo amene akhalabe maso mwauzimu ndipo amene moyo wawo uli “m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.”—Chiv. 16:14; 2 Pet. 3:11.
Kuti munthu apulumuke tsiku la Yehova ayenera kubatizidwa. (1 Pet. 3:21) Ofalitsa amene akufuna kubatizidwa pamsonkhanowu ayenera kuuza woyang’anira wotsogoza, amene adzapanga makonzedwe ofunika.
Nkhani yosiyirana ya mbali zinayi, “Mtundu wa Anthu Amene Tiyenera Kukhala,” idzasonyeza bwino lomwe zimene tiyenera kuchita kuti tizikumbukira kwambiri kukhalapo kwa tsiku la Yehova. Nkhani yapoyera, “Chitani Mwanzeru Pamene Tsiku la Yehova Likuyandikira,” idzalongosola tanthauzo la ‘kufuna Yehova, chilungamo, ndi chifatso,’ kuti tikapulumuke.—Zef. 2:3.
Msonkhano waderawu udzatha ndi nkhani ziŵiri zosonkhezera mtima za oyang’anira oyendayenda, zakuti: “Kodi Moyo Wanu Wakhazikika pa Choonadi?” ndi “Kulinganiza za Mtsogolo Pokumbukira Tsiku la Yehova.” Nkhanizi zidzatisonkhezera kupenda moyo wathu ndi kupanga masinthidwe oyenera. Ulosi wa Baibulo ndi zochitika m’dziko zimasonyeza bwino lomwe kuti tsiku la Yehova lili pafupi. Programu imeneyi ya msonkhano wadera idzatilimbikitsa ‘kukhala odzisungira ndi kudikira.’ (1 Pet. 5:8) Pangani makonzedwe otsimikizika okapezekapo masiku onse aŵiri.