Msonkhano Wadera Umene Udzatithandize Kuteteza Moyo Wathu Wauzimu
1. Kodi ndi njira imodzi iti imene Yehova akutithandizira kukwaniritsa ntchito yofalitsa uthenga wabwino?
1 Yehova amatiphunzitsa ndiponso amatipatsa mowolowa manja mfundo zotithandiza kuti tikwanitse ntchito yofalitsa uthenga wabwino. (Mat. 24:14; 2 Tim. 4:17) Njira imodzi imene timalandirira zimenezi ndi msonkhano wadera umene umachitika chaka chilichonse. Msonkhano wa chaka cha utumiki cha 2010 udzakhala ndi mutu wakuti “Tetezani Moyo Wanu Wauzimu,” ndipo wachokera pa lemba la Aroma 8:5 ndi Yuda 17-19. Misonkhanoyi idzayamba mlungu woyambira April 12, 2010.
2. (a) Kodi msonkhano wadera udzatithandiza pa zinthu ziti? (b) Kodi misonkhano yadera ya mbuyomu inakuthandizani bwanji inuyo panokha mu utumiki?
2 Mmene Msonkhanowu Udzatithandizire: Msonkhanowu udzatilangiza mmene tingapewere zinthu zododometsa zimene zingatidyere nthawi ndiponso kutilepheretsa kuganizira zinthu zofunika kwambiri. Tidzaphunzira mmene tingagonjetsere mtima wolekerera zoipa ndiponso tidzaphunzira zimene zimafunika kuti munthu akhale wauzimu. Nkhani yosiyirana ya Lamlungu idzasonyeza zimene munthu aliyense payekha ndiponso mabanja angachite kuti alimbitse moyo wawo wauzimu pamene mavuto akuwonjezereka ndiponso pamene akukumana ndi zinthu zambiri zoyesa chikhulupiriro chawo. Msonkhanowu udzatithandiza kuteteza mitima yathu, kupitirizabe kukonda zinthu zauzimu, ndiponso kuti tisaiwale madalitso omwe anthu amene amateteza moyo wawo wauzimu amapeza.
3. Kodi msonkhano wanu wadera uli liti, nanga muyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
3 Mukangodziwa tsiku ndiponso kumene kukachitikire msonkhano wanu wadera umene ukubwerawu, konzani zokapezekapo ndi kukamvetsera zigawo zonse za msonkhanowu pa masiku onse awiri. Kumbukirani kuti Yehova amadalitsa zochita za anthu akhama.—Miy. 21:5.
4. Kodi tikalandira malangizo otani pa msonkhano wathu wadera womwe ukubwerawu?
4 Ndithudi, Yehova ndi amene amatipatsa mphatso yabwino imeneyi. Choncho, kuti tikhalebe atumiki achikhristu, m’pofunika kuti tidzapezeke pa msonkhanowu, womwe wakonzedwa ndi kapolo wokhulupirika. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha zinthu zonse zimene amatipatsa mwachikondi, zotithandiza kuti “tilimbikire osagwedezeka pa kulengeza poyera chiyembekezo chathu.”—Aheb. 10:23-25; Yak. 1:17.