Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
“Sungani Malamulo a Mulungu Nimukhale ndi Moyo” ndiwo mutu wa programu ya msonkhano wadera wa masiku aŵiri, woyambira m’September. (Miy. 4:4) Idzagogomezera chifukwa chake kumvera malamulo a Mulungu sikuli kolemetsa. Ndiponso idzasonyeza mmene kuchita chifuniro cha Mulungu kumatsitsimulira ndi kubweretsa chimwemwe chenicheni ngakhalenso chiyembekezo cha mtsogolo.—Mat. 11:28-30; Yoh. 13:17.
Amene akufuna kudzabatizidwa pamsonkhanowo momvera lamulo la Kristu ayenera kulankhula ndi woyang’anira wotsogoza, iyeyo ndiye adzakonza njira zofunikira.—Mat. 28:19-20.
Nkhani yosiyirana idzafotokoza njira zomvekera bwino zimene tingakondere Mulungu ndi abale athunso. (Yoh. 13:34, 35; 1 Yoh. 5:3) Uphungu wogwira mtima wochokera m’Masalmo 19 ndi 119 udzaphatikizidwanso paprogramuyo. Ngakhale kuti uphungu wouziridwawo wa m’masalmo ameneŵa unalembedwa zaka zikwi zapitazo, tidzaona mmene ungapindulitsire aliyense payekha lero.
Nkhani yapoyera yomwe idzakambidwa ndi woyang’anira chigawo idzakhala ndi mutu wakuti “Opa Mulungu, Nusunge Malamulo Ake.” (Mlal. 12:13) Nkhani yotsiriza ya woyang’anira dera idzasonyeza mmene achinyamata angapezere mapindu abwino kwambiri m’moyo ndi mmenenso angakhalire ndi chidaliro chakuti adzakhala ndi tsogolo losatha. Woyang’anira chigawo adzamaliza programuyo mwa kuŵerengera madalitso amene timapeza tikamamvera ‘lamulo lachifumu’ la chikondi. (Yak. 2:8) Nzoonadi, iyi ndi programu yamsonkhano yomwe munthu aliyense sangafune kuphonya!